Muthokoze kuti mabwana anu alibe nazo ntchito ndipo boma la Malawi sililabadila zotelezi koma enanu bwenzi mutaimitsidwa pa ntchito kamba kosavala thayo.
Ogwila ntchito ena a mmboma mu dziko la Uganda aimitsidwa pa ntchito kwa miyezi iwiri ati kamba sanavale molongosoka popita ku ntchito.

Malinga ndi tsamba losindikiza nkhani la CGTN lati abambo asanu ndi m’modzi (6) a mu dziko la Uganda auzidwe kuti asaonetse chipumi chawo ku ntchito kwa miyezi iwiri.
Abambowo akuti adapezeka kuti anapita ku ofesi pakhosi palibe chingwe.
Abambowo amene akuti amagwila ntchito mmboma mu dzikolo anauzidwa kuti sanavale molongosoka ndipo pa chifukwa chimenecho akuyenela kaye kukapuma kuti aphunzile mavalidwe abwino.
Ku Uganda anakhazikitsa lamulo lokhudza kavalidwe kwa anthu ogwila ntchito mmboma.
Malinga ndi malamulo awo ati abambo akuyenela kuvala thayo nthawizonse akugwira ntchito.
Mu malamulowo ati amayi saloledwa kuvala chachifupi choonetsa maondo.
90 thoughts on “Awaimitsa pa ntchito kwa miyezi iwiri kamba kosavala thayo”
Comments are closed.


kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk
Kundiimitsa pantchito kamba koti sindinakulunge chingwe mkhosi chotiphunzitsa atsamuda?
Nde mwat thayo???
Malamula aku Britain
Hahahaha… kusunga mwambo. Pali ntchito zina zomwe zimakhudzana kukopa anthu, bizinesi, u loya, zimafunikadi uvala bwino. Chomwe chimadziwitsa kuti munthu ndi wa khalidwe labwino, wa mwambo, okhulupirika, komaso wa ukhondo, ndicho kuvala thayo (chingwe pakhosi). Munthu suyenera ukhala opanda thayo ku ofesi. Ndikusalemekeza ntchito, Ofesi, komaso organization yomwe munthu ukugwira ntchito. Ntchito za mu field monga, uchikumbe, ulangizi, ukazitape (CID) umayenera ukhala munthu wamba. Tchito ya ku mortuary, yobaya anthu ma jakisoni, ku prison, mu restaurant, mu bala, zili ndi mavalidwe akeso. Mini, see through, body pants, ndi zovala ku ma party, kuphwando, ku club, ku ma entertainment center ndi tourism industry. Cholinga ndikuitanila ma kasitomala.
Nanga okhwefula ali gulu liti la ntchito??? zimachititsa manyazi professional kumakhwefula ku ntchito
Kkkkkkkkkk. .. Ndipo simukunama. Zokhwefula ndi za anthu obvina ndiso oyitanira ma minibasi, asowa chochita womwe amakhala ndi makolo awo, oyenda yenda popanda cholinga pamsewu.
Malawi24,iyi ndya fake sure
Ukacite kubvala taye ndiwe wamboni za Jehovah’s ???? Zacamba sopano xayambikaxi
nanga ovala ma socks obooka aja,awaiwala?
Ino ndimaona ngati zapa nyasaland.
mmmm mpaka apo bwerani kuno muxaone mmene anthu amavalira akamapita ku ntchito
Inu muli kuti kodi chemwali
Kkkkkkkkkk zmachitka paize kmenek
Ku Education wa ODL
pa ntchito pamakhala malamulo
Kkkkkkkkk indedi kumavala thayo ndipo ngati sazivala azipumitsidwa olonso kuchotsedwa kumene ntchito hahahahaha koma
MALAMULOWO NDIABWINO MUNTHU SANGAKHALE MUOFESI OSAVALA TAE
Is how disgrace Bosses treat their workers
Eeeee
THAYO, chichewa iz wide,tamva tidzivala man
Keep it up guys pitilizani kuti sankhalatsa …..thayo? Kkkkkkk koma ndeeee eee tu eee
Nkhaniyi yongopeka ,a Mw24 anasowa nkhani yowauza anthu, nanga imeneyi ndinkhani yoti alembe? Last month anazalemba kuti ma trouser onyenya mmaondo avuta pa Malawi. Hahahahahaha. Ngati kulibe zolembe kapumuleni akuluakulu.