Samala ndi mlomo wako, muno simotukwanila Pulezidenti – sipika auza Chakwera


Lazarus Chakwera

Mtsogoleri otsutsa mu nyumba ya malamulo a Lazarus Chakwera dzulo adzudzulidwa ndi Sipika wa nyumba ya malamulo.

A Chakwera adzudzulidwa kamba konyoza Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika kuti iwo ndi kalonga wa mbava ndinso olephela ndi ogunata.

Richard Msowoya
Msowoya: Wadzudzula a Chakwera.

A Chakwera adanena izi lolemba pamene amayankhula mu nyumba ya malamulo. Iwo adali kuyankhapo pa zimene a Mutharika adanena potsegulila nyumbayi.

Mu kuyankha kwawo, a Chakwera adakwelela Paphiri a Mutharika ndi kuwathila nkhoko.

“A Mutharika dziko likuwavuta, iwo ndi olephela ndinso ogunata,” anatelo a Chakwera.

Iwo adanenanso: “a Mutharika ndi kalonga wa mbava amene akutsogolera uchigawenga mu dziko muno, kulibela dziko la Malawi mwa psipsiti.”

Atanena izi a Chakwera, nduna ya achinyamata ndi masewelo a Henry Mussa anaima ndi kupempha a Sipika kuti adzudzule a Chakwera kamba konyoza Mtsogoleri wa dziko.

Sipika adanena kuti afufuze bwino pa nkhaniyo ndipo azapeleka chigamulo.

 Popeleka chigamulo chake lachisanu, Sipika adanena kuti a Chakwera adalakwitsa ndithu poyankhula udyo za Mtsogoleri wa dziko.

Latest vacancies

354 thoughts on “Samala ndi mlomo wako, muno simotukwanila Pulezidenti – sipika auza Chakwera”

  1. Nyumba Yamalamulo Yaulendo Uno Yagwira Ntchito Bwino Chifukwa Cha Dr Chakwera Ndiena Otsutsa Izi Zimathandiza Olamula Kuchangamuka Pakuchita Zithu.In Malawi We Nid Pple Of Chakwera’s Type.My Vot IS Yours

  2. Kod Inu Mafuna Kut Achakwela Anene Kut Zinthu Zikuyenda Bwino Pamene Zinthu Sizilibwino? Chilungamo Chmawawa Zomwe Anend Achakwela Ndizowona Uyu Pitala Ndimunthu Osayidziwa Ntchito Yake Ndipo Ndimunthu Okanika Zot Dziko Muno Tili Ndi Tsogoleli Zodziwa Yekha Iye Pitala

    1. DPP woyeeeeeeee. there gud @ opposing and gud to be in opposition. govt was made 4 us and opposition was made 4 u

  3. There is a big gap between the state President and the party President, so Chakwera should be careful indeed, who told him that to be in opposition means insulting the? Kumakhala ndi umunthu abale.

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading