Chiwerewere ndi tulo ndizo zidzetsa chimwemwe – atelo akadaulo


couple, sex, students, college

A kadaulo a zofufuzafufuza a ku sukulu ya Oxford mu dziko la Mangalande ati tsopano apeza zinthu zodzetsa chimwemwe pa moyo wa munthu. Ndipo ati si makobili ayi.

Malinga ndi tsamba la nyuzipepala ya Telegraph ku Mangalande, ati chuma chimadzetsa ka chimwemwe kochepa chabe pa moyo wa munthu.

M’malo mwake iwo ati chimwemwe chimabwela kuchoka mu kugona tulo tokwanila, komanso chiwerewere.

Akadaulowa ati anafufuza pa ma banja ena ndipo anaona kuti anthu akayamba kupata chuma, chisangalalo chawo sikuti chimakhala cha nkhaninkhani.

Ndipo iwo anapezanso kuti anthu ogona tulo lokwanila ndiwo adali a chimwemwe kudzanso anthu amene amagonana molongosoka.

Kafukufuku uyu wapezanso kuti kukhala ndi abale ndi anansi a chikondi ndi aumoyo wathanzi, nazo zimadzetsa chimwemwe.

Latest vacancies

98 thoughts on “Chiwerewere ndi tulo ndizo zidzetsa chimwemwe – atelo akadaulo”

  1. Azungu asazipope kuti iwo ndi akatswiri aziwakufufuza. University degree busy kufufuza izizi? Ifetu izi tidaziziwa kalekale. Try to make research things that at the end will assist the society.

  2. so what malawi as country ll benefit through this nonsenc story? don’t spoil the reputation of journalists with ur unproffesional reporters. if u dnt hav news ideas u better writ nothng. or tel us we shud share with u

  3. The original English story of this article says sex and that doesn’t necessarily mean chiwelewele in Chichewa. I am sure there is a better word you could have used

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading