Malonda a ng’ona avuta, ati maliseche ake akumapangila gondolosi

60

A Malawi ndi kutheka tipeza msika wina oti utenge malo a malonda a fodya akuvutavutawa. Mmalo mwa fodya, mwina tizingogulitsa ng’ona za mphongo basi.

Crocodile penis

Malipoti ochokela mu dziko la Egypt ati ng’ona za mu dzikomo zili pachiopsezo pamene anthu ayamba kuzigwila ati ndi cholinga azigulitse.

Malipotiwo ati ng’ona zazimuna ndizo zili pa chiopsezo chachikulu ati chifukwa anthu atchukitsa kuti maliseche a ng’onawo akawasakaniza ndi uchi ndiye kuti basi ndi gondolosi kale, alingati nkhondo ku bedi.

Ndiye ati malonda a ng’onawa afika pa mponda chimela chifukwa alenje a ng’ona amatha kupanga ndalama zoposa K70,000 iwo akagulitsa ng’ona imodzi yokha basi.

Ndipo ati ng’ona zina ena akumagulitsa kunja kwa dziko la Egypt chifukwa anthu ena amaiko ena amagula kuti azikaweta basi monga ena achitila a mphaka ndi agalu.

Share.

60 Comments

  1. Kkkkkk kusawuka ndi mavuto akulu or sibwino. Poti fodya sakuyenda bwino ndiye mukuti ng’ona ndiye zithese mavuto aku Malawi that is not true chifukwa palibe amene amapanga ulimi wa ng’ona m Malawi ndiye boma izakhala busy kusaka ng’ona mu shire kkkk mavuto kwambiri tiyeni tingovomereza kuti zativuta basi

  2. Heee ndie ndimmene ndiidzila ng’onamo tiyeni nazo pano nazo zili mma meeting kukambilana mmene zikuvungileni..ine kumangoonelerako bwaa

  3. Kulamula bvumbwe nkulinga uli ndi nkhuku,ndiye amene angabvomele kuononga moyo wake kung’onazo ndi ndani?. Pa anthu 100 aliwonse mudzapeza kuti olemera ndi mmodzi,ndipo 99 ikhala mitembo .

  4. Komatu ndiye umphawi sizinthu utha kumupengesa misala munthu, Nanga anaganiza bwanji ameneyo kuti ng’ona ingathandize kkkkklkkkkkkl koma ziliko

  5. Ndili nazo zoweta 12 koma aaa zokuphazo nde ayi ndimakagula mitembo kuchipatala yosowa aniwake kukadyetsela ng’ona zanga nde kupha iwe wamalawi 24 ndizakakuponya mudziwe limeneli ukamakamba za bodza

  6. Hello everyone my name Thandi Daniel, I was once an HIV/AIDS patient, but today am negative with the help of Dr Abuu and God who made it possible, i suffered from depression since the day the HIV/AIDS test shows am negative although i was on drugs but i still felt uncomfortable with the unwanted visitor in my body, only those with virus understands the pains, getting a good job was a problem because of my status no friends, i thought it was the end of the world, i was just waiting for my death, i was losing weight rapidly, i was unable to get married as i don’t want to effect an innocent soul or spread the virus, and i have spent a lot money because i was very desperate of doing any thing to get rid of the virus but all effort seems not working to the extent i was conned, until i met Dr Abuu who gave me the chance to be alive today, i told him i would commit suicide if it didn’t worked out because i was tired of living and my death seems to be too far, but he told me not to worry that his medicine has healed a lot of people and it will definitely work for me too, but to me it was just words of mouth, to cut the long story short i was cured after taking his medicine, today am strong and healthy, are you living a positive life like i was before? and you want to be cured from the unwanted virus? if yes contact Dr Abuu on his email address doctorabuu1@gmail.com or you can call or whatsapp him with his number +2348066454364.

%d bloggers like this: