Manoma Kusangalala

National

Palibepo pachiwiri paja Bankala, ndipo nyerere zabwenza chipongwe kwa Moyale

By Mwayi Mkandawire

October 22, 2017

Atchola banki lalikulu lero asilikali a ku Zomba pamene anzawo a ku Kaning’ina abetsa mifuti kwa nyerere zomwe zawatimba pakwawo pomwe.

Amene anati ligi ndi kumadzulo analinga ataona ndithu, ma Bankala atakhala pachiwiri kwa nthawi ndithu, achotsedwapo lero ndi maule.

Manoma Kusangalala

Pa masewelo amene anachitika lero, asilikali a ku Zomba a Red Lions aonetsa mbonaona timu ya Siliva ataithibula ndi zigoli ziwiri kwa duuu!

Mnyamata Chimwemwe Chidati ndiye anathila onga otchola zitseko za ku banki lalikulu mu chigawo chachiwiri.

Pamene asilikali a ku Zomba anagwilitsa mwa luso mfuti zawo kuti adzetse chimwemwe kwa owatsatila, anzawo ku Mzuzu anali kuodzela mpaka abeledwa mifuti ndi nyerere.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la Mzuzu, anyamata a noma anaonetsetsa kuti abwenze chipongwe chimene asilikali a ku Kaning’ina anaonetsa powatulutsa mu chikho cha FISD.

Zigoli za anyamata atatu amene dzulo anakanika kuona golo ku Karonga ndizo zayandamitsa timu ya Moyale.

Precious Sambani, Essau Kanyenda ndi Khumbo Ng’ambi ndiwo anakhoma asilikali a ku Kaning’ina pakwawo pomwe. Mnyamata Chamveka Gwetsani anangoponyamo ka chipukuta misonzi basi.

Pa masewelo ena, timu ya Bullets yachapa timu ya Blue Eagles ndi zigoli zitatu kwa duuu ku Blantyre kuti iyo ikatenge malo a wachiwili mu ligi podomola Siliva.

Zotsatila zonse za masewelo lero zinali motele:

 

Moyale barracks 1-3 Beforward Wanderers Mafco 2-1 Mzuni Masters security 2-0 Dwangwa United Red Lions 2-0 Silver Strikers Big Bullets 3-0 Blue Eagles