Valani zilimbe, Magetsi kuti azasiye kuthima ati ndi mu 2030

Advertisement
Peter Mutharika

Ena sadzawaona ndi komwe chifukwa azakhala atatsogola kale.

Ati nkhani ya kuvuta kwa Magetsi tidakali nayo mpaka a Peter Mutharika kutula pansi udindo.

Malinga ndi a bungwe lopanga za Magetsi la EGENCO, mavuto a Magetsi ku Malawi kuno sikuti apita pompano.

Peter Mutharika
Kuvuta kwa Magetsi kudakalipo.

A bungweli amauza anthu a nyumba zolemba nkhani ndi a ma bungwe pa sabata latha.

“Monga mukuona, Shire waphwa uyu. Sitikupezamo madzi okwana kutekesa makina athu opangila Magetsi,” mdindo wa ku EGENCO Bambo Shadreck Namalomba anauza choncho anthuwo.

Iwo anati padakali pano angokhazikitsa ti njira kuti mwina dziko lino lizipata Magetsi moyepula koma kuti vuto la Magetsi lizathe ndiye si pano.

“Tiyika ma jeneleta muzigawo zonse zitatu ngati njira yodikila Mvula ndi kufuna kuchepetsa vuto la Magetsi,” anatelo a Namalomba.

Iwo anaonjezelapo kuti ma jeneleta amene ayikwidewo ayamba kugwila ntchito chaka chamawa.

Advertisement

2 Comments

  1. Very poor report writing, this reporter is writing as if it’s not his mother language.Poor, poor!!!!!!

  2. Why can’t we stop road projects and fertilizer subsidy for two years and invest the money in energy sector? Solar electricity can not take two years to start operating. The use of diesel generators will result in air pollution and loss of forex. Chonde zifunsani zinthu zinazi.

Comments are closed.