A Malawi akondwera ndi kubwera kwa Awilo Longomba

Advertisement

A Malawi okonda zisangalalo ndi okondwa ndi nkhani yokhudza kubwera kwa katswiri woimba chamba cha Rhumba Awilo Longomba.

Katswiriyu amene amachokera mu dziko la Democratic Republic of Congo (DRC), akuyembekezereka kuzakhala nawo pa phwando la msangalutso la Sand Music Festival lomwe litazachitikire Ku Livingstonia Beach m’boma la Salima, mwezi wa mawa.

Lucius Banda
Banda: Ayamikilidwa poitana awilo.

Impact Events, kampani yomwe imakonza phwandoli, yatsimikiza izi.

Ndipo a Malawi athilira ndemanga zoonesa kugwirizana ndi ganizo lobweretsa Awilo.

Anthu aonetsa chimwemwe chawo kudzera pa malo amchezo a pa makina a intaneti.

Ndipo ena anenetsa kuti kuzagwe mvula, kuzabwere mphepo, palibe chozawalepheretsa kukaona Awilo akuimba.

Ena awuzaso Malawi24 kuti oyimba otchuka mu dziko lino, bambo Lucius Banda amene ali mkulu wa Impact Events, agwira ntchito yotamandika poitana Chiphona cha mayimbidwechi.

Sand Music Festival yomwe imachitika kwa masiku atatu, idzayamba lachisanu pa 27 October ndipo idzatha lamulungu pa 29 October.

Monga mwachizolowezi oyimba otchuka amaiko ena amaitanidwa chaka chilichonse.

Chaka chino zakomera amene amakonza zochitikazi kuitana bambo Longomba. Iyeyu azakhala m’modzi mwa oyimba akunja amene adzasangalatse anthu pa zochitikazi.

Zina mwa nyimbo zotchuka za Awilo ndizotchedwa Karolina ndi Rihana yomwe anaimba ndi Yemi Alade wa mdziko la Nigeria. Nyimbozi akuyembekezereka kukaziimba ku Sand Music Festival.

Oyimba wina wa kunja amene waitanidwa ndi Thulasizwe kuchokera mu dziko la South Africa.

Thulasizwe ndi oziwika ndi Nyimbo yotchedwa Meria yomwe yatekesa dziko lino.

Advertisement