Mzimayi aba khanda la mwezi umodzi

0

Tsimwe ndi msozi lakuta banja lina ku Mbayani mu mzinda wa Blantyre pamene mzimayi wina osadziwika komwe anachokera waba Khanda la mwezi umodzi m’mawa wa lachitatu pa 6 December 2017.

Poyankhula ndi mtolankhani wa Malawi24 lachinayi, mayi ake a mwana obedwayu a Beatrice Kalulu atsimikiza kuti mwana wawo Promise Soya wabedwa ndi mzimayi osadziwika.

M’mawu awo a Beatrice womwe ndi a zaka 19 anati iwo anabeleketsa mwana wawo kumbuyo kwa m’chewali wawo
yemwe ndi wa zaka zisanu mziwiri za kubadwa nthawi ya 9 koloko m’mawa pamene iwo adali kukolopa mnyumba mwawo.

“Ine ndinamubeleketsa mchemwali wanga Lute kuti azizungulira naye kuti ine ndigwire bwino ntchito, kenako iye anapita ku msika wa Mbayani komwe mayi anga amagulitsako malonda awo, sipadatengenso nthawi yayitali Lute anabwera kundiuza kuti amayi ena amulanda mwana kumbuyo,” analongosola Beatrice.

Iwo anawonjezera kuti mayi okubayo anauza Lute kuti sanamubeleke bwino kumbuyo ndipo iwo amati amuthandize kukonza mwanayo kumbuyo, pamene Lute anawona mayi wakubayo akupita nalo khandalo.

Ndi misonzi mmaso mwake Beatrice anati: “Tinathamanga ine ndi anthu ena koma mzimayiyu sitinamupeze mpaka tinakafika ku Chilimba polisi koma osampeza Promise.”

Iwo anati atafika ku polisi ya Chilimba anangowuzidwa kuti apitilize kuyang’ana khanda losowalo pamene nawonso apolisi akusaka ku mbali yawo.

M’modzi mwa okhudzidwa yemwenso ndi landilodi wa Beatrice, mayi Mary Fred, ati zachitikazi mzopatsa mantha komanso zopatsa tsimwe kutengera msinkhu wa mwana wobedwayo ndipo apempha kuti ngati wina angaone khandali adziwitse a polisi.

“Takhala tikumva kuti anthu amaba ana koma kunena zoona nzopatsa chisoni kuba mwana wa khanda loteleri ndipo ndupempha aliyense amene angaone khanda la chilendoli adziwitse a polisi”

“Izi zameretsa   mantha pa azimayi, kuti koma nanga anawa tidziwabisa motani? popeza ana timatha kupatsila anzathu kapena ana athu mcholinga choti tigwire ntchito zina pakhomo,” analongosola mayi Fred.

Beatrice Kalulu amachokera mmudzi mwa a Mbemba mfumu yayikulu Champiti m’boma la Ntcheu.

Share.

Leave a Reply