Wapolisi yemwe anagawa zithunzi za Von Gomani amangidwe – Justin Dzonzi

200

M’modzi wa anamandwa pa nkhani za ufulu wa anthu m’dziko muno a Justin Dzonzi ati wapolisi yemwe anagawa zithunzi za munthu yemwe amanamizira kuti ndiwamkazi amangidwe.

Lolemba lapitali, a polisi mumzinda wa Lilongwe anamanga bambo wina yemwe akudziwika ndi dzina loti Von Gomani kamba kofuna kupeza ndalama ponama kuti ndi wamkazi.

A Gomani patsikuli anadzikozakoza tsitsi lawo ngati mkazi ndikuvalaso zovala zachikazi.

Von Gomani: Zinthuzi zake zidafala.

Mphuno salota, bambo wina otengeka anabwera ndikuwatenga a Gomani poganiza kuti ndi mkazi woyendayenda ndipo anapita nawo kumalo ena ogona alendo komwe zinadziwika kuti iwo ndi amuna.

A Gomani anawatengera ku polisi ndipo zithunzi zawo, zowonetsa atazikonzokonza ndikumaoneka ngati mkazi, zafalitsidwa m’magulu ambiri pa WhatsApp komaso pa Fesibuku zinthu zomwe malingana ndi a Dzonzi ndizosaloledwa.

A Dzonzi omweso ndi mkulu wa Malawi Human Rights Commission (MHRC) ati kufalitsa zithunzi za a Gomani mopanda chilolezo ndikuphwanya ufulu wa mkuluyu ngakhale kuti zomwe amachitazo ndizosayenera.

Iwo anauza imodzi mwanyumba zofalitsa mau m’dziko muno kuti aliyese ali ndi ufulu osungilidwa chinsinsi.

Poonjezera, iwo anati atha kusangalala atamva kuti apolisi omwe anagawa zithunzizi amangidwa ndinso kuzengedwa mulandu.

Von Gomani ndiochokera m’mudzi mwa Kapetera, mfumu yaikulu Kapeni mu mzinda wa zamalonda wa Blantyre ndipo aonekera ku bwalo lozengela milandu posachedwapa kukayankha mulandu wofuna kupeza ndalama m’njira yosayenera motsutsana ndi ndime 180 ya malamulo oyendetsela milandu.

Share.

200 Comments

 1. yeah akuyenera kumangidwa coz anamuphera ufulu munthu ameneyu….apolisi amajaila kwambiri…that wasn’t right at all…kumujambula munthu momuwopsyeza asakufuna adamuphera ufulu…komanso dziwani kuti ma gay amapangana za u gay zawozo okha okha…sakakamiza munthu,nawonso ndi anthu komanso ndi amalawinso ngati ena tonsefe…zaugay ndizoletsedwa kuchokera m’buku loyera “BIBLE” and sodomu ndi gomola zinawonongedwa ndi MULUNGU chifukwa cha makhalidwe amenewo..ndi MULUNGU NOT ATHU NGATI APOLISI,KODI IWOWO AKUDZIYIKA PA LEVEL YAMULUNGU CHIFUKWA CHANI???oweruza ndi mulungu osati and ankhaza ngati apolisi

 2. Ngati kumalawi kuli chiwanda cha chikulu ndi dzodzi guyz ndipo mulungu aone naye chonchita dzodzi ndi2 malo molimbikisa ufumu wamulungu akulimbikitsa ziwanda zoona dzidzi munthu opandanzelu sure

 3. Why was he taking pictures of him sharing to the whole world that is violation to his rights anthu muziziwa zamalamulo osati kungoyankhula pagulu ngati ndinu ochenjela chonsencho umbuli uli thoo

 4. Ngati uli ufulu opanga zopusa ngati zimenezi bwanji ine ndipite kunyumba kwake kwawamkulu wazamaufulu ameneyo ndikamuchinde ngati angakalole zopusa ngati zimenezo.ife amalawi timazisungira ulemu .ndindani mwa m,modzi wa kumalawi angalole kuti zinthu zopusa ngati zimenezo zizipitilira..that is nonsense…..

 5. Wamkulu wa zamawufulu ameneyo ndi galu kwabasi.and stupid man.ndiwufulu wa mtundu wanji wumenewo oyimila amuna okhaokha kuti azikwatirana.ndizopusa zimenezo kumati mulungu anali opanda mzeru polenga munthu wa mkazi NDI wa mamuna? That is foolishness.nonsense.mkulu wa zamawufulu ameneyo ndi chitsiru kwambiri galu ndatitu galu galu mbuzi ya munthu

 6. A police ,he did a good job,the world must know what is going on,well done police man,u police men why don’t u arrest both of them for immoral behavior? That gay also set him free becouse this is not justice.

 7. kkkkkk wa polic anatumiza zithuzi A TV anatumiza ma vidio ndipo zosezi zinapita kwa anthu onse kodi oyenela kumagidwa ndi ndani?

 8. Musiyeni adzigwira ntchito wapolisiyu palibepo cholakwika nanga anatukwana munthu oti amangidwe ndi aja anagwira ntchito pa 20 july 2011

 9. Nzeru Zoponsa Tikhale Nazo Umunthuso Ochuluka, Ufulu Nawo Obadwa Nawo Koma Mbuye Ndi Nkhani Ina,ine Ndi Tax Driver Ndipo Anali Customer,and Ndinalira Nditamva,and Nnadzifunsa Ndikudziyankha,satana Ndi Ziwanda Zake Alipodi.

 10. Dzonzi ukuoneka ndiwe wadyera lopusa siku lina nawe ulandira chako chilango,amangidwe chifukwa chani? Kuikira kunsana za usatana basi umudziwe yesu ndi ophunzira ake sure

 11. Inee langa ndi pepho Kwa adzodzi, ngat mkusatadi zaufulu wa mnthu, uyu anatenga yamuna mdzakeyu kuti akagonenaye nayo amangidwe, chifukwa ndiamene anafalisa uthenga Kwa apolisi, kubwelaso atola khani chifukwa Ndiwo anafalisa mma wayalesi, pomaliza inuso adzodzi chifukwa mkutiphwanyila ufulu oziwa choonaddi, umene ulii mlanduwa waukulu kwa anthu

 12. fear God first , choyamba zifuseni nokha kuti ndinu ndani pamaso pa mulungu, muzapeza yankho nokha kuti sindinu kanthu pamaso pa Mlengi anthu opotoza anthu

 13. Justin Dzonzi umunthu alibe, and he deserves mob justice by stoning him to death.

  He is a taboo
  He can bring calamity to the nation.
  Dzonzi Akudwala chiwewe chamugwira brain, chilibe mankhwala
  ationongera dziko,
  he has provoked the gods

  Kodi Galu wa chiwewe kuti asapatsire anzake, amamutani pamudzi guys?

 14. Aaaaa anthu onsewa amaikidwa ma photo awo akapalamula milandu yosiyana siyana bwanji samawamenyera ufulu???? uyuyu wapambana chani??? isaaaaa

 15. Iwe Dzonzi ndekuti munthuyo ndichibwenzi chako eti paliso zaufulu apa???? Iwe waonekeratu kuti school ya za ufulu unadumphira pa Window m’malo mwake umakaphunzira za ufulu wa satanic ndikunyenyanyenya umudziwe Yesu ndipo Jah Jah akukanthe

 16. Uchitsilu Sagawana Koma Apa Ndikutha Kuona Wina Akugairidwa Uchitsilu..A Justin Dzonzi Ndi Anzanu Onse Muuzane Mupangange Zotheka Muthetse Police Mmalawi Muno Coz Mumadananayo Kwambiri.

 17. Kkkk kkkkkkkk, some people can really prove that they are the devil’s messengers for sure. Some organisations have a real satanists foundation, dzonzi has jus proved this.
  There are real issues to deal with but busy with the issues that brings shame to GOD, why??

 18. a Dzodzi angoona kukula mutu koma nzeru alibe chimunthu chachikulu chimutu chachikulu koma kuganiza ngat mwana mxie!!!!¶

 19. Dziko la malawi silizatheka chomumangila munthu sindkuchiona apa,ufulu wake uti omwe mukunenawo azibela amuna azake pamenepo pali ganizo.mukapsa moto nonse za pa dziko koma kumwamba chanu kulibe.

 20. kod ufulu mukukambao nde uti?kod kumalawi kuliso anthu oona za ufulu wa anthu?mmalo mogwila ntchito nzinthu za nzeru ukusogilela zipusa mdziko lako? ngat nziwanda zakukwana uziuze zikakowe mu nkhumba

 21. Koma amabungwe ndi zitsiru kwambiri zoona angaikire galu ameneyo kumbiyo munaonapo tonde wa mbuzi akukwera tonde mzake? Kuli bwanji munthu wamamuna kuzisandusa kukhala mkazi akufuna chan? Ameneyo oyenera kumangidwa moyo wake onse. Mulungu analenga iyeyo ngati mamuna kusonyeza kuti sakufuna mmene mulungu anamulengera ndiye tiziti akutsata ulamuliro wa ndan? Amabungwe ndalama ndi zomwe zikukuzungizani mitu? Koma ndalama izi za pa ziko lapansi muzazisiya yembekezerani mphoto yanu pa tsiku lomaliza

 22. The photo was shared to curb the fake advertisment and con artistly by the criminal.suprised with Dzodzi.I guess u want to pocket more donor money for your useless efforts

 23. That’s not fair was it nude photos?? How about that one who post nude photos of o police woman in Kanjedza police training school??? Zilipat zimenezija?? Mpaka munamchotsa ntchito mzimai woti walakwiridwa mukumchotsaso ntchito kufa pa 2! Nde uyu mukut achotsedwe ntchito Why???

 24. Ena akhala akuchita post zithunzi za maliseche za anzawo. Wa police uja anachosedwa ntchito wina atambweza zithunzi zake koma otumiza maliseche a anzawo aja bwanji sunatamikepo Dzodzi? Monga iwo kunali kufuna? Maliseche aja ndi munthu wovala bwinobwinoyo woyenela kumumenyela ufulu ndi ndani? Ndiwe wopusa kwambiri #Nadzodzi

 25. Kodi anthu ena omwe amadzitsa kuti omenyela ufulu wa anthuwa ndidzitsiludi eti?????? Moti munthu oganiza bwino ungamayime pa chulu ndikumayankhula zopusazi???? Kodi iyeyu bambo ake adamubeleka akumagonana ndi mwamuna mzake ???? Uchitsilu sagawana koma chitsilu ichi chawonjeza ndipo sindimatha kutukwana koma ndine wokwiya kwambiri chifukwa cha zopusa zomwe galu emeneyu akuyankhula kapena iye amabeleka ana akugonana ndimwamuna mzake ???? Flesh!!!!!!!!!

 26. Kkkkkkkk Koma zinazi kusekesa kodi mukamati odziwa malamulo mumatanthauza chani? iwetu ukulimbikilila kulankhula zopusazo coz sizidakuonekele iweyo atakubela ungalankhule ngati mmene ukulankhulilamu? Okay Inutu mukudziwana ndipo mumatumana kuti akagwila mmodzi mwainu muyambe kulankhula ngati mukulankhula ndikuseri kwa lilime, Palibe chifukwa chomumangila Wa Police anagwila ntchito yotamandika

 27. Mtsogoleliyo amene wapangitsa kuti wapolisi amangidwe ndi oputsa kwambiri NDE bwanji onamizilayu akadapanga chipongwe nthawi Zina nkupha munthu mmozi mukadanenanso ndi ufulu wa bargirl wachimunayo( mbavayu)
  Kukonda zopusa basi azitsogoleli enanu
  Tamumasuleni wapolisiyo ,mwina msogoleliwe ukunena za ufulu unamtuma munthuyu
  Hahaha koma ada mbava ndizambiri

 28. Bwanji mukulemekeza zintcito za satana palibe chomangir wa polisiyo mukatelo mulimbikixa Mchitidwe onyasa mziko lathu lowopa mulunguli kulibwino chikafele kundende chizibambo chamathanyulacho

 29. Mr Dzodzi I think ndinu achisilu mwamva ndipo sindinu kholo labwino ndakwiya nanu kwambiriii za ufulu zakozo wazitengera pamgong’o asa ukuwonangati iwee iwee

 30. Amangidwe kuti chiyani akunama mumangenso a ma TV amene anamuonetsa zopusa mukufuna dziko lisokonekela mabungwe mukusowa chochota osamakagona bwanji misala etiosakamanga amene akuseweletsa ndalama za boma bwanji kupolisi kukusowa opita eta kaloweko iweyo wamabungwewe

 31. Dzonzi needs special deliverance and is a disgrace to manhood.Why does he hate police so much? He too must be arrested and taken to Zomba box 38, for treatment of his madness.

 32. Mr Dzonzi you must know that the one who posted the picture for that guy have got the right too dont be behind the one who is doing stupid thing like what he did (shame on you do you pray in the almighty God.

 33. Kodi ufulu mukuunena inu ndiye uti kupeperatu uku lamulo limati ufulu wa munthy umathera pomwe pathera zanja lake koma ngati zanja lako likhuza wina okhuzidwayo wamuphera ufulu choncho apapa von ndi mwamuna amayenera kupanga zachimuna ngati anapanga zachikazi waphwana ufulu wa akazi kotero akuyenera kukakhala kundende moyo wake onse.

 34. kod apolisiwo nthawi zonse amakhala olakwa mmmmmmh….. koma Malawian pple always hate police…..kuikila kumbuyo galu wa munthu omakwelana ndi amuna azakeo

 35. This is adverse to the government of Malawi,the must take not on this,the opposition leaders with other people the have make a plans to make the country safer,people like this one the will keep on coming out I mean that the will keep on sending them,so that if the government says something about this ,so that other country the can stop sport the country, so government of Malawi do things with wisdom

 36. Ameneyu akamangidwa ndiye murhetsenso maukwati onse apakati pa mkazi ndi mamuna tipitilize zomwe mukifunazo. Akhala bwanji Mai pomwe adapatsidwa ziwalo zachimuna? Kodi kalelani munapangako zimenezi? Mifuna amalawi atani kisonyeza kusakondwa ndi mchitidwe umeneu?

 37. Amabungwe ndinu zitsilu mwamva bwanji nthawi zambili mumayikila zinthu zopusa kumbuyo?ife tawona nkhani Za president ndikuyikaso chithuzi pompo osakambako zimenezo bwanji kapena pa kuti mukudyerapo mbolo zanu nonse amene mukudyela nkhani zopusazo bwanji mawufuluwo osapatsa ma Raster mukukana kusukulu muwofesi mawufulu akumatako

 38. This generation is going to do abomination more than Sodom and Gomorrah I feel sorry for my country Malawi the have sale the country to the devil

 39. Of course aliyese ali ndi ufulu komapa paxomwe zinacitikaxo palibe cifukwa comangila apolice. Mcifukwa ninji ozengedwa mlandu ambili nkhope zawo zankhala zikutumixidwa mma forum asiyane siyane, palibe amene amamangidwa. Ufuluwu mwazindikila lero kapena cilipo comwe mwankhala mukupeza nanuso kwa mbava yo ??????

 40. Munthu uyu sananamizire kuti ndi wa mkazi koma chibadidwe chake anabadwa ngati wamkazi chofunika anakamanga mamunayo sanamuumirize kuti amutenge akagone naye

 41. akuleka kumangidwa anthu omwe akupalamula zikuluzikulu kunjaku nde omangidwa akakhale munthu oti amagawa zinthunzi mukuti kaya,,,,,ndi nkhaniso imeneyo?????

 42. Nkhaniyi inasindikizidwanso ndi ma page ambiri aku Zambia ndipo ku Zambia ko akuti Von Gomani ndiwaku Zambia ko ifenso aMalawi tikuti ndiwakuno,komanso inuyo aMalawi 24 nanunso mumangidwe mwathandizila nawo kutumiza zithunzizi.

 43. Palibe chifukwa chom’mangira apa kutipasira zithuzi amafuna dziko liziwe,why human rights body wasting dare time talking about dis issue?what picture do u want 2 giv 2 da nation

 44. Koma Dzonzi ameneyu, amaganiza bwinobwino koma? pa maufulu onse amene takhala tikuphwanyilidwa samawawona, wotipatsiranso nkhani inu muziyamba mwawafufuza kaye anthu ngati amenewa, #alibe chipepala cha ku mental koma ameneyu?

 45. Satanism @ its best,Justin Dzodzi zimenyera ufulu a satanic amzakowo tizawona amene adzamenyere ufulu iweyo pa tsiku lomaliza pamene ambuye azasekule ma file a milandu yako.kaya mwapasidwa ndalama amene von goman ndi munthu oti angabakilidwe? dziko la pansi limakondadi ochita zoipa ndavomeleza!

  • Iweyoso uli gulu lomweli thats y ukuyankha zopusa,ngati ndi ufulu ndiye sibwenzi ndende za mdziko lino muli anthu.mumanga anthu olakwa nkhan zazing’ono ena analowa ku ndende osalakwa,nde uyu ophwanya malamulo a dziko koma bible wina nkuima kumabakira zimenezo?God forgive you otherwise you dont know what you are saying.mukufuna kukhara anzeru which xool did u went?

  • khenefi chipeta everything that goes against Gods words that is being regarded as satanic cause is being influenced by satan himself maybe you doesn’t know a word satan maybe…the one who was caught pretending to be a woman while he wasn’t thats sin before God and if is a sin then is in satans powers #khenefi #chipeta satanic comes from a word satan and that one that influences us to do wrong things is satan so dont you think thats satanic inuyo man ndiye obwelera mbuyo cause it seems kuti ndiwe mbuli pachingelezi cause had it been u knew the word satanic you couldnt have commented hate me but thats a fact

 46. Asamangidwe,instead angogawaso zithunzi za mkulu anakoketsayo timuoneko naye ayalukeko potenga mwamuna mzake kuti akathane.that’ll be fair eno

 47. Koma anthunu omenyera ufulu wanthunu manyazi mulibe? Zoona nkhani yopusa ngati imeneyi mkumayikila kumbuyo aaaaa muno mu Malawi zopusazi sitizalora till born 50s

%d bloggers like this: