Abambo atatu apha mzawo ndi zikwanje

53

Apolisi m’boma la Machinga akwidzinga ndi kutsekera abambo atatu chifukwa chowaganizila kuti adachotsa moyo wa bambo wina wa zaka 60 pomukhapa ndi zikwanje.

M’malingana ndi oyankhulira apolisi m’bomali Davie Sulumba, a polisi amangadi John Daudi a zaka 30, Henry Dawa, 19, komanso a Sinoya Petro a zaka 32 powaganizira kuti ndiwo adachita za upandu okuphawu.

knife-bloodA Sulumba anati ophedwayu, Jaison Thom, yemwe amagulitsa makala adakumana ndi tsokali mu m’bandakucha wa pa 23 Okotobala pamene adachoka kunyumba kwake ndi thumba limodzi ulendo wa ku Liwonde kuti akalitakate kwa kasitomala wake wa nthawi zonse.

Koma podutsa m’mudzi mwa a Chilonga, mwadzidzidzi kudavumbuluka abambo atatu omwe amagona panja pa nyumba ndipo anayamba kumenya ndi kutema ndi zikwanje a Jaison Thom modetsa nkhawa ndi mopanda chisoni powaganizila kuti adali okuba.

A Thom adatengeredwera ku chipatala cha boma cha Machinga komwe madotolo adatsimikiza kuti iwo adamwalira kamba kotaya magazi ambiri chifukwa cha mabala akulu omwe adali mthupi mwawo.

Potsatila kafukufuku, a polisi mderali akwanitsa kumanga atatuwa pa 24 mwezi omwewu ndipo abambowa akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu kukayankha mlandu wa kupha omwe umasemphama ndi gawo 209 la malamulo oweluzira milandu

Potsatila izi a Sulumba apitiliza kudzudzula anthu m’bomali kuti apewe kutengera malamulo m’manja mwawo popeza kumakhala kuzikalasulira makala a moto, koma kutengera oganizilidwawo kwa a chitetezo cha m’mudzi kapenanso ku police kumene.

A Jaison Thom adali ochokera m’mudzi mwa a Chipamba mfumu yaikuli Sitola m’boma la Machinga, pamene a Daudi, a Dawa ndi a Petro onse ndi mmudzi mwa Issa mfumu yaikulu Sitola m’boma lomweli.

 

 

Share.
  • Opinion