Nyerere zakwelanso pamwamba

Advertisement
Be Foward Wanderers

Mapeto a sabata awa anali okoma kwambiri kwa nyerere.
Atagonjetsa timu ya Moyale pachiwelu, dzulo anaswanso khofi kwa ana asukulu a Mzuni pakwawo pomwe.

Be Foward Wanderers
Kamwendo ndi ophunzira ake

Pa masewero amene anachitika pa Mzuzu stadium a mpikisano wa ligi, nyerere zinangokodolelamo chigoli chimodzi basi kuti athane ndi anyamata a Mzuni.

Anali mnyamata Jafali Chande amene anamwetsa chigoli kuti athetse nkhani mu chigawo choyamba.

Ngakhale nyerere zinakanika kumwetsanso chigoli china mu chigawo chachiwiri, anatengabe ma pointi onse basi chifukwa a Mzuni anakanika kubwenza.

Izi zikusonyeza kuti nyerere tsopano zili ndi ma pointi 32, awiri kuposa anyamata a Siliva (ma Banka) amene aphane nawo kumapeto kwa sabata mu masewero awo omaliza a chigawo choyamba cha ligi.

Advertisement

2 Comments

  1. Point of correction, Nyerere zili ndi 34 points pamene bankers ali ndi 32 points

Comments are closed.