Musaope, Magetsi savuta ngati chaka chatha – Escom

Advertisement

Pofuna kuzizilitsa anthu mitima pa nkhani yakuzimazima kwa magetsi komwe kwayambilanso, bungwe la magetsi m’dziko muno lati anthu asadandaule kwambiri poti vutoli silifika pampondachimera ngati chilumika chatha.

Izi zakambidwa Lolemba pamkumano wa atolankhani ndi akuluakulu a bungwe lopanga magetsi la Electricity Generation Company (Egenco) ndiso Electricity Supply Corporation of Malawi (Escom) mu mzinda wa Blantyre.

Escom: Magetsi savuta ngati chaka chatha.

Mkulu oyang’anira za malonda komaso chithandizo cha ogula ku Escom a Wiseman Kabwazi atsimikiza kuti chaka chino magetsi athima ndithu.

Iwo anati izi zikutsatira kuphwa kwa madzi mu mtsinje wa Shire zomwe zapangitsa kuti kampani ya Egenco izipanga magetsi ochepa.

A Kabwazi anafotokoza kuti kuthimathima kwa magetsiku kwayamba mwezi wa Julaye ndipo kukuyembekezeka kutha mwezi wa Disembala.

Koma iwo anatsimikizira mtundu wonse wa a Malawi kuti anthu asadandaule kapena kuopa kwambiri kamba koti chaka chino zinthu sizifika pa mpondachimera kwambiri ngati chaka chatha.

“Eya ndizoona magetsi ayambaso kuzimazima ndipo akuyembekezeka kuthimathima kuyambira pano mpaka mwezi wa Disembala chaka chomwe chino.

“Izi ndi kamba kakuchepa kwa madzi mu mtsinje wa Shire zomwe zapangitsa kuti tizipanga magetsi ochepa komano anthu asadandaule kwambiri chifukwa sizifikaso pa chaka chatha paja ndipo ndikutsimikiza,” anatero Kabwazi.

Kabwazi anati bungwe lawo lakhazikitsa njira zingapo zomwe zithandizire kuti magetsi asathime mobzola muyeso zomwe mwazina ndikutenga magetsi Ku dziko la Mozambique komaso kugwiritsa ntchito magetsi a mphamvu yadzuwa.

 

 

Advertisement

96 Comments

  1. We’re tired of u and hw many tymc hv u be lyng?we’re not kidz!musadzayankhuleso zamagetsi kumangokhalila ma promic without achievng them,eish mwatkwana.

  2. Kukaya uko kulije magesi, nimagesi yankhuni ayo magesi kuzimwa nyengo yiliyose? Akuba nosenu, ntchito yanu kubela anthu basi……… palibetso china chake chimene chimakuyendan m’mitu yanuyo kuba basiiiiii…………

  3. If you would say ….if God allows… it would be better but your intelligence it’s already failed.. for how long we have been complaining about electricity?

  4. Zaziiii…. Olo atadzapanda kuyakanso.. For how long have we been so lenient and patiently waiting for this? Mmapanga zimenezi coz mulipo nokha mmdziko munoo chaniii?

  5. Ine pandi fik kapn yamages yandifika pachinena akanangonena kut akulephela apase mpata makapani ena. kt alinganize ntikulephela kugwila tchitozathu bwinobwino chifukwa chakuzima kwamages..

  6. Mlungu sangalenge ziko kukhala lamavuto nthawi zonse, vuto ndimaganizidwe azisogoleli ,mazi ake omwewo kut abwere azungu magesi samazima,sciences timangophunzira kut tilembe mayeso ndi kukhala ndi ma PH opanda ntchito, hw long we will cry hence every year we have graduate engineer’s what are they doing with the knowledge acquired?.

  7. I think this is a big lie! They think that we are childrens but why? They say that we should not worrie, they will fix up the problem but yet the situation is already worse than last year, and in area 18 there is already black out••• So should we trust these people••••?

  8. Kuno Ku area 44 ndi Siku lililose akuzima mawa kuyaka madzulo kapena kuzima masana mpaka ten kololo ndiye mkumati magesi savuta maboza kkkkkkk

  9. Don’t worry guess in if u want cooking POMWE magetsi kulibe kungodula poo yamagetsiyo mkukampikira nanga Ana agone njara poti kuli blackout
    Don’t 4 got kt tchako and firewood tikakatola KU dondo akulanso akapanda ukulanda kungoti,……… Basi KU Malawi satana sayenda NDI m’didi

  10. Eee panopa nthawi zonse kumadalira magesi a Escom si Dhilu. Komano a escom wo ayesese kuti Magetsidi azikhala oyatsa m’madera ambiri.

  11. Kodi basi alephera fixing problem of blackout do you tell me boma can’t find lasting solution to this. Kkkk,long live blackout.

  12. Mbayani yonse kulibe magetsi amayaka utsiku okhaokha ati amafuna mbava ziziyenda bwino pokaba ife titagona

  13. nde china chiziti 2019 votelan ine!!!.ine sindingaiwale ada chibadwile ndadusa maulamuliro angapo koma izi ndaziona two years yomwei.zoonadi kusauka kwa ife amalawi nd chisankho chathu

  14. What are they talking about, the situation is already worse than yester year.Just imagine the whole day without electrity.Most of our economic activities rely on electric energy, with this trend am afraid Malawi cant develop.

    1. Kodi singakhale ngati yako.ikhale ngati yamzungu . Mzungu wapambana chani. Give yourself credit and stop thinking others are superior than you

Comments are closed.