Apha mkazi chifukwa cha nsanje: ati anangomumenya ndi Bango kamodzi basi

knife-blood

Bambo wina wa zaka makumi atatu kudza mphambu zisanu ndi imodzi (36) ali m’manja mwa Apolisi a mu boma la Lilongwe atapha mkazi wake.

Malinga ndi Apolisi, bamboyu ndi a Major Wilson ochokera mu boma la Mulanje.

Apolisi ati Bambo Wilson anakhala pa banja ndi mkazi wawo kwa zaka khumi ndi zisanu (15).

Iwo ati anauza Apolisi kuti masiku atsopano anakhala akumva mphekesela yoti mkazi wawo anali kuyenda ndi amuna ena.

Ndipo tsiku lina anapita pa okala ya banja lawo pamene anasiya akazi awo. Atafika kumeneko anapeza mkulu wina akuzagula malonda. Iwo ati anadabwa ndi machezedwe a awiriwo ndipo anakayikila kuti mkuluyo anali m’modzi mwa oyenda ndi akazi awo.

Iwo anathamangitsa mkuluyo ndipo atapita kunyumba anayamba kukangana ndi akazi awo.

Ati iwo kenako anatenga Bango ndi kuwamenya nalo ndipo iwo anathawila kubalaza kumene anakafela.

Koma a zachipatala ati mayiyu anamwalira kamba kovulazidwa m’mutu ndinso kutaya magazi ochuluka.

Bambo Wilson akuyembekezeleka kupita ku Khoti.

Advertisement

77 Comments

 1. Kupha Mkazi Chifukwa Chasanje Sibwino Ayi.Ndibwino Kumusiya Mkaziyo,akazi Onsewa Man Ndiye Mupangitsa Kuti Ana Akhale Pamavuto Tsopano Chifukwa Chazibwana Zanu.

 2. Zatero kodi ati…. Nkhani yomvetsa chisoni kwambiri… I think Pena pake akazi azitha kudziziwa kuti ali PA banja… Kotero akuyenera kumupanga zinthu zoti zisasemphane ndi zomwe mwamuna akufuna

 3. Koma dziko latha.mkazi kuphedwa ndimamuna wake anthu inu kumayamikira mulungu akukhululukileni njira yabwino kumusiya mkaziwo ali moyo iwe ukwatira nayenso akwatiwa moyo wanonse kumapitilira.akazi onsewa akusowa amuna nzeru yofunsira inathera pa iyeyu?uhulewo amachita ndi thupi lake.bambo uyu aphedwe mwinanso uhule amachita potopa ndinkhanza zachigawengachi

 4. y Malawian men like to do this.Y if you see that she doing wrong things just throw him away then find another onather one there is a lot of ladies in Malawi please stop this

 5. Kuchidapa bwanji ankaz Ali palipose akusowa amuna asaaaaa koma nanu ankaz musiye ma social media ndipo mmapezela zolakwika mpaka akukuphani

 6. bambo wina wodziwika ndi dzina loti Bilton Wapha Mkadzi Wake Ku Mangochi, Namwera Kwa Mwawa Pa Chifukwa Chomwe Sichikuziwika Bwino, Bamboyu Ndi Wazaka 58 Ndi Mayiyo Ndi Wazaka 51, Pakadali Pano Ali Mmanja Mwa Apolisi Kaya Malawi24 Inali Kuti?

 7. some women r like internet viruses,they enter into your life,edit your mind,scan your pockets,download their problems & delete your smile

 8. Nkhuku yoweta samagula pa nsika.Zomangotolanapozi kaya,lero ndinu mwayamba kuchuchitsa mwazi.Chitsilu kumakachitula kwa mwini wake,chimakhala mpokomela kwa mwiniyo.

 9. Sitikulemekeza Moyo,akazi atha? Vuto losadziwa kufunsira ndi limeneli,wakundende basitu supadzapaonanso,ambuye akuyendere munthawi yakusautsika kwako!

 10. komadi pano zanyanya ndithu Amuna kutopa uku koma tipeza njila INA yowa phela kupatula yomenyayi ndi #madamu-kesi akazi aonjeza ndithu ndi fiti ziphedwe basi tizigwilitsa ntchito poison kuti azikafela kwawo tisamamangidwe Amuna ambili pano pakhomo kumapezeka ana 5 popandapo nmodzi wako akaganyule uko akaona kuti nmimba mwatentha basi ndi we bae bae bae ndili after iwe lelo lose lino ndeaku bwinditse mowilikiza mawa ndilinalo akuuze Kukhala Ngati ndili ndi mimba iwe nkuganizila ndi game nmomwe unachitila sukana umangoti tisamala eni ana Ali pheeee kwawo aphedwe ife tinasiya zosilila kukwatila or chibwezi zikavuta timakagula VIP Ku bwandilo kapena tchezi ntemba no mathathixo

 11. Palibe cholakwika pamenepo wapha mbali imodzi yathupi lake baibolo litero mkazi ndi mamuna ndi thupi limodzi ndiye palibe chomangira muthuyo atuluke basi bola kumanga Chaponda anaba ndalama zathu

 12. Nsima Munthu Umatha Kuitanira Kwa Mzako”BWERANI TIDYE NSIMA?”nanga Kodi Ndindani Adaitanirapo Chisebwere”BWERANI MUZAGONANE NDI WACHIKONDI WANGA?”nsanje Imapha Nazi Tikumvazi,maliseche Asiyana Ndi Chokudya,posewera Ine Kumva Kt Wina Akulakalaka Kusewera Ndimusowesa.Uyo Walakwa Kupha Bebi Malo Moti Akadathana Ndi Uyo Amamuganizirayo.Kaya

 13. Apha Mkazi Atamummenya Ndi Bambo,umenewu Ungakhale Mutu Wa Nkhani?

  BAMBO APHA MKAZI WAKE.
  mwaona bwanji pamenepo. zisiru za atolakhani a J.C.E certificate.Learn To Compose Headline.

 14. “mmmmmmm” nkhani zina ndizovuta kuti uzimvetse, nkhani ya zibwenzi m’banja kunena moona akuchulukira ndi azibambo. Ambuye atithandize ndithu.

  Uyu wapha mkazi wake, mmmmm Ambuye achite naye. Mzimu wake uwuse mu mtendere “rip”

  Boma lichitepo kanthu kwa anthu ngati awa.

 15. Ife tikudandaula kuti ngozi zapa nseu zachaluka iweso ndikukaphaso mkazi wako ndi stick magic yako aaa nayeso aphedwe basi kuti zithu ziyende boh

 16. Ife tikudandaula kuti ngozi zapa nseu zachaluka iweso ndikukaphaso mkazi wako ndi stick magic yako aaa nayeso aphedwe basi kuti zithu ziyende boh

Comments are closed.