Kongeresi igwedeza Balaka

Advertisement
Mcp supporters

Kunali kanthu ku Balaka pamene chipani chotsutsa cha Kongeresi chinachititsa msonkhano pa sukulu ya Balaka Primary.

Msonkhanowu umene unasonkhanitsa akuluakulu a chipanichi kuphatikizapo a Sidik Mia unakodola khamu loti a Kongeresi sanalionepo ku chigawo cha Kum’mwera chitulukileni m’boma.

Lazarus Chakwera flops in Blantyre
Chakwera (C) DPP ikuchita katangale.

Polankhula pa msonkhanowu, mtsogoleri wa chipanichi a Lazarus Chakwera anati katangale amene a kuchitidwa ndi a chipani cholamula cha DPP akuononga dziko.

A Chakwera anaonjezelapo kuti Anthu a mu chipani awalandile a Mia.

Mu mawu awo a Sidik Mia anati Kongeresi ndi chipani chokhacho chimene chili ndi masomphenya ndipo 2019 alowa m’boma.

Advertisement

3 Comments

  1. Chipani cha MCP chinapita ndi mwini wake Kamuzu basi

  2. Tiyeni naye ameneyo watsala pang’ono. Wina agwa ndi kadya karista

Comments are closed.