Musaope, Magetsi savuta ngati chaka chatha – Escom

93

Pofuna kuzizilitsa anthu mitima pa nkhani yakuzimazima kwa magetsi komwe kwayambilanso, bungwe la magetsi m’dziko muno lati anthu asadandaule kwambiri poti vutoli silifika pampondachimera ngati chilumika chatha.

Izi zakambidwa Lolemba pamkumano wa atolankhani ndi akuluakulu a bungwe lopanga magetsi la Electricity Generation Company (Egenco) ndiso Electricity Supply Corporation of Malawi (Escom) mu mzinda wa Blantyre.

Escom: Magetsi savuta ngati chaka chatha.

Mkulu oyang’anira za malonda komaso chithandizo cha ogula ku Escom a Wiseman Kabwazi atsimikiza kuti chaka chino magetsi athima ndithu.

Iwo anati izi zikutsatira kuphwa kwa madzi mu mtsinje wa Shire zomwe zapangitsa kuti kampani ya Egenco izipanga magetsi ochepa.

A Kabwazi anafotokoza kuti kuthimathima kwa magetsiku kwayamba mwezi wa Julaye ndipo kukuyembekezeka kutha mwezi wa Disembala.

Koma iwo anatsimikizira mtundu wonse wa a Malawi kuti anthu asadandaule kapena kuopa kwambiri kamba koti chaka chino zinthu sizifika pa mpondachimera kwambiri ngati chaka chatha.

“Eya ndizoona magetsi ayambaso kuzimazima ndipo akuyembekezeka kuthimathima kuyambira pano mpaka mwezi wa Disembala chaka chomwe chino.

“Izi ndi kamba kakuchepa kwa madzi mu mtsinje wa Shire zomwe zapangitsa kuti tizipanga magetsi ochepa komano anthu asadandaule kwambiri chifukwa sizifikaso pa chaka chatha paja ndipo ndikutsimikiza,” anatero Kabwazi.

Kabwazi anati bungwe lawo lakhazikitsa njira zingapo zomwe zithandizire kuti magetsi asathime mobzola muyeso zomwe mwazina ndikutenga magetsi Ku dziko la Mozambique komaso kugwiritsa ntchito magetsi a mphamvu yadzuwa.

 

 

Share.

93 Comments

  1. Ine pandi fik kapn yamages yandifika pachinena akanangonena kut akulephela apase mpata makapani ena. kt alinganize ntikulephela kugwila tchitozathu bwinobwino chifukwa chakuzima kwamages..

  2. Mlungu sangalenge ziko kukhala lamavuto nthawi zonse, vuto ndimaganizidwe azisogoleli ,mazi ake omwewo kut abwere azungu magesi samazima,sciences timangophunzira kut tilembe mayeso ndi kukhala ndi ma PH opanda ntchito, hw long we will cry hence every year we have graduate engineer’s what are they doing with the knowledge acquired?.

  3. I think this is a big lie! They think that we are childrens but why? They say that we should not worrie, they will fix up the problem but yet the situation is already worse than last year, and in area 18 there is already black out••• So should we trust these people••••?

  4. Don’t worry guess in if u want cooking POMWE magetsi kulibe kungodula poo yamagetsiyo mkukampikira nanga Ana agone njara poti kuli blackout
    Don’t 4 got kt tchako and firewood tikakatola KU dondo akulanso akapanda ukulanda kungoti,……… Basi KU Malawi satana sayenda NDI m’didi

  5. nde china chiziti 2019 votelan ine!!!.ine sindingaiwale ada chibadwile ndadusa maulamuliro angapo koma izi ndaziona two years yomwei.zoonadi kusauka kwa ife amalawi nd chisankho chathu

  6. What are they talking about, the situation is already worse than yester year.Just imagine the whole day without electrity.Most of our economic activities rely on electric energy, with this trend am afraid Malawi cant develop.

Leave a Reply