Mabuluku ong’ambang’amba avuta pa Malawi


Mabuluku ong’ambang’amba avuta pa Malawi- Malawi24

Siumphawi koma kufuna kuyenda ndi nthawi kwapangisa achinyamata mu dziko la Malawi kugwa m’chikondi ndi mabuluku ong’ambang’amba.

Mabulukuwa akumakonzedwa m’mawondo ndi mu ntchafu, kupangisa kuti khungu lizionekera kudzera m’mabowo munthu akavala. Kukula kwa mabowowa kukumasiyana.

Kafukufuku waonesa kuti khalidwe limeneli likufalisidwa ndi akatswiri otchuka kumbali ya msangaluso. Monga oyimba, akumakonda kuvala mabuluku okhetekawa mu ma kanema a nyimbo zawo. Ndiye achinyamata owakonda akutengera kuti nawo awoneke otsogola.

Avuta pa Malawi.

Izi sizikutengera kuti ndi nyengo yozizira, pamene achinyamata akumkeramkera namatchena zovala zoterezi. Iwowa akulolera kuti azizidwe bola aoneke mopereka chikoka ndi kuyamikiridwa kuti ndi ozitsata.

Mtundu wamavalidwe amenenewa unafika ndi pakanthawi koma panopa wafikapo. Potengera kuti ku mayiko ena mabuluku wa anakhazikisa maziko pakale, zapangitsa ena kuti anene zoti “zikubwera mochedwa.”

Ngakhale achinyamata agwa m’chikondi ndi mavalidwewa, izi sizili choncho ndi achikulire amene adandaula kuti izi zikuononga chikhalidwe cha a Malawi.

Ngakhale achikulire ena akumazilimbitsa mtima ndi mawu oti “wakalamba wafuna” kenaka nawo nkuvala mabuluku a mtunduwu. Kwa ena opanda makobili okwanira, akumang’amba okha mabulukuwa.

Ogulitsa malonda akupha makwacha koopsa ndi mtundu wazovala umenewu. Posatengera kuti mabulukuwa akumakhala ong’ambang’amba, anthu akumafapo makobiri ankhaninkhani kuti agule.

Ngakhale izi zili chonchi, mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, akulimbikitsa a Malawi kuti azigula zovala zachikhalidwe zosokedwa Ku Malawi konkuno.

Latest vacancies

257 thoughts on “Mabuluku ong’ambang’amba avuta pa Malawi”

  1. Mudziko la malawi??? Mayiko ambiri inu Malawi24, munthu sangamavale “Nyanda” lero lino, fashion imasintha mosogozana ndi generation imene mulimo, kale anthu amavala mikhajo ma gulu achina yonah,noah yesu,,,ndani ndani,,,chikhala ngati analipo mpaka lero lino bwenzi iwonso akuvala ma buluku,ma suit ma jeanz zonse kutengera m’bado womwe alimowo,,ndiye si malawi yekha yemwe anthu akumvala zong’ambika za new-one,mwinanso malawi nkukhala womaliza pa nkhani ngati zimenezi

  2. Kunena zoona munthu opusa samagwirizana ndi chiphuzitso chabwino taonani enanu mukutukwana coz ndizovala zanu zimenezo km ngakhale mutukwane a 24 akunena zoona nose ovala chonchi ndiopusa .

  3. Plz God av mercy open our spiritual eyez so that we can recognise that we ar in last dayz and satan iz usng anythn kt athe kuwina miyoyo yochuluka (hoseya 4v6)

  4. Hey am from Zimbabwe,,, we are nolonger living in the past,, world over thats the way we dress,,, thats why many African countries fails to success,,,because of background minded,, thumbs to these who wear this clothes thats the fashion

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading