Wapolisi wamwalira ataombedwa ndi galimoto malo a chipikisheni

147

 

Wapolisi m’modzi watisiya ndipo angapo ena avulala dzulo usiku ataombedwa ndi galimoto pomwe anali akugwira ntchito pamalo ena a chipikisheni m’boma la Dowa.

Malingana ndi malipoti a apolisi omwe nyuzipepala ino yapeza, izi zachitika dzulo Lolemba pa 17 July pa mphambani ya Dowa (Dowa turnoff), nthawi ili 19:30.

Apolisi ati mzawo omwalirayo ndi a Brown Selemani a zaka 34 ochokera m’mudzi mwa Kacheta m’boma la Kasungu.

Apolisiwa ati panthawiyi, mzawo omwalirayo komaso ena awiri anali akugwira ntchito pa malopo pomwe galimoto ya mtundu wa Mekisedesi Benzi inawaomba.

Galimotoyi yomwe nambala yake ndi BU 4897 imayendetsedwa ndi a Clement Wyton omwe amachokera Ku Mponela ndipo amalowera ku Lumbadzi mumzinda wa Lilongwe.

Chifukwa chakuthamanga kwambiri komaso chifukwa choledzera a Wyton atafika pamalopo analephera kuongolera bwino galimoto yawoyi ndipo anaomba apolisi atatu omwe anaima pa malo achipikisheniwo.

Apolisi oombedwawo anatengedwela kuchipatala cha Mtengo wa Nthenga komweso a Selemani analengezedwa kuti atsamira mkono.

Pakadali pano apolisi awiri omwe anaombedwa limodzi ndi malemuwa akulandira thandizo lamankhwala Ku Kamuzu Central Hospital mumzinda wa Lilongwe.

Apolisi amanga bambo Wyton omwe akuyembekezeka kukaonekera kubwalo lozengera milandu posachedwapa kukayankha mulandu wokupha kamba koyendetsa galimoto mosasamala.

Thupi la malemu Selemani likuyembekezeka kuikidwa mmanda lero Lachiwiri pa 18 Julaye kwawo, mmudzi mwa Kacheta, mfumu yaikulu Njombwa bola Kasungu.

Share.

147 Comments

 1. WAPOlice kuti amungunde amapanga chain nayese ndiwatulo ameneyo ; kupusa basis prembrem Malawi 24 does no gun that is prombren its better me a mus buy gu n and give everyone l got too much many hhhhhhhhhbh

 2. Ndimawada a police athu kumawapha choncho posachedwa I will take saucide mission ndizingoomba ndi fraightliner they should learn to work mwa proffession

 3. apolice anyañya amafuna kumapanga źiphuphu kwa amaminibus asowa podyeŕa ndiye waluza ndani ?komanso pa dowa turn off malo pali road bloçk ndimalo añg’ono amaonjeza apolicewa mmmm hasi zachitika

 4. Muthuyu waombedwa kapena waombeledwa chifukwa tikaona kutsogolo kwa mfuti kuli unsi kunsonyeza kuti waombeledwa.muwauze athu zoona zenizeni

 5. Imfa yamtundu uliwonse ndiyowawa koma a police akakhala paroadblock azigwiritsa nzeru mitu yawo cifukwa amaiona galimoto ikubwera mwaspeed mwina driver analuza control koma iwo kusaganiza zothawa pamsewu mwina akanangotseka r.block driver akanagunda r.block.wapolisiyu wafa ndizinthu zoti akanazipewa.ok RIP Moyo usamalireni banja ndi ana pepani mulungu akutonthozeni sorry

 6. I aint cerebrating a mans death but sometimes a police amazafatsa kwambiri pa msewu as if njale kuwaomba sangapweteke or even kufa….

 7. Sorry guys. Anamuwidwa anali pa Chanco Reporteryi ndiye poti adya chani patawuni ananoyamba zimenezi koma kunena zowona wakulila ku Mzimba ndiye sakuziwa kanthu pepani ntawuni muno wangobwela. Mzake ndi baby yayimuna yamangidwa ija ndi ma best friends

 8. Who was ur Lecturer at University, I want to talk to him. If a deceased was hit by the car, then what is a reason of putting hands holding a gun as if he was shot. And if u r reporting on Social Media, and what is a reason of talking about newspaper as if u r reporting on newspaper, is this a paper?

 9. apolisi amanditenga mtima kobasi amakonda kuima malo obisala ati azilandila ndalama kwa anthu ndiye atengelepo phuzilo chifukwa mowawo ndiye tikuumwa ngati sasamala aphedwadi sanati

 10. Chipikiseni chabwanji? U say Galimoto bt u a showing a gun hw do these things relate? Ine ;( ndingoti pepani ana padzuwa.koma uyo wina wacibale ndamuona akutsekelela mkazi wa malemuyo.hahahahahaha sole.

 11. Zikuchita kumveka bwino kuti waombedwa ndi galimoto osati zoombeledwa ndi mfuti….tisamangopanga criticise zili zonse…. anyway REST IN PEACE mr Police man

 12. walemba nkhaniyi ndi pumbwa kuombedwa ndikuombeledwa ndimawu awiri otsiyana. ngati waombedwa ndigalimoto paonesedwa bwanji mfuti? umbuliwu ndimatenda ndithu kkkkkkk

 13. Nkhaniyo ndiyowona munthu wawombedwa kugundidwa ndi galimoto inu mukaikaso futi. komaso apolice zomaima malo obisika kuona galimoto ndikumangothamangila mumsewo sibwino mumaika moyo wanu pachisye. ma driver ena mmaimidwe otele amayesa akuba. ntchito ndi ntchito komaso moyo kumaukonda.

 14. malawi 24, you want to tell us that a gun is a car? can’t u see that u are misldading young ones on the part of learning through matching and association?

 15. Eishhhh zina ukaona kamba anga mwala fundo ranga nali a womberedwa or aombedwa which is which be??? Sinfikutha kumvetsa nkhaniyi

 16. vuto la amalawife tilibe chisoni timayiwala kuti anthuwa ndi ofunikila kwawo ali ndi ana,mkazi,makolo apongozi any way RIP

%d bloggers like this: