A Mutharika sanayenera kujomba ku msonkhano wa AU

151

M’modzi mwa akatswiri pankhani za ndale m’dziko muno a Wonderful Mkhutche ati mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika mwanjira ina iliyonse anayenera kupezeka kumsonkhano wa atsogoleri maiko a mu Africa.

Wonderful Mkhutche

Wonderful Mkhutche: Sizimayenera kukhala chomwechi.

A Mutharika sanakhale nawo pamkumano wa atsogoleri a bungwe la African Union (AU) wanambala 29 omwe umachitikira ku Ethiopia.

Kumsonkhanowo dziko la Malawi linaimililidwa ndi kazembe wa dziko lino ku Ethiopia a Chimango Chirwa.

Poyankhula ndi nyuzipepala ino, katswiri pandaleyu wati chiganizochi sichabwino kwenikweni potengera kufunikira kwa msonkhanowu ku dziko la Malawi komaso kwa mtsogoleri.

A Mkhutche anena kuti chifukwa chopulumutsa ndalama chomwe likupeleka boma pakulephera kwa a Mutharika kukhala nawo pamsonkhanowu ndichosamveka.

“Pali zinthu zambiri zomwe boma lingachite pofuna kutitsimikizira kuti limasamaladi ndalama za ife anthu opereka misonkho osati kulepheretsa ulendo ofunikira ngati uwu.

“Vuto ndiloti dziko lino muzaka zapitazi lalephera kugwiritsa ntchito bwino mwayi wopezeka kumsonkhanowu ndichifukwa chake lero msonkhanowu timauona ngati opanda ntchito ndipo kupita kwathu kumangokhala ngati kukakwanilitsa chiwerengero,” atero Mkhutche.

Munkuonjezeraka kwawo a Mkhutche ati a Mutharika anapanga izi ngati mbali imodzi yandale komanso ndi cholinga chophimba anthu m’maso ndi kupewa zoyankhula za anthu.

Iwo anamaliza ndikunena kuti zinakakhala bwino mtsogoleri wa dziko linoyu anakapita ku msonkhanowu kuti akapereke dandaulo lake pankhani yolimbilana gawo lina la nyanja ya Malawi pakati pa dziko lino ndi dziko la Tanzania.

Share.

151 Comments

 1. Musiyeni sabwelera msanga kwao akapita m’misonkhano ameneyi,,kulita kwambiri,anzake onse amakhala kuti abwelera mwakwao koma iye amakhala kuti akanali komweko or kuti msonkhano watha,,kuzipita achangu kuti azibweresa zotsatira msanga

 2. ameneyo si katswiri ndawona,umunthunso mulibe,mwina sukuluyo kapena,ndiye pamenepa chalakwika ndi chani kusapita,amakudyetsani ma buns kapena andalewa? akanapita mukanayankhula zambirimbiri apanso wajomba walakwanso,Malawi sadzatheka ndithudi.

 3. msonkhano wopanda ntchito..it lost its purpose way back..kukanika kupeza resolution ya issue ya nyanja ya mw,..nde tidziti azitsogoleri amenewa can they be trusted?? ninsense

 4. Kunena zoona I don giv a damn whether he goes or not it remains the same. The punchin bags we are, u get a salary u get punched (tax) and u go to buy tings Mr tax is there, wha the hell!!!

 5. If busy or sick can send a vice isn’t a punishment ,even if he can go or not, will never boast our economy…..never!!

 6. l think we malawians now what l can see is just a heart of jealous why alwez we like blaming our president thats not true and this is not only here in Malawi but all countries in Africa we like this let these leaders lead us its there time

 7. Akajomba walakwitsa! Akapitanso walakwisa! Malawians what should a person do for your satisfaction? Our leaders are not problems, we are the problem and that can end only if we change our jelous mindset!

 8. Basi ifeyo choona tachidziwa munthu yu Ali bwino ndipo dzikoli akuliyendetsa bwino kuti zikupwetekeni kwambiri tizangomuvotera kachiwiri kuti inuyo muzingolira ndi nsanje yanuyo choncho

 9. Umh ayi munthu olo atatani sangaoneke ubwino wake in government chilichose criticism? umh umh shame on you Malawians bizy trying to still pull our nation down,go to hell

 10. Apapo ndipamene ndadzindikila kuti peter alibe vuto lililonse Ku mtundu wa amalawi anthu mukumamutukwana chifukwa cha jelasi yofuna kungodana naye anangapita mukananena zambiri kuti akuononga ndalama za misonkho yanu a Malawi taonjezanotu.

 11. A Malawi sindikuziwa chimene mumafuna kwa asogolele athu, kaya ndi ufiti kaya ndi kusuta kaya ndi nsaje, anakapita zokamba za mbiri mbiri mimba zanu musiye ku nyoza asogoleli kuyambila lelo.

 12. Even though it can’t change the mountain,we are already stupit happy we are that we are second leading in africa interms of baby manufacturing and early marriages that doesn’t last long.happy independence 53

 13. Mmmmm mkului kujombako amafuna akondwelele 53,independent, unluckily kunachitikaso ngoz and it’s not his 4t it happen s,koma hw much did he spend on independent day compared to he could go to AU summit,Tanzania Skip’s the freedom day to avoid expenses, y my Malawi z still expending on the day while eni ufulu akuvutika ulova,

 14. inu guys,mukudabwa chani kodi? anthu akumunena kuti why sanapite komanso akanakhala kuti wapita bwenzi atalandira ma phuzo anthu kumutukwana right? the answer is that majority of malawians doesn’t like him,take or liv it but mak my words..

  • The main reason it’s most pple are savages the fact that you don’t like his policies it’s not reason enough to insult him.. I hope one day we shall learn to disagree respectfully and with dignity.He is president

 15. Zangozi ndi khaniyi sizikugwilizana amalawi chakula pano ndi mtopola basi ndikona sitikutukuka uphawi ukuchita kutifinya kamba kokamba zopanda mutu akanapita mukanati walakwa kusapitanso mukuti walakwa ana afa pangozi mukuti wapha ndi pulesideti mumaganiza bwanji amalawi azanga ?ngati chonena mulibe pena kukhala chete sikulakwa ayi.

 16. Kungoti a Malawi vuto lanu ndichani? President akayenda mumalankhula zambiri, tsono lero sanapite ku msonkhano mukulankhulanso kwenikweni mukufuna chani. KASWIRI WA NDALE ndiyekuti chani? Dzina lodyera

 17. He should surppose kuti akaonekere nangano mfundo zomwe akambilane kumenekozo iye azidziwa bwanji zomangilira Africayi kuti akhala wabwino tikamati kusemphana nazo zochitika ndiye uku, wakhala ndiye pano akuchita chiyani kumalawiko?

 18. Akanapita bwenzi mukutukwana, lero sanapite mukuti sanachite bwino! Munasuzgo mwe! You don’t know what you want! Winawu ndiufiti tsopano.

 19. Apite mumvekere akuononga ndalama ….za boma…akhalenso osapita ….ntchito sakuitha yotukula miyoyo ya amalawi.!!! Eshiiii..mukufunano chiani agalu amaliongo?

 20. amalawi ndinu mbuz za athu last tym muthalik anapta ku america ndpo munakamba zambli kt akutha ndalam apa wakhala mukuti aiso amayenela kupta mixewww nde ife tive zit? kmas akatswli enawa akungofun kutchuka

 21. OUR PRESIDENT WENT TO SCHOOL AND HE KNOWNS WHAT TO DO AND NOT TO DO. HE CHOOSE NOT TO GO TO THE SUMMIT AND AS A NATION WE HAD TO ACCEPT IT NOT CRITICISING FOR THE SAKE OF TO BE HEARD

 22. I don’t have problems with the president travelling but Iam a bit uncomfortable with the number of people who accompany him for the sake of pleasure

 23. Kikkkkkkki wasuta kwambiri chamba iwe,akadapita wekha ukadati akuononga ndalama za msonkho,amalawi mulibe pabwino maka inu andale mmafuna popezera campaign kugwesera anzanu ngati ngolephera,choncho sitingatukule dziko lathu

 24. Akatswir Opusa Mungochtapo Zilizonse Kulowetsa Ndale Ndye Wabwino Ndan Mwatkwana Tsopano Wabwno Tmudzwa Ndfe Tsopano Fwetseke

 25. Very Stupit,what Variety Of Person Is He?When Peter Skipd The Senarial Ur Lameting Hhhh Like Un Own,now Ur Hissing Like A Snake,so What Do You Want To Him?I Can Say That Peter Is Doing Something Better,and Comming Election He Is Going To Be Re Elected

  • Mention 2 things mutharika is doing better?To be a Dpp member doesn’t mean you must support everything.Wheither u like or not,Peter is waist president we had in Malawi.

 26. Ur teacher will ask u to write an essay about ADAY U WILL NEVER FORGET. At the end he give u 17/ 50 as if that day he was with you

 27. Muzinena momnveka kuti katswili pa nkhani za maphunziro a Ndale. Munthu sanaimilepo ndi u khansala omwe. Sanapangepo campaign mkuona kuti wayankhulako za mzeru anthu amukonda, Yake ndi theory mkalasi basi. Akhala bwanji katswili pa nkhani za Ndale. Mpira omango fotokoza pakamwa kapena osewela wekha popanda okumaka aliense akhoza kuoneka dolo.

 28. Inu ndinu abodza sopano. Muziyamika. Sikuti poti mulimbali yina muzingopanga critisize everything. Apa ineyo ndawayamikila kwambiri a President.

 29. Koma mwati akatswiri enawa ndi eni eni koma? Anakapitanso munakati akuyenda kwambiri akuonongonga chuma, eeeeeeeeeeh kkma yaaaaa! Kuyendetsa dziko sizochedza guys.

 30. Sakanakwanitsa kupita, amadikila sacrifices yomwe amakapanga kulilongwe kukapha miyoyo yosalakwa kamba ka kukhwima #luminat

 31. Nonsense,Akanapita bwenzi inu nomwe mukuti akuyenda yenda (akuononga ndalama zaboma),kodi inu ndinu ndani?inu ndi ndani?,anthu osaganiza koma kusintha sintha zoyankhula.

 32. We also have big problems we Malawians, had it been anapita something differently zikananenedwa. I am not his fun but let’s appreciate wen some1 dd a gud job. Envy won’t take us anywea. Let’s unit to develop this country but izi zomango pointing fingers will not help us and the this country.

 33. He is afraid of being ashamed with what is happening in the country. His gvt is full of blunders. Alot of …..gates within two years of his rein. Shame.

 34. okoma atani abale?mutapasidwa mwayi oyendetsa dziko kwa mlungu umodzi mungakwanitse inu?why always criticising , without appreciating other people’s ďeeds?yóu fault finders tatopa nanu tsopano.

%d bloggers like this: