Kokuba mifuti sitipita ndi utsi wa fodya basi. Poputa asilikali, kumazimitsila nduduzo. Maule atuluka.
Ndi Kamuzu Barracks ndi Moyale amene atsala kulimbanilana ukulu wa chikho cha FISD. Zivute zitani achitenge ndi asilikali basi.

Timu ya Bullets lero yaonetsedwa zoopsa itatibulidwa ndi asilikali a ku Kaning’ina mu chikho cha FISD.
Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la za masewelo la Civo mu Mzinda wa Lilongwe, anayamba kuonetsa chamuna anali anyamata a Moyale amene anamwetsa chigoli patadutsa mphindi makumi awiri.
Anali mnyamata Khuda Muyaba amene anadzetsa chidima ku banja la maule, kuwasiyila chizilezile mmaso.
Maule anaphukilamo mu chigawo chachiwiri pamene mnyamata wawo Chiukepo Msowoya anamwetsa chigoli kuti ayike masewelo pa 1 kwa 1.
Zinaoneka ngati maule atchola ku Barracks lero pamene anapeza penote. Fischer Kondowe anamwetsa ndithu ndi kuika maule patsogolo.
Koma chisangalalo cha maule chinafanana ndi cha munthu ochimwa chifukwa chinangokhala kwa ka nthawi kochepa chabe.
Anyamata a Moyale anabwelanso ndi ukali ndi kuthila mpholopolo kwa Ma palestina kupangitsa kuti masewelo afike ku kaphelachoka, ma penote.
Uku ndiko maule aona mbonaona, atsanzikana ndi chikho cha FISD.
Pamene Moyale inaonetsa ukadaulo ogoletsa ma penote, Nelson Kangunje wa Bullets anachita njengunje ndi kuphonya.
281 thoughts on “Amusasantha, amugweba, amutsinatsina neba lero”
Comments are closed.

Neba anatola joker
inde taonanso kut mumatha kusanza mau kma usayiwale kut nawe neba anakugonyomola kale
tavomereza basi
Neba apa ndiye wamwa madzi wometera ndevu kuisiya mkaka. Koma ndinakuchenjeza za Khuda Muyawa. I we makani thoo. Lero wagwa chagada. Akluumbuza, athibura, akuswa, akukonza, akufotokoza, akunyetsa, akukong’ontha, akuyeretsa mmaso, akuipisira mbiri, akuyalutsa, mpaka kuyenda ndi usiku ulendo wobwelera kwanu ku Ndix. Tafanana tonse. Tatuluka mu FISD Cup ndipo tatulutsidwa nd team imodzi Moyale. Machende ako neba. Mpaka umafuna referee akukondere kukupasa penoti. Game sidali yako imene ija. Ndiye Danger/ achimwene aakulu amvekere ife timafuna matimu ang’onoang’ono ngati amenewa azipha mateam akuluakulu ngati BB kuti national team yathu izikhala ya mphamvu. Hahahahahahahahaha koma nebaaaaaa.
Eeeeshhhh!!!!! Ku bb akuluakulu! Chingerezi amvekere “u expectedly it kuwina” chani chimenechi alinafe zavuta zasolobana ku bb ngakhale refu adali kumbali yanu koma Mulungu anali kwa asirikali ndiye poti inu ndizanu zija apo refuyo mumpondeso inu mwakanika basi
Zachaka chino ndi zimenezo.
Iwe mvera kuno kaye, ndiye mpikisano umenewo amafuna apezeke owina m’modzi basi. Sikuti iwe ngati uli pa number1 ndiye kuti ndi iwe wanzeru ayi fatsa. Mpikisano udakalipo, tayang’ ana kutsogolo kwakoko uwone zikubwera.
Apse mtima zenizeni,akumva nyunyunyu.kkkkk
asilikali ndi aukali,azimitsa ndudu zonse,zangoti ndwiii
Amugweba,amutsinatsina kkkkkkkkk
waiwona sniper, umangomva
kkkkk Ayooooooh
Kuthetsa kunyoza aise mulungu wayankha
Ine Ndinaziwa Team Yotulutsa Noma Imafika Final Ndiye Neba Akumwetsa Mandimu.Vuto Umadalira Home Ground Advantage Koma Apa Neutral Ndiye Akufwafwanthadi.
vuto ndilot munthu wabwino nthawi zonse anthu samuonela kukondwa and any mistake nkhani imafika pa air ndepot bb its the best team in malawi u expectedly it kuwina only forgetng that its football ⚽ even barca or Madrid imaluza koma mateam enawo akaluza anthu sayankhula amangot tidadziwa basi …we r still bullets and we w never change
Ayifwafwanfha, ayikhapira kosatwa, ayiyendesa chidibiyachidibiya, ayimeta mpata opanda madzi bullets ayikuntha!!!!!!!!
ine faint
Msongole Nevi moyale yaliza akatundu pepani kwambili a bulless nose zimachitika
kkk akuva pain
A Beletsi mwakhalila mazila anu omwe