Chiwerewere ndi tulo ndizo zidzetsa chimwemwe – atelo akadaulo

Advertisement
couple, sex, students, college

A kadaulo a zofufuzafufuza a ku sukulu ya Oxford mu dziko la Mangalande ati tsopano apeza zinthu zodzetsa chimwemwe pa moyo wa munthu. Ndipo ati si makobili ayi.

Malinga ndi tsamba la nyuzipepala ya Telegraph ku Mangalande, ati chuma chimadzetsa ka chimwemwe kochepa chabe pa moyo wa munthu.

M’malo mwake iwo ati chimwemwe chimabwela kuchoka mu kugona tulo tokwanila, komanso chiwerewere.

Akadaulowa ati anafufuza pa ma banja ena ndipo anaona kuti anthu akayamba kupata chuma, chisangalalo chawo sikuti chimakhala cha nkhaninkhani.

Ndipo iwo anapezanso kuti anthu ogona tulo lokwanila ndiwo adali a chimwemwe kudzanso anthu amene amagonana molongosoka.

Kafukufuku uyu wapezanso kuti kukhala ndi abale ndi anansi a chikondi ndi aumoyo wathanzi, nazo zimadzetsa chimwemwe.

Advertisement

100 Comments

 1. Try to write stories that are touching and helpful in somebody’s life not such that are stink/bad will just create more problems in the society, it is only a peaceful mind that brings joy in man’s life not sex or sleeping

 2. Mukanati kugonana pakati pa Bambo ndi mai monga banja mnyumba kumadzetsa chimwemwe.Kugonanaku si chiwelewele.Mulungu ndiye anakupeleka kugonanatu.Ndipo nkwabwino.Satana naye anabwela ndi zakezo zomangogonana chisawawa zotchedwa chiwelewele.

 3. Apart from the wrong word chiwelewele I don’t see anything wrong with this post. The fact is that nobody is obliged to believe in it

 4. This is stupid news,idon’t like it.Please endeavour to sending us veracity news.Xool yawo ndi manyaka kkkkkk….!!

 5. Azungu asazipope kuti iwo ndi akatswiri aziwakufufuza. University degree busy kufufuza izizi? Ifetu izi tidaziziwa kalekale. Try to make research things that at the end will assist the society.

 6. so what malawi as country ll benefit through this nonsenc story? don’t spoil the reputation of journalists with ur unproffesional reporters. if u dnt hav news ideas u better writ nothng. or tel us we shud share with u

 7. The original English story of this article says sex and that doesn’t necessarily mean chiwelewele in Chichewa. I am sure there is a better word you could have used

 8. Afufuza ku Malawi? People in Malawi to be happy they need stable peaceful country, good leadership, jobs, good salary, osati chiwerewere. Chiwerewere won’t put food on the table, only it will create fightings, killings, orphans, diseases and high number of divorce.

 9. Chiwerewere??????

  Can’t you find a better word kodi nanunso?????

 10. Do you really know what you mean by chiwerewere? Please, don’t mislead people here. Chiwerewere means kugonana chipwirikiti cha akazi kapena amuna mosaganizira za umoyo wako kapena wa anthu ogonana nawowo. In English it simply means adultery or promiscuous behaviour. Is what the so called experts have found? Kapena mumafuna kunena kuti kugonanatu?

 11. Without money chiwerewere sichikoma komanso opanda dollar tulo sitibwera zikuoneka akafufuku amenewo mitu yao sikugwira ntchito

 12. Kodi olembanu mumaphunzira chani kusukulu kwanu? Kapena simuphunzira mokwanira kapena aphunzitsi anu ndi mbola. Zoona mukukanika kutanthauzira nkhani mpaka kugwirisa ntchito mau olakwika? Tanthauzo la “chiwerewere” mukulidziwa?

  1. Musakhale ngat mumatha kutanthauzira chingende inuyo. Mot sukudziwa kut the word “sex” is translated as “chiwerewere” while the word “adultery” is translated as “chigololo”? Iwe ukufuna uoneke wotsata uli wosatsata buanj?

  2. Jason Makavelian Kayera ndichifukwa chake mumalemba zosokonekera. It is mere dullness to translate word by word from one language to another. You better go back to the classroom. Umangoloweza eti? Content mater is substantial and overrides.

  3. Kkkkk! mumayankhula chichewa tsiku ndi tsiku koma simukuchidziwanso.Akati sex tanthauzo lake ndi kugonana,pamene chiwerewere ndi kugonana kosavomerezeka ndipo kumachitika pakati pa anthu omwe sali pabanja,pamene chigololo ndi kugonana kosavomerezeka komwe kumachitika ndi anthu kapena munthu amene ali pabanja ndipo amazembera mwamuna kapena mkazi wake kukachita chigololo panja

 13. Mkazi ndi mwamuna amene ali legally married akamagonana sichikhala chiwerewere. It’s irrational kugwiritsa ntchito liwu loti chiwerewere in this article. Coz the moment munthu wangowonapo mawu oti chiwerewere nkhani yo yakwiyitsa kale okonda zopemphera yet the article is just as clean as a health education.

 14. When a white man creates a phone and you video chat with your brother you call it technology but when your Grandmother in the village uses a mirror to see you while you are hundreds of kilometres away you call it witchcraft. It’s about tym we value our own Africa products.

Comments are closed.