Kwanuko akuti chani za Nyerere? Ligi ija yatengedwa basi

Malawi Football

Wakwiya ndi mfiti. Amene sakusangalala pano ndiye mwina ndi neba basi.

Kuli chisangalalo ku banja la nyerere. Ku manoma lero amwa wamkaka, kusamba wa mkaka ndipo chilichonse kwa iwo chili tayale.

Malawi Football
Nyerere

Patatha zaka khumi ndi chimodzi, lero nyerere za manoma zaphulapo ligi ija imene pena imaoneka ngati neba atha kuwaphumitsa.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la za masewelo la Balaka, nyerere zinaonetsetsa kuti zisasunge mkute kuti zizamalize sabata la mawa. Zinali za papsa tonola basi.

Ena amakhulupilila kuti mwina anyamata a Masters Security ndi kuchitapo chamuna lero ndi kuphumitsa nyerere mwayi wawo koma zakanika ndithu.

Zigoli ziwiri za mnyamata Peter Wadabwa, chimodzi chochoka kwa Foster Namwera ndi chimodzi china chochoka kwa njoka Esau Kanyenda ndizo zatseka mpikisano wa ligi lero.

Manoma anapita mu masewelo akufuna ma pointi atatu basi. Ndipo atatuwo awapeza atakhoma Masters Security ku Balaka.

Ngakhale anyamata a Masters Security anakokela umu ndi umu, kuthilamo ka chigoli kamodzi koma ngati ka thumba ka mchere kothilidwa mu nyanja yaikulu ya India sizinaphule kanthu.

Pamene oyimbila amaimba pinto kuti mpira watha ndi pamenepo pamene opambana ligi anadziwika kuti ndi nyerere.

Advertisement

249 Comments

 1. WAKULA NEBA 11 YRS NIPATALI OSATENGA LIG KOMA MWENZE KWAMENE UKO KU MALAWI? 11 YEARS OSATENGA LIG KUNO SITILUMVETSA KOMA BB NIMORE FIRE INE ONE THOMZY CHIPATA ZAMBIA MAULE MULIBWANJI?

 2. Kuno onse zisoti avula. Ulemu kwa manoma. Akutiso kuli zaka seven kusogoloku Manoma Akutenga izi mosatizana. Koma ena akumayankhulaso za Neba.
  Ati zikuoneka kuti wasala pang’ono kufika pa white Eagles. Sure.

  1. Nzopweteka mai makamaka ikakhala team ngati imeneyi kuti isatenge kwa 2 yrs ngati zachitikilamu even kumangalandeko Man U panopa ili pa vuto masapota awo mngokwiya zedi malingana ndi momwe zikuyendera. Chinanso chofunika kwambiri kwa masapota nchoti adzidziwa kuti iyi ndi league and pamakhala ma team 16 or over and onsewo aim yawo nkutenga chinkho so asamadandaule kwambiri ndimasewera awa

 3. Neba wachita bwino kutenga league,Amuna titasiya kuvala ma pantie pano tikuvala ma boxer short kkkkkkk and atsikana atasiya kuvala ma half pitcoat Muhahahahahaha Neba

 4. Inunso ni a Noma eeet?? I thought you were suppilosed to be neutral as a page,,,, how will you post then the victory of the so called Nebaa,,, Shame

 5. Agogo fc awona mwana koma ndiye kwatelera..zamanyazi uchembere adathelatu mpaka 11 years osawonako ngakhale wadiso limodzi..anyway congraturations! nomadzi family being champions elect.

 6. Malawi24 sikuyenera kunyozedwa lero page iyi ndiyanu ndipo admin wa page iyi sanasangalare. Titapatsidwa ma game otsogozana timkadandaula ndi page yomweyi idayambitsa kunyoza inu mkumathandiza kuchokera pachiyambi pa league page iyi sidalembepo nkhani yabwino yaife ndiye ngati ndikunyoza munyoze ife chifukwa next season tikuonani muli limodzi mibwebwe inu admin tikudziwa kuti zakuwawani kuti league yatha chonchi koma paja ndidanena kuti chaka chikakhala chokolora olo utadzala gaga umakolora chimanga

 7. Guyz ngati tilibe comment kungosiya osalembapo kathu social media singakudandauleni kuti simunalembe mpala kutukwana zocheza zomwezi iiiiiiii koma yes yes mwakulira kuti?zampirazi mwaziziwa okulakula kapena?

 8. League ñdiye mwateñgadi after 11 years koma musamalimbane ñdi bullets, size zanu ñdi achina Mzuni, Masters ñdi Dwangwa.Moñgoķumbutsana; super league bullets:13 times Noma 6

 9. Amalawi tidakhala bwanji? Tiyeni tidziyetsa kupanga zathu ndimene zinthu zathu zikuyendera, tikambe ndimene Nyerere zachitila bwino pa league imeneyi osati neba no! Noo! Neba watani sizokwiyitsana

 10. Paja mwana akankhoza kumene kuyimba linkhwelu amayimba mkutulo komwe,ndiye zachitika apazi.kutenga league kwanoma chaka chino kuli ngati kutulo ndiyenela kuwawata kwambiri,koma musayiwale kuti mwankhala mukunthela panumber 6 zaka zambiri bullets ikutenga league koma bullets simakunyozani!!

  1. Koma ndiye, amalotadi alindi anzake akusewera. Ndiye ndizimenezi, kutereku akuwona ngati alowa ufumu wakumwamba anyapala amenewa.

  2. mumanyoza koma kuti fb inali ndi anthu ochepa . komanso inu munatha dzaka 8 osatenga olo charty imene,mpaka munadikira kufika kwa gabadinyo muhango kuti mutenge muyambenso kutenga zikho

 11. Kampopi kumvetsa chisoni,,,musachulutse zokamba apa ingovomerezan kut anzanu awina mukanakhala inu mtown mukananyasa osat sewero nde pot ndaanzanu mwat munyoze,,,,hiyaaa chikho tatengabe no matter how you talk

 12. Nyerere zokha nzomwe zimakwanitsa kutenga ma cup awiri kapena kuposera apo, koma sitidakhalepo osatengako chikho. Choncho, this year’s strategy was to grab super league and not a cup.

 13. Zampira izi ndine wa #Bullets neba watenga basi tonse nga #Blantyre palibe zonyozana ingosangalalani basi osati kunyoza #Mapalestina iyayi Zampira izi zimadana nkulalata

 14. Aaah zaka 11 nde munthu ukataye nthaw ndi kumukwiira neba….muli class imenei inali mbuli mapeto kapena tinene kut mbutuma kkkkk zabwino zonse gogo wanthu noma wayamba kukwawa pamenepa hahahahahahaaaaaa

  1. Munthu wa nkhaza amadziwika ndi malankhulidwe ake kutenga league Kwa Noma mpaka kuisandutsa mbuli, gogo ine ndakululuka ndi malankhulidwe oipawa ndikudziwa ena amangozindikila atayankhula udyo chifukwa cha mkwiyo

 15. Maule Sangakwiye, Noma Mpaka Zaka Ten Olo Kutenga League, Amamvetsa Chisoni Koma Mpira Sumakoma,,,, Maule Maule, Every Year, Tipumeko Nafe.

  1. Kusazindikira kuja nde kumeneku sukudziwa kut ntchito imeneyi ndiyautolankhan n game yi ukundiuza kut isn’t newsworthy???? Come on osamatichititsa manyaz neba

 16. Neba usaiwale kuti std bank cup inathelamo osailawa bola ife league tinatengako kumayambiliro kaya zatha zaka 11 koma macup timatengabe

 17. *Sichipongwe koma chilungamo* *Beforward wanderers Nyerere inatengako league WhatsApp kulibe, , plasma TV kulibe,tablet kulibe, Facebook kulibe kkkkkma 4n tiku user ma ground 4n kuli ma 4n azidina kkkkkkkk Noma sizatheka ⚽ izo ndizomwe akunena anthu akuno

  1. Iii!!! tilaweko abale nanga mudzingotenga nokha?11 yrs sipano tisiyeni tiusumane.Ndkudziwa kut nebayi watisiya dala kuti tilaweko chaka chino chokha chaka cha mawa timpatsa.Asaaa tiyeni tinjoyeretu Nyerere chaka cha mawa chikubwerera ichi neba atilanda.

 18. Kwa 11yrs tikuyembekezera kukwatira popeza tinalonjeza kuti tidzakwatira pokhapokha neba akadzatenga ligi chaka chake ndi chino. Eee congrats

 19. I don’t think alipo wakwiya,Noma inayambila kutali kukonzekela ndiye season ino zaonetsadi kuti anakonzekedi congratulations neba.

 20. KO’d inu munatha zaka 6 osatenga league, manyazi bwaa, lester city inakhala zaka 150yrs, kudzatenga mu 2015_16season

  1. Manyazi bwanji nanu tikukamba Zapano ungandiuze kt panene noma inatha 11yrs simatengako cup ndekt inali focus pama cup games nde chaka chino apa za league zo mkona atenga

 21. 11 Years Osatenga Lig? Anthu Kuno Akuti Ati Ndimaloza.Akutinso Mwina Chaka Cha Mawa Kukhala Njala Chifukwa Izi Zachitikazi Ndi Mwikho.Atinso Bullets Izi Za 11yrs Izi Saziziwa. Yewooo!!!

Comments are closed.