Ine ndi kamnyamata kachisodzela – watelo Mutharika

Advertisement
Mutharika

Wakalamba wafuna. Mstogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika amene akhale ndi zaka 81 pofika 2019 ati iwo ndi kamnyamata kachisodzela ndipo azapikisana nawo pa chisankho mu 2019.

A Mutharika anena izi mu mzinda wa Mzuzu pamene anayima kuti apelike moni kwa anthu ena mu mzindawo.

Iwo anati mu chisankho cha 2019, apikisana nawo ngakhale kuti azakhale adakali agogo.

Mutharika
Mutharika: Wakalamba wafuna

“Anthu masikwano akukonda kukamba nkhani ya achinyamata. Ndiye upeza anthu a zaka 50, kapena 60, ngakhalae 70 imene kuzitchula kuti ndi achinyamata. Inensotu ndi wachinyamata, ndipo 2019 ndilipo ndithu, kuzathamanga nawo kuti mwina ndipambane chisankho,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika anati chifukwa mayiko a ku Ulaya anawasankha kuti ndiwo otsogolera achinyamata mu Africa muno, iwo ndiye kuti ndi wachinyamata basi.

Zokamba za a Mutharika zachititsa jenkha a Malawi ena amene amayesa kuti a Mutharika atha kusiyila mpando kwa wachiwiri wawo a Saulos Chilima amene ali achichepele.

Zinamvekanso kuti a Mutharika akuganiza zosankha bambo George Chaponda kuti azatenge udindo wawo iwo akapuma koma a Chaponda atakhudzidwa ndi nkhani ya kuba chimanga, zinakhala ngati zasolobana.

Anthu ena ankanenanso kuti a Mutharika akuganiza zosankha a Ben Phiri kuti apitilize udindo wawo mu 2019 umu.