Wapolisi wamwalira ataombedwa ndi galimoto malo a chipikisheni


Gun

 

Wapolisi m’modzi watisiya ndipo angapo ena avulala dzulo usiku ataombedwa ndi galimoto pomwe anali akugwira ntchito pamalo ena a chipikisheni m’boma la Dowa.

Malingana ndi malipoti a apolisi omwe nyuzipepala ino yapeza, izi zachitika dzulo Lolemba pa 17 July pa mphambani ya Dowa (Dowa turnoff), nthawi ili 19:30.

Apolisi ati mzawo omwalirayo ndi a Brown Selemani a zaka 34 ochokera m’mudzi mwa Kacheta m’boma la Kasungu.

Apolisiwa ati panthawiyi, mzawo omwalirayo komaso ena awiri anali akugwira ntchito pa malopo pomwe galimoto ya mtundu wa Mekisedesi Benzi inawaomba.

Galimotoyi yomwe nambala yake ndi BU 4897 imayendetsedwa ndi a Clement Wyton omwe amachokera Ku Mponela ndipo amalowera ku Lumbadzi mumzinda wa Lilongwe.

Chifukwa chakuthamanga kwambiri komaso chifukwa choledzera a Wyton atafika pamalopo analephera kuongolera bwino galimoto yawoyi ndipo anaomba apolisi atatu omwe anaima pa malo achipikisheniwo.

Apolisi oombedwawo anatengedwela kuchipatala cha Mtengo wa Nthenga komweso a Selemani analengezedwa kuti atsamira mkono.

Pakadali pano apolisi awiri omwe anaombedwa limodzi ndi malemuwa akulandira thandizo lamankhwala Ku Kamuzu Central Hospital mumzinda wa Lilongwe.

Apolisi amanga bambo Wyton omwe akuyembekezeka kukaonekera kubwalo lozengera milandu posachedwapa kukayankha mulandu wokupha kamba koyendetsa galimoto mosasamala.

Thupi la malemu Selemani likuyembekezeka kuikidwa mmanda lero Lachiwiri pa 18 Julaye kwawo, mmudzi mwa Kacheta, mfumu yaikulu Njombwa bola Kasungu.

Latest vacancies

143 thoughts on “Wapolisi wamwalira ataombedwa ndi galimoto malo a chipikisheni”

  1. Ndimawada a police athu kumawapha choncho posachedwa I will take saucide mission ndizingoomba ndi fraightliner they should learn to work mwa proffession

  2. apolice anyañya amafuna kumapanga źiphuphu kwa amaminibus asowa podyeŕa ndiye waluza ndani ?komanso pa dowa turn off malo pali road bloçk ndimalo añg’ono amaonjeza apolicewa mmmm hasi zachitika

  3. Muthuyu waombedwa kapena waombeledwa chifukwa tikaona kutsogolo kwa mfuti kuli unsi kunsonyeza kuti waombeledwa.muwauze athu zoona zenizeni

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading