Kwavuta kumsewu, mitengo ya zilango yakwezedwa

168

Pofuna kuchepetsa komanso kuthana ndi ngozi za pamsewu mdziko muno, boma podzera ku bungwe loyang’anira za pansewu la Department of Road Traffic and Safety Services lakweza zilango kwa anthu olakwira malamumo a panseu.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe nyuzipepala ino yapeza chomwe chatulutsidwa ndi akuluakulu aku bungweli posachedwapa.

Aliyense opezeka akuthamangitsa kwambiri galimoto azilipitsidwa K50, 000.

Bungwe loyang’anira za pamsewuli lati zindapusazi ziyamba kugwira ntchito kuyambila lolemba sabata ya mawa, lomwe ndi pa 13 Novembala.

Bungweli layika K30, 000 kuchoka pa K10, 000 ngati chindapusa chatsopano kwa aliyese oyendetsa galimoto yopanda chiphaso choiyeneleza kuyenda pamsewu (Certificate Of Fitness).

Kupatula apo, shoveli aliyese oyendetsa galimoto koma alibe layisesi azigamulidwa kupereka chindapusa cha K100, 000 kuchokera pa K10, 000.

Pa zindapusa zatsopanozi, Road Traffic yati aliyense opezeka akuthamangitsa kwambiri galimoto azilipitsidwa K50, 000 kuchoka pa K5, 000 komaso opezeka akuyendetsa galimoto yosalembetsedwa mu kaundula wawo azipelekaso chindapusa cha K50, 000 kuchoka pa K5, 000.

Bungweli silinasiyile pomwepa koma kuthanaso ndi ma shoveli onse omwe amapanga chisankho choopseza kapena kudelera apolisi a pa msewu ndipo lati onse opezeka olakwa pa mlanduwu azilipitsidwa chindapusa cha K200, 000.

Izi zadza kaamba kakuchuluka kwa ngozi za pamsewu mdziko muno zomwe zapangitsa kuti miyoyo yambiri itayike.

Share.

168 Comments

 1. Tisadanepo APA nthawi yakwanayakwana IFA imabwera mosiyanasiyana tisithe boma olo timange miseu ngozi sizingathe. Ine Christopher Rodgers muchihiwa.

 2. Tisadanepo APA nthawi yakwanayakwana IFA imabwera mosiyanasiyana tisithe boma olo timange miseu ngozi sizingathe. Ine Christopher Rodgers muchihiwa.

 3. Kod amenewa amakhara akugwila ntchito kapena amakhare akupanga chibisabisa? Zoona munthu angamugwile pa4n kkkkkk Malawi sadzatheka bas.

 4. Drivers are the main reason for accidents,seconded by poor roads,then poor cars,lastly the root cause is corruption.corruption in construction,giving licences,giving COF.I bet you guys 60 % here commenting went through recommended vehicle driving process.60%here are petient enough to wait for doted line before overtaking.Drivers these days lost all the most important part of defensive driving,respect and petience

 5. Pofuna kuthana ndi ngozi,kapena pofuna kupitiliza kuwabera a malawi,kukolola posalima,kulipili anthu kumalipira koma cha nzeru osawoneka,no mankhwala in hosptals,poor roads,everything poor std..stupid

 6. Waminibusi ngati mwapsa wonjenzerani mitengo minibusi ndiyanu ndani angakulamuleni abvutike alibe galimoto basi aPeter akuyenda pagalimoto anthu onse aku Thyolo Ali ndi magalimoto sakeera minibusi

 7. Apa ndiye mwanena zowona a Rose Roice ndagwilinzana nazo ndipo apoliai alemera chifukwa ndidani angapeleke ndalama zambiri ngati zimenezo bola kungawana ndiwa traffic pamseu ndipo muona kuyambira lero a motor exams siya kukhala mu office Ku panga driving licence azikakhala pamseu ndikumene kuli ndalama

 8. Waminbus Ali Pa Mavuto,Ma Driver Tonse Tilankhulepo, Mpaka Tichitepo Kanthu .Dziko Ndi Lathu Mpaka Azitibwezera Nmbuyo Chonchi, Choipa Chitsata Mwini,2019 Ndikuona Lili mawa,.,

 9. Waminbus Ali Pa Mavuto,Ma Driver Tonse Tilankhulepo, Mpaka Tichitepo Kanthu .Dziko Ndi Lathu Mpaka Azitibwezera Nmbuyo Chonchi, Choipa Chitsata Mwini,2019 Ndikuona Lili mawa,.,

 10. Izi zingothandiza kuti apolisi alemere kwambiri coz apano ziphupu ndinjira yokhayo ingaombole mavutowa, ngati amalandira yochepa paziphupu apa ndeyakwera basi, a traffic chaka chanu ndichino takatani

 11. madriver ambiri akuseweretsa moyo wanthu ndinthu,zinandiwa ndikuchoka mzimba kupita ku mzuzu driver wina wake amayendetsa minibus speed 180 per minit, mpaka ndinamuuza driver kuti inetu sikuti dukapeleka magazi kumzuzu cental hospital,pliz chepetsani speed, anandiyakha 3pin yomwe ndalipira ndiyochepa ndiyomwe amalipira wokwera ngolo! kkkkk

 12. This is abnormal but do u consult wen u wnt to do things or u tink athu zitsiru these ar mare drivers who get k30 grand monthly salary were on earth wil they get those fines umbava mukuputawutu mmangopabga zithu mwaumbuli bwanji

 13. Ndalama zopangila campaign zimenezo???? Komatu mukanawakonda Amalawi……Muziganizira muli inu ….how many DPP cars move without papers ….only mpango wa blue ……

 14. Amalawi apa zafika zinthu sopano zafika powawa koma ndikuziwa kuti bushiri ndiyemwe akusokoneza zikoli chifukwa ndi satanic koma tisamale kwenikweni apolice ndi armay samalani mutha nose ndi ena amuboma

 15. Uku Sikuchepetsa Ngozi, Koma Kupititsa Patsogolo M’chitidwe Wa Katangale Ndi Ziphuphu.
  Patha Zaka Zingati Chiyambireni Kabungwe Kanuka?
  And Ndingozi Zingati Zomwe Mwapangitsa Kamba Ka Maganizo Anu Omwe M’mangopanga Ngati Mwina Mwake Mulibe Mitu?
  M’malo Moti Muthane Ndi Anthu Omwe Aphwanya Malamulo, Maso Anu Amakhala Ali Tong’o Pandalama.
  Ndiye Anthu Angasiye Bwanji Kuphwanya Malamulo Anu Opusawo?
  M’matithandiza Inde Koma Penanso M’matipweteketsa Ndinu Nomwe.
  Ngati Mukufuna Kutolera Ndalama, Pezani Njira Yina.

 16. BOMA LIMENELI NDILAKUBA OSAVOTELASO AYI AKUTI WONA NGATI SIFE ANTHU NANGA ANTHU ANAFA KU STADIUM ANJA MUPANGA NAWO BWANJI PLZ MALAWI AKULILA KWAMBILI MUSATERO PALIBE ANGAPANGILE DALA NGOZI ALOAD TLAFFiC MUWANENAWO AGWESA MAGALIMOTO ANGATI PONGOFUNIKA MUSAMALE NDIMALAMULO ANUO

 17. Asiyeni akudzichotsa okha pa mpando ndi mfundo zawo zopusazo kufuna kubela amalawi anzanu basi inu nkumalemela , tionana nkati mwandime tidzakuuzeni maganizo athu, ukakhala pamwamba pa Njovu usamati kulibe mame.

 18. Zimenezo sizingachepetse ngozi koma kuti katangale ndi ziphuphu zichuluke njira yabwino yochepetsera ngozi zapamseu ndikukonza miseu yabwino,yolimba komanso yapamwamba ndikukhulupilira kuti a Malawi adakonda akanamakhala ndi atsogoleli okonda dziko lawo

 19. Afuna angowaipisila mbili ambwiye awa, ambwiye akazagwa pa mpando asazadabwe akhoza kuzagwa ndi nkhani zokhuzana ndikasinthidwe ka nkhanza ka pa nseu

 20. Asiyeni akudzichotsa okha pa mpando ndi mfundo zopusa ngati zimenezo, alangizi akowo samakukonda tionana nkati mwandime tidzalankhula maganizo athu .

 21. AAA mabuluku amenewa Ali pa foto apa aaaaaa kuli kudya ndalama he,hede !!!!!!!! Choncho muziti afuns kwabwino sthandize apolisi powapatsa magalimoto. Yea.

 22. The police are always checking the capacity of passengers rather than checking if the car is worthy on the road. Breaks, indicators, reflectors, then licences instead they are busy collecting 2pin on their pockets. We need to make a strike pliz and stop blaming leaders but the public workers are so corrupt

 23. amene amaswa malamulo ndindani mesa ndinu nomwe nanga inu kukadzaza mangalimoto muzilipila zingati mesa mati ngalimoto ya police simadzaza mmmm kuba poyela zakuvutani aphungu kambilanani zokomera amalawi osat munthu mmodzi ayi

 24. Komano zomwe zapangidwazi za mitengo yolipila mwamntundu uwu, ai tisaapangise a police a panseu kukhala olakwa ai anthuwa timagwila nao bwino ntchito koma zomwe wapanga iwezi ndinenatu iwe utangozuka kwanuko uli ooh basi lelo ndikakonze malamulo apanseu cholinga chako ukuti umvese kuwawa wa minibus basi zonsezo mukufuna wa minibus ndiye muusaade a traffic atraffic amagwila bwino ntchito yao koma iwe wapanga iwezi mukufuna upwetekese wa chikulile, aaaaa mukanasintha asazakudandaule zitavuta anthu tikuonaaa eeeeeee

 25. nanunso muphunzire kuyankhula chilungamo mukanangoti zimene timabaz zikuchepa osat takweza ncholinga chofuna kuchepesa ngoz kodi ndi anga ma driver kapena ma pasanger amene anakonzekela kupta ku nseu kt akufuna kukacita ngoz? mmesa ngozizonso mukumazyambisa ndinu amene ndi usatanic wanuw agalu anthu inu? zandinyasatu zimenez muuzane mbuz za anthu inu

 26. Kunena Zoona Ndalayi Yachepa Kwambiri.Kumuza Driver Achepetse Speed Amalalata.Apa Sanatiganizire Ife Okwera.Chilango Chikanayambira One Million.Miyoyo Ikutayika Chifukwa Cha Ziganizo Zopusa Za madriver.Ma Overtake Achibwana.Kaya Opakira Ma 4 4 Ndiye Awasiya Pati? Amagalimoto Asamatilalatire Poti Ndife Osauka.Tisamangofa Ngati Myama.Apolisi Nawo Asiye Chinyengo.Pa Zalewa Roadblock,lirangwe Mwaonjeza Kucheza Ndi Madriver Uku Akukufumbatitsani.Ma Minibus A Mwanza Komanso Ntcheu Balaka.

 27. RTSS apapa yakanda malo osanyelenyetsa. Kulambalala dala pamene pakuyabwa kumakakanda pambali. Aaaaaaa hmmmmm. Monga zomwe zimapangitsa ngozi ndi kuchepa kwa zilango?? Panopo muyembekezere ngozi zambiri komanso kulemera kwa apolisi ndi kusauka kwa boma. Komanso ndifunse nawo, ndalama zimenezo anthu adzizitenga kuti? Ndiye timange ndende zambiritu chifukwa amphawi adzaza Ku ndende chifukwa sadzikwanitsa kulipira. Pomaliza parliament yathu iwunike zimenezi coz parliament ndiyo mathero a chiyembekezo cha amphawi.

 28. Akufuna ndalama zakapani basi ,ndani sakuziwa kumbuyo kunalibe ngosi ndiye mwaziw liti sikuti inu ndi ophinzira ndiye inu president phunziro langozi simunaphunzileko mwaziwa lero

 29. Pano akufuna aturuse ndarama 5000 yogwirana tikafuna chenji tizikasitha Ku BANK zausiru Malawi sazathekanso basi

 30. am not dpp cadet, koma chokhachi ndikuvomelezana nanu. tisafe ngati nkhuku. ziko ndilaling’ono ndikale, timathamangila kuti? magalimoto anu amapanga ndalama koma mkulephela kuapatsa service.

 31. Kunena zoona uku sikuchepets ngozi koma kuwonjedzela katangale pakati pa a police apamseu,kupela zilango zonkhwima sikungachepetse ngozi,koma kunena zoona anthu ambiri kuno Ku Malawi saphunzila galimoto mwandondomeko ambiri amangokagula ma licence komweko kukuchokela zilangoko,palibe chachilendo pa Malawi chakula ndikutidelera anthufe akuwona ngati chilichose akhoza kupanga mmene akufunila koma adziwe izi tonse ndife ana amlungu ndipo patalike pafupike Mlungu azalanga moyenela zonsenzo palibe chimene chingachepetse ngozi,kuchepetsa ngozi tikuphunzitsa anthu mwadongotsolo kuchepetsa ziphupu ndiposo mwaluso osati zilango.

 32. Misewu yake yonyansayi Ndiye mumati ngozi zitha chifukwa anthu aziwopa kulipira. Zopanda nzeru. Malawi is importing monthly thousands of fleet of cars, very sad the same old poor roads. Ndiye mukati ngozi tikupangitsa ndife ma driver osati inu aboma amene mumangothamangira mma boarder kutolera duty and mis using it. MAGANIZO akumidima basi. Yatsani Magetsi kuwale

 33. Apatu akanati azipeleka ndalama yokwana 2million kwacha,akalephera azimangidwa ndipo akatulusidwa asazayendesenso galimoto,chifukwa pali ena amamwa mowa akuziwa kuti atenga anthu.Moyo wamunthu ndiosowa,sibwino kumawaseweresera anthu miyoyo.

  • Kuchita njiru ndi omwe ali ndimagalimoto???,magalimoto ake ati??.Chomwe mufuna muzisuta chamba,kumwa mowa,kunyamula anthu ngati matumba achimanga,kufuna kupha anthu mwadala??.Vuto tilinawo pamalawi ndi Umbuli,chifukwa munthu sungamwe mowa ukuziwa kuti utenga anthu,akakugwira uziti msanje chifukwa uli ndigalimoto,GALIMOTO YAKE ITI YOMAYELEKEZA NDI MOYO WAMUNTHU??.Ndikupusa kapena ubulutu kumayankhula zoti kupanga kaduka chifukwa ena ali ndimagalimoto.Boma lisasekelere zopusa agwire anthu basi ndipo zilangodi zisachepe.MAN MULI NDIGALIMOTO?? Fuso lopusa.Ooh chifukwa muli ndigalimoto ndiye mutha osamasamala zamoyo wamunthu??.

 34. PANKHANI IMENEYI ACHITA BWINO KWAMBILI KOMA WOYAMBA KULIPIRA AKHALE PRESIDENT CHIFUKWAAGALIMOTO AMATHAMANGA KWAMBILI ACHIWILI AKHALE ASILIKALI ANAZANZANAKWAMBILI MUTATA ALIPILE10BILLION

 35. Just make it compulsory kuti every driver should go for defensive driving course osati zotikawazi mukufuna tikhale akabaza mdziko muno

 36. Ndiye tiziyenda ndi ma thousand panseu? Tiwatenga kuti ngati salary yathu sifika ndi 50 000 yomwe sitili ngatitu iwowo omaweruka ndi cash daily

 37. Kodi driver angayipephe ngozi ndi chifukwa cha akukweza chilango . Chifukwa ngozi siyithawika komaso anthu sibbwezi akufa

 38. ,mmmmmm, mhuu angoona kupanga zimenezo masiku asalawa ndiochepa, zimenezi zipangisa anthu ambiiiiiiiliiiii kutaya chikhulupililo ndi boma lao boma timalikonda kwambili monga mtsogoleli wa dziko lino timamukonda komano malamulo enawa aziziwa kuti akufinya amalawi omwe ndiposachedwa dzitsankho zikubwela anthu angathe kuweluza m’ene angaweluzile malinga ndi malamulonsi, chitsanzo pakatipa pamamveka za nkhani ya anamapopa malo mongopeleka chitetezo m’ene amachitila komano anthu zikafika poowakana naonso amaona mochitila mwao, ukangoona achitetezo afika mkuzaola muzio tiyeni muzikafotokoza konko, komano pankhaza zomwe aona angazakhalenso mchidwi mkuvotera? sindikukhulupila, apa akubwelesa zimalamulo zikhwima kufuna kungopweteka anthu oyenda panseu kodi zimenezi mzimwe timayembekezela povota paja? abale inu mukonza za malamulo apanseu musampangise mtsogoleli kukhala oipa kapena azitukanidwa chifukwa cha inu ai. kodi azilangizi a mtsogoleli mukulangizapo chani mtsogoleli za malamulo apanseu? zoona munthu akalipile 120, 000 kapena 50, 000 ma 5000 alakwachani mukufuna amaminibus apange chani, masiku asala ochepa fewesani zinazi mntundu wa amalawi umve kukoma koma mukafinya anthufe aaaaa kaya kuti zizatha bwino ai chonde chepesani ndrama zolipila panseu tikalakwisa musatiphe mkuphatu uuku chonde musapangise mtsogoleli wathu kuti zisazamuyendele chifukwa cha anthu ena andale zadala cholinga mtsogileli agwe pampando ai risatero

 39. ngozi zizatha pokhamakha aboma agumule talayu koma ngati satelo ngozi sizitha or ndipango aesikomu maonjeza ndalama mukulandila koma magesi sakusiya kuzima, nde mukamadusa museumu mukumapangaso matama mugalimoto yanu mukumakwela itati ipange ngozi nose ndiku mwalila ndekuti magesi sangamazimeso

 40. ose amene apangamalamulo amenewa ndi mbuzi zamano mmusi ,katangalesangathe chifukwachokweza mitengo, koma ngatimumadzitenga azeru lelomudziwe ndinu mbuzi,agalu

 41. a traffic museumu akuonjeza kodi boma simunga lowelerepo kuti ma galimoto azidusa bwino koma pena ake atraffic mwaonjeza kodi mukumasowa ya tee mmmmmmmmmmm khalidwelimeli likuonjez mukumagwila magalimoto kutI mateyala ndiokutha koma titati tionesese mwinaso teyala ndi jombo yokutha kwambili ndi jombo

 42. Boma la DPP limangozonza anthu osalakwa.Magetsi kulibe nabiziness kulibe ndikumakweza mitengo ya pansewu. Wbat the real problem?kunja kuno kuli mulungu akuona kumeneku ndikutipha tili moyo. Even it goes to parliament singapange pass..End result olemela ndi apolice andi a Road Traffic. Izi zikungolimbikitsa katangale basi. Palibe angalipile zimenezi. Ngati mukuganiza bwino chonde ndikupempha muchotse…..

 43. Ngozi zimenezi si kuphwanya malamulo a pa nsewu kokha ayi. Pali wina yemwe wabweretsa mzimu woyipa mdziko muno. Anthu tinayamba kalekale kuphwanya malamulowo. Koma ngozi sizinafike mulingo wa chaka chino. Ngakhale mutalanga mwa mtundu wanji, palibe chomwe chingasinthe.
  Komanso misewu yathu yambiri sili bwino….

 44. Zangozazana mbuli ZOKHA ZOKHA m’ bomamu ndi road traffic komwe kulizimbava ZOKHA ZOKHA nde muone mene ma officer aku road traffic mene akugulira magalimoto kd amalandila ndalama zingat ? Ndi ma cleaner omwe kugulanawo ma department okuba awa

 45. Kumeneko ndie kupititsa patsogolo chinyengo, amene achitebwino ndi atrafic police osati mboma. Atsogoleri anthu samaganiza bwino or mukweze chilango sizitathauza kanthu cifukwa palibe drive yemwo angakwanitse kulipila ku mboma mapeto ake ndi chinyengo ndi a traffic basi

 46. Osati kuchetsa ngozi ,koma kuti boma lasauka. Ngakhale mutamatchaja 1 million ,ngozi zizichitikabe zikuonetsa kuti cheni cheni chimachititsa ngozi sakuchidziwa ,ndikamaphunzira defensive driving ,pali zifukwa 5, zomwe zimachititsa ngozi, mwa chimodzi mseu, pamene imkachitika ngozi ya asilikali IJA ine ndinali pafupi, vuto ndi mseu .

 47. Ndye Kukwela Kwa Ma #Found wo Kusitha Zithu?Kodi Ngoz Zimachita Kukodzedwa?Apa Ndye Akwanilitsidwad Mau Aja Za Kayesala Zipite Kwa Kayesala Ndithu.!!!!

%d bloggers like this: