Tisiyileni opopa magazi tiwatambile ife – watelo Ngolongoliwa

0

Mfumu yaikulu ya alomwe a Paramount Ngolongoliwa wati Mafumu ndiwo akatswiri pa nkhani za ufiti ndipo athana ndi anamapopa.

A Ngolongoliwa amauza izi Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika pamene anayendela anthu okhudzidwa ndi nkhani yopopa magazi mu dera la Mulanje.

Senior Chief Ngolongoliwa

Senior Chief Ngolongoliwa:  Tithana nazo ndifeyo Mafumu.

A Ngolongoliwa ananena kuti iwo ndi mafumu anzawo a chilomwe ali ndi kuthekela kothana ndi anamapopa amene avutitsa anthu okhala mu madera awo.

“Ife tikupempha kuti ana athu muzigona,” anatelo a Ngolongoliwa. “Ngati zinthu izi zili za masalamusi othana nazo ndifeyo Mafumu anu.”

Iwo anatsindika kuti ngati mmudzi muli afiti, mfiti yaikulu ndi mfumu ya mmudziwo. Ati iyo imayendela mudzi onse isanakagone mu ufiti.

“Ngati za anamapopa zili za mmatsenga simungazithetu, ozitha ake ndife Mafumu anu, akulu akulu pa kutamba,” anatelo Ngolongoliwa.

A Ngolongoliwa ananenaponso kuti Mafumu ndi okhawo angadziwe ngati mmudzi muli anamapopa chifukwa iwo ndi amene ali ndi maso oona mu matsenga.

Ku madera a Mulanje, Thyolo, Phalombe ndi Nsanje akuti kukumabwela zinthu zopopa magazi. Anthu 6 aphedwa pokayikilidwa kuti ndi iwo akupopa magazi.

 

Share.