A Chakwera alinenela boma la DPP kwa azungu

Advertisement
Lazarus Chakwera and Peter Mutharika

Mtsogoleri wa zipani zotsutsa mu nyumba ya malamulo amenenso ndi otsogolera chipani cha Kongeresi wanenela a Mutharika ndi chipani chawo cha DPP kwa azungu.

Mu chikalata chimene a Chakwera alembela a kazembe a mayiko a kunja, iwo ati anthu a DPP akhala akuchita za mtopola ndi zoopseza kwa munthu amene akufuna kuyimila Kongeresi pa chisankho cha chibweleza.

Lazarus Chakwera
Chakwera: Anthu a boma la DPP akuchita za mtopola.

A Chakwera ati anthu a DPP akhala akuopseza ndi kunyengelela Bambo Lawrence Sitolo amene ndi kandideti wawo pa chosankhochi ku dera la Nsanje Lalanje.

“Ena akhala akunena kuti amugula, ena amulonjeza ukazembe ndipo ena amuuza kuti a Mutharika amupatsa malipiro a phungu ndi ka ndalama koonjezela kapamwamba,” alemba choncho a Chakwera.

Iwo ati anthuwo akufuna a Sitolo asaimilenso uphungu ku deralo ndipo ati akatelo apindula kwa nkhani nkhani.

A Chakwera alembela azungu a ku Mangalande, ku Jeremani, ku Amereka ndi a ku bungwe la UN.

Advertisement