Awagamula zaka zisanu ndi chimodzi za kalavula gaga chifukwa chokodzela mzawo


Area 25 Women Jailed

Lawaluma lamulo ndipo lawasiyila chilema chachikulu chokuti ngakhale a chipatala sangathe kukonza. Ndipo inu nonse okonda kuchitila nkhanza ena, bisalani patali chifukwa mawa mutha kukhala inu.

Amayi atatu a ku Lilongwe amene anagwila mmayi mzawo ndi kumusunga momukakamiza ndi cholinga chofuna kumuchita nkhanza, agamulidwa kuti akasewenze ku jele kwa zaka zisanu ndi chimodzi.

Area 25 Women Jailed

Amayiwa amene amachokela ku dera la Area 25 ku Lilongwe, ati anagwila mmayi mzawoyi chifukwa amafalitsa nkhani yoti mmodzi mwa atatuwa ali ndi kachilombo ka HIV.

Iwo ati pokwiya anamutenga ndi kumutsekela m’nyumba ndi kumuchita nkhanza kuphatikizapo kumumenya, kumukodzela ndi kumuvula. Pochita izi iwo adali akujambula.

Atafika pa bwalo, mkulu oweruza wawagamula kuti apite ku ndende akasewenze kwa zaka zisanu ndi chimodzi.

Amayi atatuwa ndi a Thokozani Msiska a mmudzi mwa Enukweni, Mfumu yaikulu Mtwalo mu boma la Mzimba. Palinso a Zelifa Phiri ochokela mmudzi mwa Setha, Mfumu yaikulu Zulu ku Mchinji. Omaliza ndi a Rodness Chose ochokela mmudzi mwa Gonthi, Mfumu yaikulu Kamenyagwaza mu boma la Dedza.

Latest vacancies

130 thoughts on “Awagamula zaka zisanu ndi chimodzi za kalavula gaga chifukwa chokodzela mzawo”

  1. Tizingowaloza,poti umfiti kulibe Ku police,nanga tikawamenya atimanga,NDE azimayi tipeze mankwala owapotoza mapazi bola osajambula powalozapo

  2. Zaka zachuluka guys, Nkhani yake yochepayi… Mukulephera kumanga nduma zaboma zikungoba ndalama zamisonkho ya aphawi…. Agalu inu mukapsa moto kumwamba nonse ama Court…

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading