Akukana a Malawi kudyela suwiti mpepala: ochepa okha akutchena


condoms

Sikuti ndi yodula kwambiri jumboyo, imathekanso kupezeka yaulere koma a Malawi ochulukilapo ndithu akumayizemba.

Malinga ndi kafukufuku, zadziwika kuti a Malawi sakugwilitsa ntchito kwambiri chitetezo pokasamba. Angolowa ndi mutu basi. Itchoke itchoke.

condoms
A Malawi sakutchena

Pa mwambo omwe unachitikila ku Bingu International Conference Centre ofuna kupeza njira zatsopano zoyenela kigwilitsidwa ntchito kuti a Malawi ochuluka azigwilitsa ntchito kondomu, zinaululika kuti pa chaka munthu mmodzi ku Malawi kuno amagwilitsa makondomu anayi basi.

Malinga ndi kafukufukuyo, mu chaka cha 2016, anthu 260,000 anatenga matenda opatsilana pogonana zomwe zikusonyeza kuti anthu ochuluka samatchena ayi.

Poyankhula pa mwambowu, a Atupele Muluzi amene ndi nduna ya zaumoyo anati Malawi akufunika dongosolo la kagwilitsidwe ntchito ka kondomu kuti nkhondo yolimbana ndi HIV ndi Edzi komanso mimba zosakonzekeleka ikhale ya phindu.

Latest vacancies

171 thoughts on “Akukana a Malawi kudyela suwiti mpepala: ochepa okha akutchena”

  1. Iwe kukupasa sweet kuti udyele mpepala ungayimve kukoma .nanga tichulukana bwanji ngati sitikudyana lata lata .bible lidati tichuluke ngati mchenga

  2. kkkk man aids inatha kuli matenda ambiri BP etc mankhwala 3times aday while arv’s 1tablet aday which is which zisalani muzazindkila pasogolo ife ttakwapula kale tabwinot.

  3. Kukhutisidwa pa chigololo ndi puleni mboniyanga ndi Robert Mugabe analesa anthu ake kugwilisa ntchito kondom chifukwa imayambisanso matenda

  4. Best way ndi kuziletsa chigololo sichabwino. Tiyeni tikhale okhulupilika ku azikazi komaso azimuna athu. Ine olo zitavuta maka condom sindizavala ndipo imandibhowa koospa. Amzungu asatipepelese ife.

  5. A Malawi anzanga tiyeni tigwiritse ntchito ma paketiwa. Zikumveka kuti amalobodola nkhongono koma ndibwino kusewezetsa kusiyana ndi kutenga HIV or STI.

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading