‘Si ine ameneyo’ – zithunzi za m’busa wa CCAP kunyanja ndi ‘ka bae’ zivuta

Advertisement
Billy Gama

Kwatuluka tizithunzi ndipo tikufalitsidwa mu ma Fesibuku ndi mu ma WhatsApp umu.

Mu Zithunzi zimenezi m’bambo wina wachikulire wapanilila ka msungwana mu mphechepeche kunyanja.

Billy Gama
Anthu akuti bamboyu ndi a Billy Gama.

Anthu akuti bamboyu ndi a Billy Gama amene ndi abusa a mpingo wa CCAP komanso anali mlangizi wa a President akale a Bingu wa Mutharika pa nkhani zokhudza mipingo.

A Gama ndi munthu okwatila ndipo ali ndi ana, ena a msinkhu ofananilanapo ndi msungwana ali mu chithunzicho.

Koma pamene a Malawi ambiri agundika kuthotha a Gama kuti ndi a chimasomaso kapena kuti a chidyamakanda, iwo akanitsitsa kwa mtu wa galu kuti munthu ali pa chithunzicho si iwo.

A Gama ati anthu aupandu ndiwo ayambitsa nkhani yabodza choncho ati cholinga akufuna awaonongele mbiri.

“Munthu ali mu chithunzi chimenecho si ine ayi, n’kutheka tafanana pang’ono koma tsimikizani ndithu kuti si ine,” atelo a Gama.

Iwo apempha Mulungu kuti awakhululukile anthu amene akufalitsa nkhani imeneyi.

Koma a Malawi ochuluka akuona ngati mkulu ali mu chithunzi ndi a Gama, ndipo akudzudzula abusa.