Madzi a ku 18 salibwino: a Water Board achenjeza kuti tudzi titha kuthudzukila kachikena

145

Mavuto a madzi ku 18 aja sikuti anapitilatu, atelo a bungwe loyang’anila za madzi mu mzinda wa Lilongwe a Lilongwe Water Board.

Wamkulu wa bungweli a Alfonso Chikuni anena kuti pali chiopsezo choti tudzi titha kuthudzukila kachikena mu madzi opita ku Area 18.

water tap

Madzi avutaso ku 18

Iwo amanena izi pamene bungwe loyang’anila za ufulu la MHRC linawaitanitsa pa kafukufuku wa umve umene bungweli linamwetsa anthu a ku Area 18 mu mzinda wa Lilongwe.

“Ma pipe a tudzi sali bwino mu derali, akhalitsa ndiye sakuchedwa kuphulika,” anatelo a Chikuni.

Iwo anati ngati a bungwe ali ndi mantha kuti ngozi inaoneka posachedwa yoti madzi anasakanikila ndi tudzi itha kuchitikanso.

“Padakali pano dera la ku 18 liri pa chiopsezo,” iwo anatelo.

Share.
  • Opinion