Ma suti a Bisnowaty autsa mapiri pa chigwa

David Bisnowaty

Phungu wa dera la pakati mu boma la Lilongwe a David Bisnowaty aputa mavunkhomola.

A Bisnowaty dzulo lolemba anajambulitsa ndi Mafumu a mu dera lawo ati atatchena ma suti amene Phungu’yo wawagulila.

David Bisnowaty
Bisnowaty aputa mavunkhomola

Polemba pa tsamba lawo la Fesibuku, a Bisnowaty analemba mozithilamo amvekele: “sindilonjeza zinthu osakwanilitsa, onani ndinalonjeza Mafumu ma suti. Awa atchena apa awa.”

Koma a Malawi ambiri sanakondwe nawo a Bisnowaty ati kamba koti anali kuzitamandila pa zinthu za mkutu zenizeni zopanda ndi mchere omwe.

A Malawi ochuluka amene anathililapo ndemanga pa nkhaniyi anasonyeza kukhumudwa kwawo ndi khalidwe la Phungu’yi.

Ena anadzudzula a Bisnowaty kuti bola akanamazitamandila pa chitukuko chooneka ndi maso osati kamba koveka nsanza Mafumu basi.

Choseketsa chinali choti Mafumu ena anavekedwa ma suti aakulu.

*Ma suti a Bisnowaty autsa mapiri pa chigwa*

Phungu wa dera la pakati mu boma la Lilongwe a David Bisnowaty aputa mavunkhomola.

A Bisnowaty dzulo lolemba anajambulitsa ndi Mafumu a mu dera lawo ati atatchena ma suti amene Phungu’yo wawagulila.

Polemba pa tsamba lawo la Fesibuku, a Bisnowaty analemba mozithilamo amvekele: “sindilonjeza zinthu osakwanilitsa, onani ndinalonjeza Mafumu ma suti. Awa atchena apa awa.”

Koma a Malawi ambiri sanakondwe nawo a Bisnowaty ati kamba koti anali kuzitamandila pa zinthu za mkutu zenizeni zopanda ndi mchere omwe.

A Malawi ochuluka amene anathililapo ndemanga pa nkhaniyi anasonyeza kukhumudwa kwawo ndi khalidwe la Phungu’yi.

Ena anadzudzula a Bisnowaty kuti bola akanamazitamandila pa chitukuko chooneka ndi maso osati kamba koveka nsanza Mafumu basi.

Choseketsa chinali choti Mafumu ena anavekedwa ma suti aakulu.

Advertisement

31 Comments

  1. bisnowaty ndi khuluku alephera kutipatsa chitukuo mmalo mwake wangowagulia aunjika magogowa

  2. Vuto La Amalawife Kunyoza Too Much.Pamenepo Mafumu Ena Analibe Suit Apa Aipeza.Akunama Akulu Mwachita Bwino Mwathandiza,kp It Up

  3. Vuto La Amalawife Kunyoza Too Much.Pamenepo Mafumu Ena Analibe Suit Apa Aipeza.Akunama Akulu Mwachita Bwino Mwathandiza,kp It Up.

  4. Bisnowaty watichotsa manyazi, ,, mafumu akuwoneka bwino, ,,
    Ana anjoka nsanje, ,, mufanazo

Comments are closed.