Sitisintha malamulo ndiomwewo – apolisi a pansewu atemetsa nkhwangwa pamwala
Apolisi apansewu mudziko muno atemetsa nkhwangwa pamwala kuti iwo sasintha malamulo omwe abweretsa atsopano ngakhale ma shoveli amaminibasi ndi owathandizila awo anapanga zionetsero.
Izi ndimalingana ndi wachiwiri kwa wa mkulu wa apolisi apansewu mmchigawo chakummwera a Alex Zimba omwe anena izi kuimodzi mwa nyumba zofalitsira nkhani mdziko muno.
A Zimba anena kuti zomwe akufuna oyendetsa magalimoto onyamula anthu komaso owathandiza awo kuti asinthe malamulo ena apansewu omwe abweretsedwa kumene, ndizopanda pake.
Iwo akanitsitsa mwantu wa galu kuti oyendetsa magalimoto onyamula anthuwa asayembekezele kuti momwe anapanga zionetsero lachisanu lapitali zinthu zisintha.

A Zimba anena kuti malamulo atsopano omwe awakhazikitsa apansewu ndichifikwa chakuchulukwa kwangozi zapansewu zomwe sizinasiye malo mdziko muno.
Moonjezera iwo anena kuti cholinga chawo sikufuna kuletsa galimoto za mtundu wa minibasi kuyenda mminsewu mdziko muno koma kufuna kuteteza miyoyo ya anthu onse oyenda pansewu.
Lachisanu lapitali pa 23 June, oyendetsa maminibasi mumzinda wa Blantyre anapanga zionetsero zokwiya ndi malamulo atsopano omwe akhasikitsidwawa ndipo oyendetsa maminibasi aku Mzuzu anapanga zionetsero tsiku lotsatila lake lomwe linali loweruka pa 24 June komweso anthu angapo anamangidwa kamba la zionetserozo.
Ena mwamalamulo atsopanowo ndioti: osakweza thumba la chimanga kapena katundu minibasi ndipo opezeka azilipila mlandu wa 20,000 MK kapena kukagwira ukaidi wa zaka zisano mogawana oyendetsa ndi omuthanfizira (Dalaiva ndi kondakitala).
Mashoveli onse amaminibasi auzidwa kuti asiye kukweza anthu anayi anayi mmipando ndipo kupezeka otero azazengedwa mlandu zaka 5 aliyense kapena 150,000 MK mogawana shoveli ndi omuthandiza.
Oyima malo osaloledwa (Wrong parking) azipeleka 20,000 MK kapena zaka zisanu ndipo lamulo lina lapita kwa ma basi akuluakulu kuti basi isayende usiku yopezeka mlandu 200,000 MK komaso mubasimo musamapezeke oima kupezeka oima mlandu 200,000 MK kapena dalaiva ndi kondakitala ku ndende zaka khumi.
Latest vacancies
171 thoughts on “Sitisintha malamulo ndiomwewo – apolisi a pansewu atemetsa nkhwangwa pamwala”
Comments are closed.









Akuluakulu komanso ang’onoang’ono, chomwe ndachiona pano nchoti , anthu amene amadzitcha anzeru ,omveka ,achuma ndi odziwika m’dziko , amafuna azitipangira timalamulo toti ife amphawi azitisowetsa mtendere basi akatero iwo kumtima mbee!!! . Anthu oterewa alipo ochepa kwambiri ndipo akunama ndi afana sativuta ,2019 tizasankhe anthu ngati awa:
1 :osauka kwambiri komanso wokhala kumudzi ,chifukwa akhonza kudziwa mmene umphawi umawawira etc ..
2 :wosaphunsira koma wodziwa kulankhula chingerezi chifukwa ndi chinenero
3 : mupitilize ndinu kwiko !!! Mpaka no:10
Apolisi Ngati Mwasowa Nthito Pitani Kanyereni Kwanu! Kagadileni Nyanga Za Azigogo Anu Ku Midzi.
Koma police mmm uniforomuyi mmmmm peza ina,,,,
u driver ukhala ntchito yopweteka zedi
Koma winayo njala inamuswa kuyasamula chochi sipalupaso apa
Kod Pamenepa Anthu Aziyendera Abale Ndi Anatsi Awo…? Bcz Akamayenderana Amatenga Kenakake Monga Thumba La Chimanga Kapna Ufa, Nanga Azichita Hire Galimoto Bcz Of Asingle Bag.? Is This True…?
Tsopano munthu wagula thumba la chimanga pa Njuli nde ulisenze mpaka mu Limbe? Mmene dziko lathu lasaukiramo anthu ma transport adziwatenga kuti? Inu kukhala ndi galimoto si onse ali nazo.
Kk
Dziko lapansi lamulaka mphawi
Kkkk timakonda zimenezi osaopa
Malamulo Ali bwino awa kma akanatiganizlako zathumba lachimangalo
Dil ili bwino
Driver Osasambanso Muzitaninaye?
Ine ndikupanga support malamulo awa: 1. Azikhala ndi ulemu kwa ma passenger.
2. Mpando umodzi anthu atatu.
3. Aziima mmbali mwa nsewu osati zoima mwachisawawa.
4. Conductor achokemo chifukwa amaiwalitsa ma passingers change.
Note; awa ma driver akuona ngati ndife ana, za thumba la chimanga atiganizira koma zinazo ndiye akangopanga awamange basi chifukwa mmene amapita kumayeso a ntchito ya driver zonsenzo anazipeza ndipo anavomeleza kuti azasata malamulo.
Koma chonsecho misewu idakali yamakedzana… Nd’e ngozi zitha?
Bravo apolisi. Nganga
Kuba
Kodi apapa anyamata akujambula Dvd yandan
Very Stupid Policy!!! Zimba you are very stupid.
Minibus isanyamule katundu, lory isanyamule anthu.kodi munthu kuoda katundu wa 30 sauzanda angapange hayara galimoto? Koma boma ili ndilankhanza