Nduna ilanda minibus chifukwa chotenga ma 4-4

Advertisement
Chiumia Obama Grace

Samalani oyendetsa minibus chifukwa ngakhale nduna tsopano zalowelela pa nkhani yolanga anthu onse ochita chibwana ndi malamulo a pamseu.

Chiumia Obama Grace
Nduna Obama

Nduna yoona za m’dziko a Grace Obama Chiumia anadabwitsa anthu mu mzinda wa Mzuzu pamene analanda makiyi a minibus chifukwa inanyamula anthu moonjeza.

A Chiumia ati anakwera nawo minibus imeneyo imene inali pa ulendo wolowela ku Karonga. Iyo inaika anthu anayi – anayi pa mpando m’malo mwa anthu atatu – atatu.

Minibus itaima mu Mzuzu kuti imwetse mafuta, a Chiumia anatsika ndi kupita kukatenga makiyi kumudziwitsa oyendetsa kuti ulendo wathela pompo kamba waswa malamulo a pamseu.

Iwo kenako anayitana Apolisi kuti azawanyamule oyendetsawo kukawatsekela.

Patachitika ngozi zoopsa mu miyezi yapitayi, Apolisi akhwimitsa chitetezo cha pamseu ndipo ambiri opezeka akuswa malamulo akulangidwa mopanda chisoni