Dziko la a Wandale ku Mulanje ndi Thyolo lagwila mseu: ati asankha nduna tsopano

Advertisement
Vincent Wandale

Posachedwapa pofuna kukaona phiri ku Mulanje kapena kujambulitsila mu tiyi ku Thyolo, a Malawi tizifunika kupita ndi chiphaso choyendela (passport).

A Vincent Wandale amene adalengeza kuti maboma a Thyolo ndi Mulanje ndi dziko loima palokha, alengezanso kuti tsopano asankha nduna zawo mu dzikolo.

Vincent Wandale
Wandale

A Wandale amene akutcha dziko lawo kuti ndi MUST analengeza pa tsamba lawo la Facebook kuti sabata ino kuli kulumbilitsa nduna ku dziko la MUST.

Iwo anaonjezelapo kuti akhalanso akutumiza makalata a ubale ku maiko ena kuwadziwitsa za dziko lawo la MUST.

A Wandale amene ali mtsogoleri wa dzikoli sananenepo amene akhale pa gulu la nduna zawo.

Anthu owatsatila a Wandale ananena monyogodola kuti a Wandale awakumbukile pamene akusankha nduna zawo.

A Wandale akhala akunena kuti iwo akudziwa kuti maboma a Thyolo ndi Mulanje tsopano ndi dziko loima palokha.

 

Advertisement