Tiloleni titsilike nkhalango kuti odula azikanika kuziona – ng’anga zapempha


Viphya Forest

… Asilamu atsutsana nazo

Ng’anga mu dziko muno zati zikufuna chilolezo cha boma kuti zithe kutsilika nkhalango za mu dziko muno kuti anthu odula mitengo akhaule.

Malinga ndi malipoti a olembankhani, madolo a zitsambawa anena kuti iwo ndi ofuna kuthandiza boma kuteteza nkhalango.

Dinala Chabulika
Sheikh Chabulika: akana zotsilika nkhalango.

Iwo ati atha kuyikamo mankhwala a zitsamba mu nkhalangomo ndipo anthu onse ofuna kulikha mitengo azingopeza nkhalango zasowa basi akafuna kuziononga.

Koma a bungwe la chipembedzo cha chisilamu mu dziko muno ati maganizo a ng’anga awa ndi achabe ndipo aboma asawamvele ndi komwe.

Malinga ndi oyankhulila bungweli a Sheikh Dinala Chabulika, Asilamu sakugwilizana ndi ganizo la akadaulo a zitsambawa.

Iwo anati chofunika ndi choti aboma alimbikitse anthu kutsata malamulo okhudza katetezedwe ka nkhalango kusiyana ndi kulola ng’anga kuti zigwilitse zitsamba.

“Sindiye kuti tikuti zitsamba akukambazo ndi zoipa iyayi, koma mphamvu yake ndi yosadziwika,” anatelo a Chabulika.

 

165 thoughts on “Tiloleni titsilike nkhalango kuti odula azikanika kuziona – ng’anga zapempha

  1. Mukukhala ndi moyo wathanzi pafamily yanu ndisaoneso munthu akulimbana ndikumalankhula zankhalango zaboma apa sizikupatsani ndrama zimenezo moyo wamasiku ano ndikachtu basi ngati tilibe ndrama kuvutika kokhakokha basi siyani zimenezo sizikuthanfizani.

  2. Ndi zasin’angazo kapena zosirika nkhalango mukuti zaboma sizikuthandizani boma silimakupatsani chisamaliro mufamily yanu tayesani mungokhala mnyumba mwanu ngati bomalo lingakubweretsereni zakudya masewera eti pangani zosamalira pakhomo panupo kuti bomaloso lizipsa mtima likakuonani

  3. Palibe mfundo ndazinvapo apa tamangolimbikirani kugwira ntchito ndi mabusiness anu muzipeza mariziki komaso kusamalira mafamiry anu ndi kumapemphera. Muzaona zinthu zikukuyenderani bwino osalimbana ndi

  4. Koma kuwauza anthu kuti azikapha albino ngati akufuna kulemela anthu opanda chifundo inu lero mukufuna kuononga ziko pofuna kupha ntundu wa a Malawi mukufuna kusilika nkhalango ngati ndinu ndati? Muziti chani posilikapo poti munthu umasilika chinthu chako osati chamwini nkhalango ndiza a Malawi tonse osati zainu nokha ayi siyani usilu umenewo

  5. Kodi galu wasing’anga wankulu wayambisa zimenezo ndindani ngati mwakhuta kapena misala yakuyambani mungopita kuchipatala cha misala. Kodi nkhalangozo ndizainu apumbwanu kodi ngati ndinudi akatakwe amankhwala mumaziwadi zitsamba bwanji anthu akumavutika ndimatenda osiyana siyana inu osasilika bwanji kuti anthu asamadwale mmizi mwanumo agalu inu siyani manyi amenewo ndithu zisilu za asing’anga inu mbuzi za mano kumozi

  6. auzeni akadaylowo kuti akatsilike Ku adimack kuti mbava zikafuna kuba chimanga matumba azisowa komaso Ku boma mbava zobandalama zikafuna kuba ndrama za boma zizisowa iyi NDE yololedwa osati nkhalango mukapita kotsilika nkhalango tionetsana musamuka muno anyanga nose

  7. Aaah zopepera ndithu…mesa amene amayambitsa kudura nkharangozo ndi a forestry .. Tikuziziwa bwinobwino zinyengo zomwe amapanga poti

  8. If it was a Christian praying for that more people would have agreed but since it’s sing’anga they are calling it mad etc Africans hate themselves.

  9. Uwu ndu umboni woti ndalama ya vuta pamalawi makasitomala akusowa mpaka kupempha boma kuti liroleze kutsilika nkhalango mwalekeranji kupempha chilolezo chotsilika malubino kuti wowapha asamawawone mwina boma likadalora

  10. Malawi wa lero musilika nkhalango kut athu asamadule mitengo kapena kut athu asamakanyeremo kapena kukapangiramo chigololo kkkkkl Malawi sazathekaso

  11. Osakatsirika ana anu aakadzi aka kuti asamatenge mimba asadakwatiwe bwa.mxieuuuh!!!

    Mukasirika nde ma game ranger adzikalondera chani?

    Musiriketu ndi afisi komanso mikango yomwe kuti tisamaiwonenso mwina zikhale nazonso muuzimu zidzikanika kutipha.

    …..kodi **Mr Udzafa imfa yowawa** alikuti alakatureko apa!!?

  12. Ndiyanu…. inu paja mulibe Mavuto eti.. simuziwa mmalo enawa amagwesa moti adzalemo chimanga…kusayenda ,komaso

  13. Tsilikani basi kuti mbava za mitengo zisadurenso, koma mutdilike mwa ulele. Mukakwanitsa mukasilikenso nyanja kuti onse ofuna kulanda nyanja apezeke atafa( Tanzania govnt okuba nyanja)

  14. Ngati amadziwadi kutsilika apatseni mwayi akatsilike kumene kwayambira Cashgate.pulezident ndi ndima zake ndi amene akuononga dzikoli ndi Cashgate

  15. Fodya ameneyo. Chimenecho nchiyambi chotipanga ife kuti tidziwapembeza.This is not an era when one can still be to pulling as back to those devilish ancestral beliefs. God the creator is all we should be looking up to, not some witch doctors.

  16. Anthu openga inu mwapanga bwanji.Between the people who simply cut and the so called ng’anga who is a dangerous threat to forest.People simply cut after some time in some trees suckers may grow again to become new trees.But what do Ng’anga do when obtainig their herbs.they dig and remove roots.pamenepo pangakhaleso mtengo wina ngat??.Sono funso langa nkumati ngat tawavomereza kut asilike nkhalangozi Abale Munakalembesa Za Unzika!!!!!!!??kkkkkkkkkk

  17. Witch doctors thy r fool ngat uli ufiti muyaluka osakayamba ntchto bwanji mukufuna bomaso lichose kandalama ka misonkho azakulipireni inu afiti ngati mukufuna job mupite ku AGRIM mukaone magobo usilu eti

  18. Ka technology kathukathu ka chi Malawi. Koma ndie pin code yoloweramo yo asasunge sing’anga mmodzitu. Chifukwa atangofa mwadzidzidzi ndie kuti ingalakwe

  19. Ndi mbalameso zimenezo eti mukatsilike nkhalango yachita kukhala kuti ndi ya azigogo anu….bwanji akumakudulilani zitsamba zopepetulila anthu ma midzi mwanumo chamba eti…..osakatsilika ndalama za boma zikumangobedwa chisawawazi bwanji ma rubbish

  20. Aloleni atsirike nkhalango, atitsirikirenso our tax money, chimanga, nyanja yathuyi komanso miyala ya mtengo wapatali. Kuti akanganya osololawa akasolola azimera michira ngati anyani. Kkkkk!

  21. muyike ma vimpire ndi zi predator imported from America,china ndi Nigeria za satanic palibe ngakhale ndi mmodzi adziyiwandikila mkhalango kkkkkkkkkk wina athawa dziko lake lomwe

  22. anthu akuyamwidwa magazi kumweraku bwanji osakathandiza apolice kumbwandira anamayamwawa

  23. Ndiye mmimba mungoyesera kutentha after kudya zimango,kkkkkkk osaonantchire kumangowona ma xool blocks koma yaaa….

  24. Aloleni anthu akuononga nkhalango kwambiri mupita kwachinyama mukaone mmene anthu amalala awonongela nkhalango kutola nkhuni zomwe zagwa zokha ndinjila ina mupitenso kwa Jordan kulilangwe mukaone mmene nkhalango yathera mupitenso ku chibvumbe the same lilangwe boma likulephera kuteteza nkhalango

  25. Shuppitt ng’anga mukanika kutsilika mabwalo a mpira flames amazaifafanthira pakhomo…nkhalangi nzambuyanu hiyaaa osangolimbikitsa yodzala mitengo bwanji kwina ndinu mutha mizu apa ndi mitengo

  26. Ang’anga inu mutsilike mu chi Greek koma mukangoesa kutsilika mu chichewa Dzalanyama ameneyu tionjezela moto kuchitanae!

  27. Akuleka kumasilika anyamata anthu ampira kuti asamaluze bwanji?,zamatama basi kapena mukufuna musilike,cholinga muzigwilisira nokha ntchito mitengoyo powopa anthu kuimaliza kuti mungasowe kutenga mankhwala?.Ife zamatama ayi.

  28. Magesi kuduka daily u think nsima ndi ndiwo anthu aphika bwanji? leave them cut down trees it’s not for government it’s God,s trees everyone got rights to cut nkhalango

  29. Aloreni atsilike pamenepo nde tizidula mopanda mantha nanga kutsilika kwathu kuno ngati zimagwira Ntchito kkkkkkkkk asing’angawo angofuna kuoeza mwai wokadula mitsitsi nkhalangozi ponamizira kuti akutsirika

  30. This must be done at village level, its good idea. But my question is will tourists be able to see the forests? because these herbalists can make a National Park not to be visible.kkkk But otherwise its good innovation, lets allow them to experiment with one forest then we will come with feasibility study.

  31. Kumeneko, nanga mmachedwa kuti thayimu yonseyi..wawooh problem solve tsayano..heeyi tawuza asilikali aja atulukemo kaye tikufuna mulowemo ma club eena anzeru zatsopano. athamangethamamgemo koma mujudule zonse osati mbali imodzi yokha yawodulawo ayi komaso ngakha wofuna kuwonongeramoso aziwona ng’ong’ola, good. very gudu..!

  32. tinene kuti m’makomo mwawo akamapita kogona samalowetsa katundu wawo mnyumb mkutsekera kuwopa mbava? Bodzatu ili asin’ganga.

  33. Kungofuna kudzinchukitsa kuti mumatha mankhwala . Bodza basi. Ndikuti munayamba mwapangapo zotelozo?

Comments are closed.

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading