Vakabu yayambilanso: anthu 87 atsekeledwa kamba koyenda usiku

Advertisement
Malawi police

Inu amene mumatamika ndi kuyenda usiku kumati Apolisi anasiya Vakabu samalani. Mukagona mu chitokosi tsiku lina.

Malawi police
Vakabu yayambilanso

Apolisi ku Limbe mu boma la Blantyre, lachitatu anatsekela anthu 87 atawakokolola kamba kopezeka akungoyenda nthawi yosayenela.

Malinga ndi Apolisi, mu Limbe munakhala mukuchoka ma Lipoti ambiri oti anthu achitidwa chipongwe.

“Anthu amadandaula kuti alandidwa ma foni, ena abeledwa ndalama ndinso kusompholedwa zikwama,” atelo a Polisi.

Iwo ati pofuna kukhwimitsa chitetezo, Apolisi anaganiza zoyendako mu tauni ya Limbe ndipo anambwandila anthu amene akuwaganizila kuti amachita za chiwembuzi.

“Tinagwila anthu 87 amene amangoyendayenda mtauni nthawi yosayenela.”

Apolisi ati anthuwo anawapeza ndi mafoni ndi katundu wina amene akuganizilidwa kuti ndi wakuba.