Aopa kusalandira malipiro, sitilaka yathetsedwa ku makhothi

Advertisement
Malawi High Court Strike

Othandizira ogwira ntchito ku mabwalo ozengera milandu m’dziko muno athetsa kunyanyala ntchito komwe amapanga kuyambira mwezi watha.

Izi zikudza patangotha tsiku limodzi pomwe boma la Malawi linaopseza kuti silipeleka malipiro a mwezi uno kwa onse omwe apitilize kunyanyala ntchito.

Malawi High Court Strike
Sitilaka yatha kumabwalo ozengela milandu.

Othandizilawa amanyanyala ntchito pofuna kukakamiza boma kuti liyambe kuwalipilira nyumba zomwe iwo amakhala chinthu chomwe boma latemetsa nkhwangwa pamwala kuti silingapange.

Chikalatachi chomwe chalembedwa ndi mtsogoleri wa bungwe laogwira ntchito ku mabwalo ozengera milandu a Charles Lizigeni, chati anthuwa abwelera Ku ntchito lachinayi likudzali.

Chikalatachi chati kuthetsa kunyanyalaku ndikutsatira malangizo omwe alandira komaso aunikila kuti anthu ena akuphwanyilidwa ufulu wopeza chilungamo.

“Tikufuna tiudziwitse mtundu wonse wa a Malawi kuti tathetsa kunyanyala ntchito komwe ife othandizira ogwira ntchito kumakhothi timapanga ndipo tonse tiyambilaso kugwira ntchito lachinayi pa 24 Ogasiti,” yatero mbali Ina yakalatayo.

Ngakhale izi zili choncho, ogwira ntchito ku ma khothiwa akanitsitsa mwantu wagalu zomwe boma linanena posachedwapa kuti kunyanyala ntchito kwawo kunali kosatsata malamulo.

Iwo ati kunyanyalaku kunali kotsata malamulo ndipo zomwe linanena boma zoti kunali kusatsata malamulo ndi bodza lamkunkhuniza.

Lolemba lathali, boma linatulutsa chikalata choopseza ogwira ntchitowa kuti ngati sabwelera kuntchito nsanga, onse salandira malipiro ndiposo linaopseza kuti lipanga chinthu chomwe silinanene.

Advertisement

3 Comments

  1. Inu ogwira ku makhothi mumati sitalaka mupita nayo pati??? Dziko la Malawi limakondera anthu a ma degree. Ndikaonetsetsa ambiri a inu ndi a form two kapena ena amwayi form four. Pakadali pano anyamata omaliza form four alipo miyanda miyanda kotero kunali kosavuta boma kukuchotsani ntchito nkulemba malova omwe angoti mbweeee mntawonimu.

  2. Mwagwa nayo gemu. How can you demand for benefits that do not fit your positions? Surely you couldnt have your salary this month. You shown that you are foolish. Mumangomva kuti sitalakala eti. This is second time weeping for bigger benefits without being given. Matako ambuyanu.

Comments are closed.