Sitisintha malamulo ndiomwewo – apolisi a pansewu atemetsa nkhwangwa pamwala

Advertisement

Apolisi apansewu mudziko muno atemetsa nkhwangwa pamwala kuti iwo sasintha malamulo omwe abweretsa atsopano ngakhale ma shoveli amaminibasi ndi owathandizila awo anapanga zionetsero.

Izi ndimalingana ndi wachiwiri kwa wa mkulu wa apolisi apansewu mmchigawo chakummwera a Alex Zimba omwe anena izi kuimodzi mwa nyumba zofalitsira nkhani mdziko muno.

A Zimba anena kuti zomwe akufuna oyendetsa magalimoto onyamula anthu komaso owathandiza awo kuti asinthe malamulo ena apansewu omwe abweretsedwa kumene, ndizopanda pake.

Iwo akanitsitsa mwantu wa galu kuti oyendetsa magalimoto onyamula anthuwa asayembekezele kuti momwe anapanga zionetsero lachisanu lapitali zinthu zisintha.

MINIBUSES
Oyendesa ma minibasi amakhiyana ndi apolisi a pa nsewu pankhani ya malamulo atsopano.

A Zimba anena kuti malamulo atsopano omwe awakhazikitsa apansewu ndichifikwa chakuchulukwa kwangozi zapansewu zomwe sizinasiye malo mdziko muno.

Moonjezera iwo anena kuti cholinga chawo sikufuna kuletsa galimoto za mtundu wa minibasi kuyenda mminsewu mdziko muno koma kufuna kuteteza miyoyo ya anthu onse oyenda pansewu.

Lachisanu lapitali pa 23 June, oyendetsa maminibasi mumzinda wa Blantyre anapanga zionetsero zokwiya ndi malamulo atsopano omwe akhasikitsidwawa ndipo oyendetsa maminibasi aku Mzuzu anapanga zionetsero tsiku lotsatila lake lomwe linali loweruka pa 24 June komweso anthu angapo anamangidwa kamba la zionetserozo.

Ena mwamalamulo atsopanowo ndioti: osakweza thumba la chimanga kapena katundu minibasi ndipo opezeka azilipila mlandu wa 20,000 MK kapena kukagwira ukaidi wa zaka zisano mogawana oyendetsa ndi omuthanfizira (Dalaiva ndi kondakitala).

Mashoveli onse amaminibasi auzidwa kuti asiye kukweza anthu anayi anayi mmipando ndipo kupezeka otero azazengedwa mlandu zaka 5 aliyense kapena 150,000 MK mogawana shoveli ndi omuthandiza.

Oyima malo osaloledwa (Wrong parking) azipeleka 20,000 MK kapena zaka zisanu ndipo lamulo lina lapita kwa ma basi akuluakulu kuti basi isayende usiku yopezeka mlandu 200,000 MK komaso mubasimo musamapezeke oima kupezeka oima mlandu 200,000 MK kapena dalaiva ndi kondakitala ku ndende zaka khumi.

Advertisement

172 Comments

 1. Malamulo alibwino kwambiri…anthuwa amaonjeza bus mpaka anthu 30 kuimilira aaaah zimabowa kumene..komanso a min bus amakonda kuika zimatumba kapena katundu pansi pa mipando anthu tiziponda pamenepo…ndipo ali nkuyankhula mopusa conductor…zipitilire zimenez ndithu awone polekera ma driver..anthu tizikhala atatu pampando…kumalawi kuno ena tili nkukwera minbus tisanasambe ndie za anthu anayi zimakwana kuchita kumakhudzana mmapewa ayi ndithu.zisinthe bravo bravo a police

 2. Akuluakulu komanso ang’onoang’ono, chomwe ndachiona pano nchoti , anthu amene amadzitcha anzeru ,omveka ,achuma ndi odziwika m’dziko , amafuna azitipangira timalamulo toti ife amphawi azitisowetsa mtendere basi akatero iwo kumtima mbee!!! . Anthu oterewa alipo ochepa kwambiri ndipo akunama ndi afana sativuta ,2019 tizasankhe anthu ngati awa:
  1 :osauka kwambiri komanso wokhala kumudzi ,chifukwa akhonza kudziwa mmene umphawi umawawira etc ..
  2 :wosaphunsira koma wodziwa kulankhula chingerezi chifukwa ndi chinenero
  3 : mupitilize ndinu kwiko !!! Mpaka no:10

 3. Kod Pamenepa Anthu Aziyendera Abale Ndi Anatsi Awo…? Bcz Akamayenderana Amatenga Kenakake Monga Thumba La Chimanga Kapna Ufa, Nanga Azichita Hire Galimoto Bcz Of Asingle Bag.? Is This True…?

 4. Tsopano munthu wagula thumba la chimanga pa Njuli nde ulisenze mpaka mu Limbe? Mmene dziko lathu lasaukiramo anthu ma transport adziwatenga kuti? Inu kukhala ndi galimoto si onse ali nazo.

 5. Ine ndikupanga support malamulo awa: 1. Azikhala ndi ulemu kwa ma passenger.
  2. Mpando umodzi anthu atatu.
  3. Aziima mmbali mwa nsewu osati zoima mwachisawawa.
  4. Conductor achokemo chifukwa amaiwalitsa ma passingers change.
  Note; awa ma driver akuona ngati ndife ana, za thumba la chimanga atiganizira koma zinazo ndiye akangopanga awamange basi chifukwa mmene amapita kumayeso a ntchito ya driver zonsenzo anazipeza ndipo anavomeleza kuti azasata malamulo.

 6. Minibus isanyamule katundu, lory isanyamule anthu.kodi munthu kuoda katundu wa 30 sauzanda angapange hayara galimoto? Koma boma ili ndilankhanza

 7. Apa tsopano ndingoitana Boko haram ndi Al-shabab iphwanye Malawi ikundiphwetekesa mtima, agalu onse adyera akupanga malamulo amenewa. Ngakhale ku South Africa kochita bwinoko kulibe malamulo awusatana ngati amenewa. Mbuzi zawanthu. Ngozi zikuchitika mmaiko enawazi akumanyamura mathumba achimanga?…..Eeeish musandipyese mtima Agalu Atrafic inu.

 8. apolisi ake ati omwe atemetsa nkhwangwa pamwala?
  momwe akuteromo, akudziwirathu kut zandiwo zapezeka & muona momwe katangale akulire mmisewumu. &
  mkamatenga wapolisi wapamseu, muzionesesa kut galimoto amayidziwa, chifukwa enawa amangodziwa fungo la chamba ndi la mowa basi, kenako maso tong’o pa ndalama.
  wapolisi wanji osadziwa theyala lokutha?
  za malawian hemp basi.

 9. Ine ndati minbus isakhaleso ndi conderctor amene uja amathaso upangisa overload ,amene uja alibemo ntchito mmene muja. Enaso sasamba amanunkha litsilo ,tiyeni tione mmene maiko ena amapangila, komaso ife okwera mini bus tikhale ndi ufulu ngati minibus yapanga overloaded bwanji tizitsika or pakhale number ya apolisi yaulele nkuwauza kuti minbus yomwe takwera yalakwa, mwina zingatithandize ife a Malawi

 10. Koma chomwe muziwe azimba malamulo anuo amveka pamodzi ndi apuresidenti koma yamba mwaona Kaye dziko lake Kaye ndiye mupite maiko omwe akupsnga zimenezi monga Ku South Africa kulibe muthu kutenga chimanga Kumudzi kupita mtauni ife ndi dziko lathu ndiosaka timalimma Kumudzi ndikumatengera mtauni kukokera kuti salale tikulandila tigule Malaya ndiye mukunenezipakuti inu muli ndigalimoto ndi pita wathu yo koma chomwe mudziwe muone dziko Kaye ndi anthu alibe galimoto

 11. Kodi masiku ano malumulo ayamba kupanga ndi a polisi mmalo mwa parliament? ???? Basi 2019 kulibe chisankho cha aphungu popeza ntchito yawo atenga a polisi tidzangolimbana ndi kuwachotsa agogo Peter Muthalika basi

 12. NGATI MWALETSA AMINIBASI KUTENGA KATUNDU KATUNDU PAMODZI NDI MUTHU NAOSO AKAMBAZA AZINYALASO MUTHU YEKHA KATUNDU PANJINGA INA.

 13. Zonsezi kuti zithe boma ligule ma bus akuluakulu ngati a anzathu aku Tz okhala ndi ma boot akuluakulu komanso oyima paliponse. Tikupanga malamulo pamene dziko lathu sitinafike pamayendedwe abwino ma bus akuluakulu ndiochepa .

 14. Ma mininbus akutengabe anthu folofolo pa mpando a Police mkumawadutsa osapanga kanthu. Akati sasintha malamulo akutanthauzanji?

 15. Wapolice wakukondwa Koma boma likukavuka chifukwa miseu,wanozgenge mba police yai or mungapoka,galimoto or mngapoka,makala vingoma kwali ni vichi kuti kuti boma lilemelengepo yai chifukwa ndalama zikuluta,mumathumba so pulikani,ivyo wathu wakudandaula,mkugwila chito na wathu sithani malango,ndilo boma

 16. Mbava zapolice zimenezitu ndiagalutu enieni. . Maiko aanzathu salimbana ndizimenezi ayi.. tapolice takunoti mpofunika kumati tibula pansewupa azitimanga titalakwadi ….. mphuno zawo onse

 17. Pipiiiiiiiiiiii! Vuuuuuu!!!!!!! 5pampando pashamba3 plus matumba,kuminulaso mkosayamba.ogwlaine adzakhala pamsewu pompo kutha kwachaka kut pakamukonde.guys alimaches mndan ndsute chamba

 18. Kunafunika kuganidza bwino anthu mvula ikasowa timakhala ndimapephero opepha mvula Kodi nanga mademo asanachitike anthu apephera mwapadera za ngodzi zikuchitikadzi titaonesa si man bus okha omwe akuchita ngodzi galimoto dzina zikupangaso ngodzi ndye pa ayenera kumenya nkhondo ya satana chifukwa iye akugwira ntchito yake ndipo mene tikukangana iye akuwina tisaiwale kuti Pephero ndichida chachikulu chimene chinga bweretsetso mtendere ndi chikondi mu mdziko

 19. ndaganiza bho maminibus azikoka ma trailer kuti azinyamula katundu wama kasitola awo basi tiwone pamene wopolitsiyo angapedzere mulandu driver kkkkkkk

 20. Kumeneko ndiye timati kupusa,inu munthu thumba uchokera nalo pa BEMBEKE ungapange hayala Galimoto yapedera m’malo mokweza mu mini bus yomwe ndakwerayo.Ndichimodzi modzi apa MUMALANDA MAKALA inunso nkumakaphikira MAKALA OMWEWO OLETSEDWAWO.Zawutsiru basi

 21. komano zingovuta kuti pena boma siliganiza bwino. ziphuphu, panseu sizingathe.
  chomwe likanapanga boma akanaika lamulo loti, milandu wapezeka zokhuzana ndi za panseu, fees itakhazikidwa kukhala 1500 kwacha.
  pamenepo palibe angamakambilane ndi wa traffic mkupanga chinyengo ai, aliyense atha kulipila.
  bvuto ndiloti, mukutchula zi mafee zazikulu mapeto ake polephela kulipila mumangokambilana, chinyengo chachitika, chonchi chinyengo sichingathe, malo motion ndalama zizipita Ku boma basi zikulowa m’atumba atraffc, Iwo mkumasangalala boma mkumasauka kumaafinya anthu ndi misonkho.

 22. Dziko loyendetsedwa ndi osaona malamulo ake amabwera motelomo. Kunakakhala kuti ndiopenya malamulo amapangidwa ku paliyamenti ndi ma MP. MANYAZI INE NDI DZIKO LANGA.

 23. Lamulo ligwire ntchito bravo kwa Police ndi onse amene atengapo gawo popanga lamuloli. Koma chonde ife ma passengers tisaone muma Roadblock minibus kapena bus ikupitirira pa Roadblock kukaima patsogolo Conductor ndi Driver or one of them akutsika kukakuma ndi wapolice kutseli kapena kubwerera mmbuyo kukaonana nda Police. Amene timakwera ma minibus hope you know what I mean.

 24. Taona malamulo ife book la mboni osati timalamuli iti tingokhala masiku 32basi tatha. osadandaula. Zisiya or a police ayiwalaso kuti ayika timalamulo ma bongo

 25. #Mukhwapa zomwe ukunenazi sizowona ayi ndi dziko lamalawi lokha maminibusi ake amanyamula anthu 4to5 mipando muzanyamulanso matumba achimanga momwemo misewu yaka yoipanso maminbusi ake aDubai zopanda balance munseu zikamayenda,kodi umadziwa kuti mamnibusi aDubai maiko ena sowavomela kuyenda maiko awo chifukwa zilibe balance zimachitisa ngozi

  1. Zoona? Ndi dziko la Malawi lokha lomwe anthu amalongezedwa 4 mmipando ya minibus? Tabwerani muzawaone anthu 4-4 ku South Africa. And here minibus driver’s are very naughty than those in Malawi.

  2. Chongofunika kulemekeza malamulo anthu atatu pampando ndi nkhani ya bwino ndithu, komanso pasamakhale wothandizira driver.

  1. Amenewo ndi a speed trap(oyang’ana liwiro la galimoto). Ndi kamera yo,galimoto amaiwonera patali,ndikutulukira komwe isanatulukire

 26. Kod muthamangila kulanga wa minbus bwanji popeza ngoz zikuchuluka mzama galimoto akulu akulu apatu sinnamve zachilango chaoyendesa ma truck police yanyansi ngati sinnayioneko

  1. Malamulo alikwa buses & minibuses,mabus auzidwa kuti asapezeke oyimilila,ndiye inu mukunena ziti ,bus ndizotenga ife anthu pomwe track ndiyakatundu ndiye mkona malamulo akupita kwambili kwa otenga anthu

  2. Moses no ukatelo nawe ukulakwisa coz ngozi ndi ngozi so samayenela kusakha ngoz ya truck ija yapha athu angat ndezasiyana bwanji ndi bus lory yina gudumuka pachichili round about yinapha ndikuvulaza athu angat? So boma likungoyenela kupeza njila zina zabwno zochepesela ngozi coz apa akuphaso ufulu wathu wamba athu ena tili ndi ma business ang’ono ang’ono oti timadalila kut amibus atinyamulile mukuona ngat aziyenda bwanji ndindani angakwanise hire ndimwomwe zithu zavutila pano

  1. Tisanamizane apa, ngozi sizichitika chifukwa choti munthu wanyamula thumba lachimanga, sibwino kulanga a ma minibus okha ngati kuti ngozi zonse zikuchitikazi akupangitsa ndi iwowo, chofunika apa kuti ngozi zichepe akuluakuluwa anayenera kungofufuza mozama zinthu zomwe zimachititsa ngozi pansewu, miyoyo yambiri ikuthera pansewu ndipo si ma minibus okha omwe amapanga ngozi, ma bus akulu akulu, ma truck, ma galimoto ang’ono ang’ono, njinga, ma boat, ndege ngakhalenso ma train akumapanga ngozi

  2. You can’t specifically mention kuti ichi chimachitiza ngozi.Koma zina mwa izo ndizomwe apolisi akunenazi.Every car has capacity ndiye mukaika katundu wambiri mumachitisa kuti mupitilire capacity ya galimoto.Therefore, balance of the car imayamba kuvuta komanso you bring problem to matayala agalimotoyo.Katundu azitenga koma should be of size. Tiyeni timvomere for our safety.

  3. Ofcoz maganizo awili onse ndikugwilizana nawo koma tiyeni tione ngozi zikulu zikulu ziwili zinachitika pakatipa panalibetu ya min bus koma ndikudabwa kut apolice mchimfukwa chani akuthamangila kukapanisha wa min bus yet magamoto ena sananenedwe komanso athu timatha kupita malo osiyana mkukabwela ndithumba lachimanga mundiuza kut tizichita kupanga hire kut atinyamuli thumba limodz ndikugwilizana nazo daisoni kut amangoyenela kuyika muyezo wakatundu bas osati kubanilatu

  4. Anthu mukuunikira za lamulo limodzi bwanji,? Malamulowa sanapangidwe lero ayi ndipo ma driver akuziwa kuti sizachilendo ayi, chomwe achitapo ndikukhwimitsa chilango basi, pa easy gyz, mpando Anthu atatu, ma driver asiyenso mwano oti popanda stage amaima potenga munthu koma wina akapempha kutsikapo amamuyankha zachipongwe ngati size yake

 27. Zoona Anthu kuimilila kuchoķa ku liliongw to mzuzu thus y when accident happen no one can survive I agree with the Malawi police thus good

 28. Ifenso mapassenger tatemetsa chikwanje pamwala sitisintha maganizo tizikwera ma taxi ndi ma lorry tione kt apolice agwira ndani nanga aminibus azinyamula ndani

  1. Koma zokwera 4-4 apopo aganiza bwino, zongoima palioonse aganiza bwino, apolice nd abale athu atiganizira za katundu koma katundu asachuluke kuposa mulingo wa bus, malamulo agwire ntchito basi

 29. kumeneko ndiye kupusa kwa boma la MALAWI aiwala kuti zonsezi sizingatheke omwewo akupanga malamulowo ndi amene angalimbikitse mchitidwe umenewu chifukwa a apolice a pansewu ndi amene azidya ma K5000 akapezeka dalaivala waphwanya limodzi mwa malamulo amenewa zimene sizingabweretse kusintha kuli konse kapena kuchepesa ngozi za pa msewu zimene zikusonyeza kulephela kwawo ndiye mmalo mwake kumapanga malamulo opusa ngati amenewo, lamulo loti minibus isanyamule thumba lachimanga akutanthauza chiyani popeza ma means ama transport tilinawo kwathu kuno ndi ma minibus mmadera ena sikufika bus anthu ambiri amalima kumudzi ndiye akufuna kutenga thumba limodzi la chimanga angakwanitse kupanga hire galimoto? kapena chifukwa choti iwowo ali ndi magalimoto sagwiritsa ntchito bus za anthu ndiye akuona ngati ndi zophweka??? tiyeni tiziganizirana a malawi ngati udindo wanu simukuukwanitsa musachulitse ukali ayi pemphani ena akuthandizeni maganizo kusiyana ndi kupanga zinthu zokomela anthu ochepa mchifukwa chake malawi azakhala osalira chifukwa chofuna kuti anthu akumvereni pogwiritsa ntchito mphamvu, ganizani kawiri anthu asanayambe kuvutika mayendedwe ndi katundu(MALAWI TOGETHER WE CAN DO MORE).

  1. Thumba la chimanga ndi moyo wa munthu chofunika ndi chani abwana! Nanunso ganizani bwino pamenepo chifukwa malamulo sangakomere tonse ayi. Wina akuyenera. kuphinjidwa ndithu pamenepa

  2. ENASON BRIGHT CHAKUNJA bwana ndikukumvani thumba la chimanga ndi moyo chopambana ndi moyo koma pali zinthu zina zikamachitika sikukhala kukonza koma kuononga mchifukwa ndimati boma liyenera kuunikirapo pa nkhani ngati imeneyi inu mukundiuza kuti zonsenzi atamasatila madalaivalawa koma ngozi mkumachitikabe inu munganene kuti vuto mchiyani????? pali ma issues ambiri omwe boma liyenera kutengapo mbali poonesesa kuti zinthu zikuyenda bwino chifukwa ndiyambe kukamba pano mpakana mawa mwachitsanzo ku traffic departiment komweko akumatulutsa ma driving license pamene munthuyo sanapite ku driving school, ndiye munthu malamulo oyendesera galimoto wawatenga kuti???? misewu yathu ndiyolongosoka?????

  3. Ine ndizikwera train ndimatumba anga ambatata basi. Hiyaaaa atikwane nazo ife nanga. Koma nde pasazachitikedi ngozi ina mulibe matumba anthu ndikufa. Apo nde ma demo azayamba

 30. akayambisa ma demo kawiri ofunika muzingowaombela, coz amationongera katundu wathu. zaulesi basi. nanga ma demo mkuononga katundu wa anthu zimagwilizana bwanji? apolisi pliz tazitipherani amenewa

 31. Koma aunikilepo poti driver adzimangidwa coz passenger wanyamula thumba la chimanga pokhapo sizoona makosana bola za atatu pa mpando ndizomveka ndithu

  1. Kkkkk kodi ngozi zachitika masiku amenewa ndi ma minibus angati akhudzidwa? Nanga a Judge anamwalira pa ngozi ya galimoto aja kodi nkhani ndiyoti anasenzetsa matumba mgalimoto? Nanga driver ndi bodyguard wa anduna aja anachita ngozi chifukwa cha over parking nanga ajawa anali akulu a chipani chathuchi anamwalira coz galimoto inachita over parking kapena amachita exceed limit? Thus y timati ngozi meaning chithu chosayembekezereka nde izi sizoti zithetsa ngozi ayi koma amphawife npamene titheee

 32. Nafeso ma dalayivara sitisintha…tatemetsa khasu pamwala kut tipangaso ma demo & next week from MONDAY minibus iliyonse siyenda

 33. Asasinthe Kumene ma driver ndi ma conductor amatitenga okwera minibus ngati akapolo awakhaulitse mwina tingamakwere mwamtendere

 34. Ndipo.i second that mapholisa anthuwa ku Lilongwe kuno a matinyamura ngati matumba a soya. Four four akuti. Koma xodabwitsa ncoti kwe mwini minibus amapititsa za anthu atatu pa mpando.

Comments are closed.