Zativutanso ku Blantyre: Maminibasi sakuyenda, ogwila ntchito akunyanyala

Advertisement

Atadzadzidwa ndinkwiyo kamba kosagwirizana ndimalamulo omwe abweretsa apolisi apansewu, oyendetsa maminibasi mimzinda wa zamalonda wa Blantyre agwirizana kuti lero sagwira ntchito yawo yonyamula anthu mmisewu.

Izi zikutsatira kubwera kwa malamulo atsopano omwe apolisi apansewu abweretsa ndicholinga chofuna kuchepetsa ngozi zomwe sizinasiye malo mudziko muno.

Ma minibasi sakuyenda ku Blantyre. (Image credit : Sharon Chirwa)

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga ndichakuti apolisi apansewuwa alamula kuti galimoto iliyonse yomwe inapangidwira kunyamula anthu, apa tikukamba za maminibasi, isamanyamule katundu wina aliyense kupatula anthu okha.

Izi zakhumudwitsa eniake a magalimotowa omwe anagwirizana kuti lero achita zionetsero pokwiya ndimalamulo omwe abweretsedwawa.

Momwe nthawi imati seveni koloko (7:00) lero mmawa, mmisewu yambiri muzindawu munali chu kufikira tikulankhula pano kaamba la sitilakayi.

Ena mwa oyendetsa maminibasiwa anauza nyuzipepala ino kuti iwo ndi okhumudwa kwambiri ndimalamulo omwe apangidwa ndi apolisi apansewuwa.

Ndipo anati apanga sitilakayi pakufuna kusonyeza kukula kwa mkwiyo wawo pamalamulo atsopanowa.

Kunali chimnabalala Ku Ndirande pomwe oyendetsa maminibasi one anasonkhana ndikuyamba zionetsera pakusonyeza mkwiyo wawo pankhani yamalamulo atsopanoyi.

Muzinda omwe koma kwa Kamba oyendetsa galimotowa anayatsa moto mmphepete mwansewu nawoso kukwiya ndimalamulo atsopanowa.

Padakali pano oyendetsa maminivasi Ku Chilimba mumzinda omwewu agwirizana kuti ngati apolisi apansewuwa sasintha maganizo awo pankhaniyi, anthu kuyambila mawa pa 24 Juni azilipira K500 kuchoka Ku Chirimba kukafika mntawuni ya Blantyre mmalo mwa K150 ndipo opita Ku msika wa Limbe azilipira K700 mmalo mwa K200

Advertisement

352 Comments

  1. Apa zinthu kumalawi zafika posokonekela ine ndimagulitsa maungu ndipo ndimaoda 1.500 thumba kuchekela ku mbulumbuzi ndingapange hayala galimoto muganizepo bwino apapa

  2. I nuyo mkumayelekeza ndi maiko akunja kuno simukuganizira amphawi mzifutsa kaya kwa ife tinayendandapo UK, USA,RSA Nigeria Pakistan ndi maiko wosiyanasiyana ndimaiko olemela mashop nawo pafupipafupi komaso amakweza ma ma 50kgs mumamibasi musamame plz, funso ndilot box nyama 20kgs mpunga 10kgs suger 5kgs bag ya mbambayira 10kgs mchere 2.5kgs tomato 2.5kgs munthu yumozi mumibus.a traffic apa mwanganiza mbwanji ndinkhalamba yanuwo?anthu akumudzi akagula kuti katundu ngati inu mkulesa katundu mumibus?.plz think b4 you do something.

  3. apa sizili bho. dziko lili mmanja mwa agalu, zoona kumati tisamakweze katundu mminibus ndiye tizipanga bwanji osaukafe? kodi ngazi zonsezi zikubwera cz anthu akweza katundu mmaminibus? mmalo mofinya ma driver omwe amaendetsa ataledzera mukulimbana ndizopanda pache! Ngozi zikumachitika olo driver alimo yekha and kutenga 4 pampando sikutanthauza kuti kumabweretsa ngozi. Vuto lolamulidwa ndi Nkhalamba ndilimeneli sangatithandize! mpaka kumati minibus isamaende usiku ndiye nanga kwa anthu omwe amalandira uthenga wazovuta or matenda usiku azidikira kut kuche? ZazIiiiiiiiiiiiii

  4. Eeshshsh…boma lathu ndilankhaza guys. Tsilimaganiza zamavuto akumalawi. Now we’re pyn k800 4m A25 to town wt whch salaries cn aford to py such fare, we nid APM to go around dffrnt companies and see how much r we rcvng per month.

  5. Eshiii amalawinso kusalila. Katundu mukulesawo ukuletelani umphawi cifukwa umaleta makhobili.dzulo nimati nigula zinthu koma ndalama ndinabwelera nazo kuzambia. Am telling u the truth crossing border business imakuletelani makhobili dzedi maka maka lilongwe bwalo lanjonvu ndi malo ena. Dikhilani kwa sabata imodzi chabe zinthu zifika pena .kunoko kuzambia zizingatheke zimenezozo panopa ndikupita Kulusaka kukatenga zikatundu abvutika ndi anthu anu azamalonda

  6. Nkhaniyi tisailowetse ndale ganiziran mmene timakhalira mu min bus muja nde ukhale ndimunthu odwala mphele suitenga???? a malawi nthawi yakwana malamulo ayambe kugwira ntchito tiyeni tikhale mchidwi chomawerenga constitution yathu osati kumangokhalira kutsutsa 3-3 mmipando ili boh nkhaniyi ikukhudza ifeo tikat akuphwanya ufulu wa eni ma bus wa tikunama iwowa ndamene anayamba kutiphwanyira ufulu kalekale potichinyira 4-4 ngat mitembo… Ntchito yabwino a police ipitirire mpaka malamulo onse atidziwika kwa anthu

  7. Osataya nthawi ndikutukwana boma ayi amenewo ndiwo malamulo.Musapange zinthu ngati simukudziwa ayi ngati simukudziwa ndibwino kufusa gays pls olakwisa ndima driver

  8. Amene adatimenyera ufulu dziko lathuli kulibe adapita inu mukutipanga nkhaza bwanji ngat mudava kuwawa during dat tym? Musatitenge ngat zisilu tilinayo mphavu yomenyana nanu. Mukuti ife tikakudyerani kuti sitose tilizintchito za boma ayi timadalira ma business omwewo dziwani kuti malamulo mukuika dziko lathu lino tsiku lina muzalililira dzikoli zinthu zitatembenuka

  9. Boma lopusa
    This policy only benefits the rich minority while the poor majority people are hurt
    Mmalo mothana ndi ama bus mukulimbana ndi aminibus
    Kod ungapite kwa nyezerera opanda kutengako khonyo?
    Mundisamale

  10. Choyamba bomalo likoze kaye miseu ndikumayika bwino malamulo. Komaso osati kungopala ndiye ndikumati akonza minseu. Kwa nzanthu mukambakotu minseu ndiwoneka bwino ndipo akamayika malamulo zomakwanila

  11. Kunena chilungamo kumalawi ndikosauka, and anthu ndi omwe ali ndi ndalama ngakhale ndalama zakeso zimakhala zotibela aphawi tomwefe. Miseu kumalawi ndiyosalongoka akati akoza nseu ndiye kuti apala ndi grader basi akatelo ma radio kusokosa amvekele akoza nseu. Zopusa zokhazokha basi. Ndiye lero aziti osanyamula katundu ma minbus. Enanutu mufela ntchito. Obwletsa lamulowo ali kwawo pheeeeee ndikumakuuzani inuyo amvekele muziwangwila onyamula katundu

  12. Madriver ambili akumalawi ndmbuli that’s yy akupanga zoterozo let’s see kumaiko akwazathu malamuro amene akuwakanawo ndiamene akugwila ntchto kwazathu nde apolisi asakomedwe nd k500 yomwera kachasu kumasekelera zopusazo malamuro agwile ntchto bas

  13. Can we say all these ngozi is because of the careless of the driver I have a different views on this issue I think as s Malawian we need more prayers Satan is at work you punish people without sin again have you improved your roads or have you discipline your corrupt Police personnel’s or have you civic educate the masses about the dangers of overloading in minibuses maybe you have the views that the conductors are forcing the people then I wonder where are the rights of the people you are tolling day in day out I think more work to be done by the government than to pose laws on the shoulder of the drivers and conductors

  14. lamulo labwino kwambili. Ndichinthu chimodziso chimene chawonetsa kuti malawi akuzindikila tsopano. Pamene kalekalelo malawi sankadziwa kuti mubus kapena minibus imakhala ndi limet kanyamulidwe kawanthu.I thanks poti malawi wasukusula izi zichepetsa ngozi zapeseu.

  15. Mukamati ku south africa samakwela ndikatundu dziko lathu mungalifanizile ndi south mukunama ndizimene akuika malamulo kuona ngati ali kwa merica zo zimene kumalawi ndikomvutika atalowe boma akumaba kumabweletsa malamulo owapweteka aphawi tionana 2019

  16. Tayendan mupte mozambique-mu amene mukupanga malamulonu ngt simukakwera limodz ndi mbuz kapena nkhumba minibus…. Nde kuno mukufuna kuzuzaso anthu osauka kalefe ndi half nthumba la chimanga logailidwa ndi azigogo m’mamidzimu zoona agonyete inu??

  17. Vuto ndikulira amalawi ndichifukwatu amakwera 4 4 mtunda Wa pin amati ndiri Ndi 800 makamaka mzuzu nkhata bay eeesh komanso traffic kuba amati kayime pasogolopo olo uli 3 3 NDE amati tachita ukangokana wanyaa makamaka uyu timati ujeni uyu iiii 2am Ali pa nseu at kuzisaka zomwera

  18. To my View..Gvt/apolice akanangopanga regulate pakanyamulidwe kakatundu..osati kuletseratu!!Reason is —
    .1Minbus drivers hold licince named (PG)passanger and goods.
    2ndipo palibe licence named passanger only!!coz opanga malicence knws kut passangers goes with katundu..
    ndipo Ma driver wo amakhala ataphunzira kanyamulidwe ka passanger and goods…
    akanat kumanyamula mwa limit bhola if over loaded must b punished bhola..
    Komanso Every mibus has Buneti komwe anapangirako kutika katundu.. so wat??
    ngat a minbus atapezeka kut ayika katundu pamwamba pa minbus ngant mowe amachiyira ma big Bus itha kukhara case ina…

    Khani yangoz ndiyonvetsad chisoni ndipo zachulukadi…komano malamulo amenewa apelekedwanso kwa ma Big Bus ?? chifukwatu ma Big Bus ndiomwenso akupanga ngoz kwambiri!
    Dont forget kut Galimotozi zimapangidwa ndi malo oyika katundu omwe..komano khani ndikanyamukudwe zomwe zinafunika kungopanga regulate bas osati kuletseratu..
    kod ngat aletseratu anthu tiziyenda opanda kachibinyira kakatundu??

    Gvt/police please Construct misewu yabwino..kut ngoz zichepe b4 imposing some other laws like kuletseratu katundu
    Mosewu yambiri kumalawi ndiyophotchokaphotchoka …kapena kut misewu yambiri ili ndi ma pot holes zomwe zikudzetsanso ngoz kwambiri..
    Poor roads=too much Ngoziii

    Big up!! the owners of minumbuses for such strike..komano khani ndiyoti katundu muzinyamula mwa size kulingana ndi Bunet yanuu

  19. Zangooneselatu kuti ma minbus sakuwafuna mmalawi muno coz si ngozi zonse zimene zikuchitika kamba ka minbus nanga ma galimoto ena ndie awapasa malamulo anji? muganize bwini a # Traffic

  20. Zatipeza mochedwa kwathu kuno kukakhala maiko azathu maminibasi amangonyamura anthu osati ndi katundu yemwe ai .ma mpaka kumbuyo katundu pha!!! Ngozi zireka kumacitika concho .lamiro labwino kwambiri

  21. Kodi inuyo kumakhala kumphunzila kwambiri ?kapena kuzindikila kwambiri? inuyo agogo anu agogo awooo,anayamba apangapo zimenezo? mumazitenga kuti zimalamulo zonyansazi? kodi mwaiwala inu 20 ndi 21 july yaulamuliro wa mtchona wankulu uja? ah ah ah amalawi dzikoli ndilathu tisamangovomela zili zonse,,,,khodzekani lilongwe lachiwili kwatelela muzandivomeleza, nkhani ndiyodana ndi malamulo autsilu.

  22. Xokwera ma bus 4,4 xausilu.Kungokhala ngat dzinyama.Asiyeni apanga strike tione kut ikamatha 3-4 days adya chani makomo awowo.Akapanga xosokoneza katsekeleni ku maula prison.Mumachita kutipakila ngat nkhuku zot zafa kale bwanji.k150 distance ya 2 km simakukwanani.APolice akwidzingeni ose opanga chisokonezo.ma strike awowo adzingokhala ma nyumba shupiti

  23. Apolisi achitabwino kutero komanso sanachite bwino osat malamulo azikomerabe anthu olemera okhaokha basi ife kuno kumudzi tingofa basi ndimavuto palibe chabwino

  24. Ngozi zambirj zikuchitika kwa mabus akuluakulu zapanga affect Bwanji maminbus? bullshit government sionse ali ndimagalimoto mu Malawi. Mukakhala muntengo musamati pansi palibe mame.

  25. Ngozi zambirj zikuchitika kwa mabus akuluakulu zapanga affect Bwanji maminbus? bullshit government sionse ali ndimagalimoto mu Malawi. Mukakhala muntengo musamati pansi palibe mame.

  26. Apapa aboma achita bwino kukhazikisa malamulo amenewa,dziko lathu lakhala lomvesa chisoni kwa mayiko amnzathu mutati mupite ngati ku South Africa simuzapeza munthu atanyamula 50 kgs yachimanga,malata kapena zinthu zolemera kwambiri kukweza mu minibus.Komanso eni ma minibus ngati akufuna kukweza tiwavomeleze kutero mwachisanzo,ulendo wa 150 atauyika 250 kapena 300 bola kusiyana ndi mbwelera zomwe akuyankhulazo

    1. Tikufuna tizikhala momasuka m,mipando komanso capacity ya minibus izikhala yonera tatopa ndikukwera ma minibus ngati matumba

  27. Dziko lakuvutani kuyendesa.kodi malamulo amenewa akuchokera kuti?kapena dzikoli mwalisintha sopano simarawisotu?ufulu mumanena uja uli kuti?musawone ngati tikurankhula morakwika koma zawonjeza.izizi simuwonjezeraso malamulo ammanyumbamu tikamakumana ndi azikazi athuso?Kofi mukuwona ngati ndionse angakwanise kumapanga heyala ngakhale atakhala ndimatumba awiri achimanga?izi ndizo nkhaza.mukuti long parking,5yrs paliso mtendele apa?kapena mukufuna tilibe ndlamafe tingofa!!!!!!?dzikoli tonse tinalipeza ndilamwini namalenga musafike powonjeza chonchi.kwa emwe wayambisa izi chonde chonde nganiso mwawunthu chonde yangana zamawa usawone zalero rokha

  28. palibe chachilendo as long as I know malamulo apansewu..zonsezi zinali prohibited mmbuyo moansemu.the only problem here is that the punishment given is beyond the crime level itself. apa nde its the same as akupha galu aphedweee!!

  29. Another way of perpetuating graft.Whoever came up with this mad cow disease,they very well know that there is no space in our prisons and that just a handful would pay such fines.

    Assuming the driver is fined K150,000 and gives the kapokola K30,000,then thats a windfall for him and his master napping at the station.What a deliberate move.

    An increment from K5000s they used to get to K30,000 will completely _eradicate_ all their poverty.

  30. Malamulowo ndi akale koma ma driver kuderera, or lamba amamanga akaona police koma chomwecho cholinga cha lamba ndikuthandiza iye driver osati police.

  31. KODI MALAMULO NDIMAYESA ACHITIDWA KUNYUMBA YAMALAMULO POLICE ILIBE PHAVU KAYA KUNO TIMAVULALA CHIFUKWA CHOSAZINDIKILA

  32. Kodi mukanyanjala zikupindulirani? Simukuona kuti mukanyamula anthu opitirira muyenso, muchita ngozi kumakha kovuta anthu kuti apulumuke?

    Mvetsetani ndikukambirana, dziwani kuti Boma likufuna kuti anthu asamakhale ndi chiopsezo akakhala paulendo.

    Kunyanyala sikukuthandizaniiiiiii.

  33. koma kunena zoona malamulowa ndi akale, kukwela mini bus tikuziwa kale kuti ndi atatu pa mpando ndipo timaziwa kuti mini bus siloledwa kunyamula katundu ngati chimanga. Nawo amalole akuziwanso kuti sakuyenela kukweza anthu pamwamba pa katundu izi wins aliyense akusowa. Ndiye pano ziyamba kugwira ntchito take, ndipo kuyomika galimoto malo osayenela ndi mulandu inu mukuziwa bwino lomwe. Chomwe mungapemphe mchakuti akulileni kuti muziyenda usiku koma mosamala basi, sizonyenyalazo ndiye ndalama mukatenga kuti mwenzi ukatha mukupanga zimenezi ena ali ndi awo ena ali njinha ayamba kukwela inu mulibe ndalama iwo zawo zikuyenda

  34. Akutinso mai akakhala ndi mwana asakwere minibus ngati afuna ayenera kumulipilira mwanayo, komanso akuti anthu onenepa azikhala awiriawiri pampando bus yimalemedwa kwambiri

  35. Malawi iwe dzuka please aaaaaaa for hw long now u kip on fighting for nonsense …am really tired of dis bullshit for real munthu angayende opanda bag??bombocrat

  36. Ine zoti wapolice kapena soldier angapange malamulo ogwira mutu ndimakaika kwabasi.

    Magulu awiri amenewa : police and soldier malamulo a anthu amenewa amapanga apply as if every one went kuma training awo ausilikali. Mwina malamulo amene akhazikitsawa akhale ma bill to be presented in parliament.

  37. Akufuna Abise khalidwe laziphuphu vuto sikatundu koma kulola galimoto kuenda losakwaninira kuyenda pamseu monga 1 matayala okutha 2 galimoto yopelewela mabrake 3 exceeding, and over speeding. when cruising there is atendancy of weight transfer that can lead to tyre bursting and vehicle instability when decending agradient and vehicle overturning when negotiating a corner. THE BEST SOLUTION ,THE GOVERNMENT SHOULD FORCE SPEED LIMITERS ON PUBLIC TRANSPORT AND CHECKED WEEKLY.

  38. Ine ndikakwela bus kuchoka Ku BT ndimakafika Ku Mangochi choimilira ndiye tamuyang’aneni ameneyu tamusiyani wa minibus kaduka eti

  39. Malawi walero sazatheka mukupanga malamulo mmalo molimbikisa kupemphera aaaaaaah koma agalu awa saganizadi satana akugwira ntchito yake yoononga ndiye the best way ndikupemphera bas komaso the whole nation shud b involved coz ngozi sizingamachitike mowilikiza like this palichinachake chikuchitika so let’s pray hard Malawi

  40. Eish dzosaenda makamaka kwa mwana wa school lero yemwe akulemba mayeso a form 4 koma amaphunzira kutali dairy amakwera min b, apanga bwanji mmmmm dzandikhuza hvy.

  41. Wa Minbus akagwere. More over mawa its weekend and monday Holiday. Tikuonera udya chani ndikunyanyala kwakoko.

  42. Inu mukaimisa minbus kukuuzani kuti yazaza mumadandaula muti simufuna kudikirira INA.
    Pano mukumwaza maganizo oti asamakupakireni moonjeza .
    Sitizatheka ife

  43. Amalawi tyeni tzganiza pamseu ngoz zachuluka mukt apolisi sakugwira ntchto…pano apolis akhwimise chtetezo mukut apolis nd zitsru mumafna chani

  44. kod akupanga ngoz ndi ma minibus okha? mundfunsileko a traffick kuganiza kosathandiza kumeneko.ngat ma public transport they are involving themselves in accidents nde pali zabwino. look for other measures. nde ngat anthu akulephera kukagwira ntchito will the nation develop??? think twice!!!

    1. am agree with you ask them

      Ndipo Ma Big bus akuchitanso ngoz kwambir…meaning kut ma Big bus aletsanso kunyamulankatundu??
      hw ppl can travel without Bags??
      Ndipo ma small cars akupanganso Ngoz heavy reason yayikulu ndiyakut with hav poor Road with alot of pot holes..hw can gvt ecpectd teduction of accidents??..constract good roads 1st

    2. Werenganinso malamulo aperekedwawp.Galimoto yaying’ono yakhuzidwa -iyo ndiye palibe kulipira koma kungopitiratu kundende; basi yayikulu, minibasi;mwachidule tingoti palibe galimoto yomwe siyinakhuzidwe.

  45. Kuyakhula monyoza pachimene apanga amaminbus ndikusazindikila muuzimu ndithu ndiposo kwayinu amene munapeza chuma chapasi panyajanu mwayeneladi kunyoza aphawife ndipo ndikupepha mulungu wanuyo akuwonjezeleni chuma chambili kmaso moyo wautali ngat angatheso kupeleka moyo zikoma malo mwa onse okwela ma minbus osati oyendera galimoto yawo

  46. Zikomo kwambiri apolice popeleka lamulo limeneli! Anthu ama minibus saganizila miyoyo yawanthu, amazadzisa kwambiri, komanso lamulo limeneli mupelekenso Kuma bus

  47. Ama Minbus amaonjeza achita bwino opanga malamuloyo anaganizapo bola zipitilire akapezeka akamusekere kumene. Akapezeka wa policenso akupanga ziphuphu amusekere tatopa kukhala pa thumba ma minbus mu

  48. Boma lamalawi ndilupusa kobasi kale lonse lija samaziwa kut mmabus ndi mmaminbus mmakhala mlingo kapena number yonyamulira anthu lero zachitika ndipomwe akupang demand anthuwa lero sakugwirizana nazo kamba iwo anazolowera zoipazo

  49. As of now mbuzi zina zaphwanya police unit kuzomba (chinamwali police unit) akut kukwiya shame @ those people kungofuna kuzunzitsa mawanja awo

  50. Kulemba nkhanitu mwantopola uku police amabweretsa malamulo? Law enforcement is not is not formulating laws! Kawerengenso nkulu!

  51. Apo a Police aganiza bwino kwambiri coz minibus siyenela kunyamula katundu ngat momwe amanyamulira akapolo amenewa,sikatundu ekha amatikwezanso mothinana m’malo mwa atatu pampando kumanyamula 4 pena mpaka 5 nde ngat simukufuna basi kapangeni park kunyumba kwanu olo apa biiii mudzikwera ndi azibale anu coz mitengo mwakhazikitsayo zikuoneka kut mwapenga misala mitu yanu yasiya kugwila ntchito.

    1. Mr Abas kagwereni uko…kkkk.malamulowo salibwino reason ndiyakut palibe livince named passanger(p) only wat i knw Minbus Drivers hold (PG)passanger and goods
      komanso uwawauze apolice woo achotse ma Bunet akatundu omwe minibus iliyonse imapezeka nayo…

      khani yangoz ndiyonvetsa chisoni
      nde chomwe apolice akanapa ndikupanga regulate mapakilidwe akatundu osati kuletseratu.
      Ndipo iwe innocent do you knw kut ma Big Bus nawo amanyamula katundu??….ndetu apolice aletsenso ma big bus chifuka ma Bus nde akuchitanso ngozi kwambiri..ndipo khani yangozi imabwera munjira zambir ..1 ndi poor roads …too much pot holes zimisewu zakumalawi..

      nde uwawuze apolice ayambe anangakaye miseeu yabwino b4 everything imposed

    2. Inu ama minibus ndi akuba nkhani ya zonyamula katundu ndi kukweza ndi ma passanger sizikugwirizana nde palibe rizon yokwzela mitengo Zakanyamulidwe katundu akanakambilana ndi abomawo osat kukweza mtengo nde zachamba ndukanazo zinenezo.

    3. Zamitengozo ndizachambad koma sinanga apangira kuwawidwa…..
      4 that i cant agree with dem
      koma inuyo mumat achita bwino kuwaletsa kunyamula katutundu which z not fair..chifukwa we cant travel without bags..or kachibinyira

      ndipo upeza kut Ma bus akuluakulu sanaletsedwe which z not fair again..chifukwa ma bus akuluakulu omwe amakhulupilira ndiomwe akuchita ngoz kwambiri nde uzifunse

      here z Mathematics..kkkk
      Poor roads + Drink and Drive=Ngozi
      thats main reason
      zakatunduzo nditi minor reasons

      nde uliwuze bhoma limange misewu komanso lizimanga ma Driver omwamowa

  52. zawo tiziyenda wapasi akudana ndichulungamo bwanj? ngat akufuna agule magalimoto oyenera kunyamula athu 4-4 osat zinazi ayi ….. well done Road-Traffic osawagonjera athu amenewa

  53. You can say many things against police on this issue but at the end lives will be saved. When something new comes,society tends to be resistant I don’t know why. Let’s see positiveness before we look at negative side.

    1. Iwe ndiwopusa aise…. Ngoz ndi ngoz u cant avoid.. Palibe postv measure apa wat we kno price will be high n yet were alrdy up. Boardguard & driver wa minster anapangaxo exced?

  54. Amalamulo apanseu musasokoneze ana akulemba mayeso komanso abusiness fe tiri ndi maudindo ganizani mofatsa zaka zonsezi munali kt enafe timalima kumudzi maulendo amakhala osiyanasiyana

  55. malamulo ena ndiautsiru munthu ungamapite ulendo opanda katundu?that’s stupit ngati iwowo ali ndi magalimoto ife timakwera minbus nde tidzikanika kukweza chimanga tidzikadya kwao?

  56. Amamini bus samapeleka ulemu kwa passenger awo,Umachuluka ndi mwano.Apolice ngwilani ntchito yanu.Ankhaule amaiwala kuti Analembedwa ntchito.

  57. Hahaha lamulo logwila ntchito tsiku limozi lokha. Adya Chan apolice, a roadtraffic akapanda kupanga ziphuphu? Dikilani muone plan B yochokela ku likulu komko lofuna kudyela anthu.

  58. Ndizoona zake zimenezi,taganizani 4-4 mpando umodzi ena osasambanso pomwepo monga ma conductor.Chilichonse chimakhala ndi mulingo.Aliyensedi opezeka azimagwidwa palibe kunyengelerana anthu amafa atalipira maminibusiwo.Kumaganizo kwanga zaka komanso fines zachepa,makamaka akamayendetsa atamwa mowa ngakhale asazayendeseso galimoto moyo wake onse komanso kundende zaka 50.NGOZI ZAMBIRI ZOMWE ZIMACHITIKA,ZIMACHITIKA CHIFUKWA CHOSASAMALA.

  59. muzangopwetekedwa za zii,,lamulo silimaposa mphamvu,,inu mukumva kupweteka bwanji?mwazolowera kutichinyila four four,conductor akutinunkhisa kunkhapwa ndimkamwa mosasuka,,pangani ma demo mukamaliza mutiuza

  60. kkkkkk waminbus ndilibe nayo vuto olo atanyamula 5/5 but i hate wa bus amanyamula anthu choimilila from LL up to BT munthu kutopa paka kupolama osayakhulapo pot ma bus ambili ndi amabwana et osapezelela amamin bus ama bus akuzuza anthu hevy kumakwela bus 8am kunyamuka 4pm zosez simaona mukoze ma bus kaye …….

  61. mumatiuza tisamakwere minibus t tizikwera bus yet ma bus ndiomwe akupha anthu this is silly Malawi grow up lija ndikale nanu akulu akulu assosiation come muzaone how maiko ena momwe amapangira pa nkhani zama taxi kufuna kubela wanthu basi

  62. Anthu ena mulibe umunthu,,,inu ngati muli ndi galimoto kwanu what you can do is to thank God kuti muli ndi mayendedwe anu,,izi zikhonza kutheka kumutamanda iye ngati galimoto lanulo munalipeza mu njira yoyenera koma ngati sichoncho NYOZANI a ma minbus pakuti iwowo ndi amene akuimilira amphawife

    Ndipo malamulo amenewa sakhuza a ma minbus okha komanso ife anthu okwera

    Think when your phokonyore get break down mukamakagula ma parts mumakwera chani? Mudzapeza kuti ndi minbus

    Mungotamika pano kumanyoza ma min bus koma muli andiphule ndi pume asapengwa okugwa ndi kumina amkanda patuwe ngati ine

    INE NGATI MNZIKA YA MALAWI IZI ZOKHA ZAFIKAPO NDIPO EISH KAYA

    1. Pakufunika muimvetse fundoyi man , sizoti akuletsa a maminbus kuti asamayende ayi koma zinyamula anthu ndi katundu nde zokanidwa zimenezo and minbus ndiyonyamula anthu not katundu

    2. Mponda,chili kwa nzako usamati chigwire nyanga,koma ndiwe mmalawi nzanga iwe?Chabwino amphawife tiziyenda bwanji ndi umphawi wathuwu?For instance munthu ukuchokera kumudzi watengako thumba la chimanga ayendenawo bwanji ameneyi?

    3. Ife tikwere min-bus katundu akwere mu lorry,,pakutinso lorry imaloredwa kunyamula katundu yekha koma anthu ai,,ndiye ndi umphawi uli kwathu kuno zitheka izi?

      Pena pake tizitha kumaganiza tisanaombere m’manja zilizonse pls

    4. Man katundu ndi athu sizikuyenela kukwela galimoto imodzi mukamapanga maulendo anuwo muziwe kuti osayenda ndi matumba aufa olo mbatata

  63. EEYA NDIZONA ZAFIKA POOOHYA UKATENGA ANHTU OCHULUKILAPO UMAYENDA ULI CHEUCHEU NGATI WANYAMULA CHAMBA KAPENA WABA KUOPA POLICE. APATU AKUNGOPANGISA ANTHU KUTI AZITUKWANISA MSOGOLELI POMWE MSOGOLELI SAZIWA CHILICHONSE. CHONDE MA TRAFFIC MAN MUSAPANGISE MSOGOLELI WA ZIKO KUNYOZEDWA KAMBA KONGOFUNA KUZIKUNDIKILA CHUMA MWA INU NOKHA CHONDE TAPOTA NANU. MALANGIZO KU BOMA. ABOMA LOLANI ANTHU AZIKWELA 4 4 PAMPANDO AZIGWILA LONG PARK NDI KATUNDU OOOCHULUKA OSATI PANG’ONO AI. MUKAZUNZA MA DRIVER MINIBUS KU 2019 KU, ZIZAVUTA MUSAVOMELEZE APOLISI KUTILANGILAYU PANSIPANO. TONSE TIKUYEMBEKEZELA KUZAWELUZIDWA NGATI TIZAPEZEKA TITACHITA BWINO, BWANJI TIZILAPILATU.

  64. Samalani Katundu Akataika Sitibweza,, Mukapeleka 2 Thousand Muchedwa Nokha,, Driver Akaima Osamufuxa Kt Akudikira Chan Amakhala Akudikira Athu Hahahahahaha Lero Kulibe Zmenezo

  65. *Kwa ma Minibus driver ndi conductor malamulo atsopano ali motere:* *(a) osakweza thumba la chimanga kapena katundu mini bus opezeka azilipila mlandu wa 20,000 MK kapena kukagwira ukaidi wa zaka zisanu mogawana Driver ndi Conductor.* *(a) Osakweza anthu 4-4 mmipando kupezeka otero azazengedwa mlandu zaka 5 aliyense kapena 150,000 MK mogawana.* *(c) Wrong parking 20,000 MK kapena 5 yrs kundende izi zabwera kamba kochuluka kwa ngozi Mmalawi muno.* *(d) Bus isayende usiku yopezeka mlandu 200,000 fine.* *(e) Musapezeke oima mu basi kupezeka oima mlandu 200,000 MK kapena driver and conductor ku ndende 10 years.*

  66. A police achita bwino pokhazikisa malamulo a new pa nseu ngozi zimachukuka due negligence of the drivers of which innocent people lost their life’s

    1. zoona m’bale ngawa umphawi uli ku malawi kuno munthu ungakwanise kupanga Hire Galimoto chifukwa cha 50kg ya cement zoona? azathu ngati muli ochita bwino koma ganizilani amphawi ndithu.

    2. @ Francis E. Mpelula iweso akukhuze kuti uzindikire kut mulungu sakondwera ndi infa ya munthu olungama chifukwa choti wina wake akufuna ndalama a lot of people are dying due road accident and yet u r agreeing kuti ma bongo high roof etc azipakira anthu 4 per seat how dell are you think twice brother kukumana ndi mavuto doesn’t mean its tha end ov life koma anthu amene akufawo akusiya ana of which iwe sungawathandize uzaziona akaxakhala mmbale wako

  67. Lelo simukugwira ntchito eti mukamaliza kuyatsa moto muganize nso sopusa zimene mumapanga kutichinyika mutima vannett tanu takalekale against our will. Four four bamipando ngati timatanuka timavanett tanuto

    1. Kkkkkk ineso ndiyambisa yanga strike ngati winiko. akatiphachila kena kuonjezela matumba amatemba, anyezi ndizina zotelo mafungo ambiri mbiri

  68. Ife kale timayenda wapansi kukafika mozambiqui ndiye inu ana amasiku ano ankhuku zachizungunu muziona phuzirani ufiti muziuluka basi

  69. For sure min bus siyonyamula katundu koma anthu unless atamangilira kangolo kumbuyo azinyamule ngati sakufuna ayisova… Misewum tikuvutika kwambili … Yonyamula katundu ndi ya magalimoto amarore

  70. POLICE simapanga Malamulo koma anzathu awa timawavotera kupita ku nyumba ya Malamulo,zonsezi zinalipo kale ndipo panopa akungokumbutsa chabe,palibe minibus driver wa permanent,ukanyanyala upuza ndani?nzako abwera ndipo bwana wakoyo amulembanso ntchito!!Mukulufalitsatu zabodza apa atolankhanir inu,you are not abiding to your ethics of journalism!Tell Malawi the truth osati zabodza ayi,kunyamula katundu saletsa koma mumaonjedza a minibus!!

  71. amene mukudana ndi a ma Minbus mulibe nzeru,, tsopano munthu aziyenda opanda katundu?? U think aliyense angakwanitse kupanga hire,, bola apolisi angonena za exceeding kapena wrong parking Koma zakatunduzo eeeeh enafenso tivutika nsaname

    1. south africa yake it? yomwe tax sitenga katunduyo kumanama bwino luggage umakweza mu minibus zikakhala zambili u wait yomwe ili ndi trailer osanamiza anthu apa

    2. Ngati munakhalako ku south Africa muyenda ma short distance mwina mchifukwa simawona anthu mu minbus ndikatundu koma most minbus oti akuyenda long distance obvious katundu amanyamula nde zinazi osamangoti ku south Africa sizichitika poti inuyo simunaziwone kulibe minbus yoti singanyamule katundu koma amadana ndi overload

    3. pali ndi katundu wake akuluakulu just imagine ma mini bus ochokera kwa bvumbwe kupita kulimbe amadzadza ndi zimatsaka za ndiwo za masamba okhaokha momwemo muli ma passengers ena akupita mudzintchito zotsiyanatsiyana ,mwini katundu akukhala pa mpando chithumba chake pa miyendo

    4. Ifenso tili kuno ku South Africa i have lived both in Jozi and Cape Town for a long time timakweza katundu mu tax(min bus),timagulaso mipando so don’t deceive people

    5. Tonse ndife osauka,koma Galimoto ikanyamula Katundu opyola muyezo imathawa balance,chitseko cha minibus chakumbuyo or ma window amene akatsekulidwa angapo mphepo imalowa ija imathawitsa balance ndiye osamangotukwana cholinga ndikuteteza miyoyo yathu.Zikomo

    6. Nazir palibe watukwana apa and zomwe nkudandaula ine ndizoti akuchita kukaniza thumba limodzi lomwe,,, anthu enanu simukudziwa mmene zikutiwawila coz u have ur own cars

    7. Penapake bomali ndikulimvetsa coz tangoganizani mmene imadzadzira tax ma condactor kumatulukira panja komanso tax ikuthamanga kwambiri sizikhala bwino ndye mmm lamulo ligwire ntchito basi. Mukanena za kuno ku SA musafanizire ndi malawi ku malawi munthu sangalole kugula mpando kt aikepo katundu.

  72. Malamulo aku malawi, odikira kut pafe anthu kaye nkuyamba kuwagwiritsa ntchito, after sometime, we r goin back to the same bullshit, wat nonsense and waste of tym!!!

    1. Malamulo agwire ntchito basi, msonkho amakhoma wa anthu 3-3 koma iwo amafuna 4-4, akafuna kunyamula munthu kuima paliponse koma akamafuna kuti wina atsike amati palibe stage, ndibwino ngati palibe stage malamulo agwire ntchito

  73. Bravo Road Traffic anthu awa amatipachira ngat matumba ife. Tikati tilankhuleko chipongwe chokhachoka chomwe timayankhidwa

  74. Ngozi zambiri zomwe zachitika pakatipa panalibe ya mini bus. Ma private cars, big buses ndi ms lorry. So a ma minibus alakwa chani? Munthu amayenda wopanda katundu? Tinene chilungamo ma minibus ali ndi zofooka zawo koma amathandiza kwambiri. Enanu mukulankhula mowanyoza chifukwa mumayendela njinga minibus simukuyidziwa. Munthu wina amachoka ku Machinjiri pa mini bus to work ku Blantyre everyday ndiye angatani pamenepa? Mukunyozanu muli ndi ma tax omwe azikamutenga pa mtengo wotchipha?

    1. Its not only about accidents, koma anthuwa salemekeza ufulu wama passengers amangomunyengera nthawi yokwera akakwera basi amakhala galu

    2. Koma mpaka tizilephera kutenga thumba lachimanga ku mudzi kuopa kuti atilanda apolisi munseumu. Zausilu zimenezo. Mfundo imeneyo aganizepo mofasa akulakwa

    3. Sionse amene salemekeza the problem of one u can not acuse all,and more over there are some amakananso kunyamula katundu mminbus zawo.ngati munakumana nazo ndiyomwe munakwela inuyo.

    4. Sikuti aletsa ma min bus kut asamayende what is that they have to follow rules pa nseu sometimes passengers amaoneka ngati zitsiru ma driver kumakhoma ma min bus ngati kut atenga matumba achimanga what they want is capacity, car has to be proved that it is fit to carry passangers & driver akhale ndi zomuenereza kukhala driver moyo ndi mpamba mind u not zomwe ukinenaza

    5. Ine ndikaona kuti minibus yadzadza koma akufunabe kuti ndikwele sindimakwela. Ndimadikila yina, ndakwelayonso ngati akufuna atenge munthu tifinyane sindimalola. Ndimawauza kuli bwino andibwezele ndalama zanga. And that is here ku SA. Ndiye zimakukanikani bwanji anthu oti mumamvananawo chilankhulo. Ndi inu nomwe ma passenger amene mumawalimbikisa chifukwa mmalo mopangana kuti sitilola kuti utenge anthu ena muno pamapezeka ena amati it’s ok ndachedwa ine bola ndikafike. Don’t blame them, blame yourselves.

  75. Enanu mukunyoza amaminibus as if kwanu konse muli ndigalimoto zanuzanu muganizire anzanu omwe amadakira minibus popanga business even kupita kuxul&kuntchito even apolice ambiri amadalira minibus zomwezo ndiye mukuona ngati avutike ndi waminibus yekha?????

    1. Olo atasiya kuyenda palibe angadandaule ntchito chimodzimodzi,,athu achipongwe amenewa..walipila nkukupolamilaso pakamwa nkhani yake anthu 4,

  76. Akhale sapeleka ulemu amaminibus. Apolisi khwimisani malamulowo, wapolisi amene apange zibwana waona polekela. Amaminibus atitopesa ngozi pano sinkhani.

    1. Tikuti ulemu alibe amaminibus chikondi chimakhalapo pokwera koma potsika ngati ulibe mphamvu akusiya utavulala kapena kachikwama kako katangambika. Kodi pakona pamakhala pamene munthu akutsika koma pokwera sipakona? Ngakhale utaima pa bridge ndikuimitsa amaima ngati apolisi ali kutali. Ndiye ife zatikwana apanidwe basi

    2. Guys ngozi ndi thawi even Angodana ndi a Ma Minbus Pomwe kuti muonesese akugwa NDE ndi Ma Bus awowo Ndi ma Minbus zikugwirizana bwanji !!!?Apapa sitimayenda Boma lo ndilimene litakhoxe mayendedwe basi

    3. kodi tinene kuti mamini bus amapanga ngozi chifukwa chonyamula katundu ndi anthu four-four,,,,,nanga bwanji nawo ma bus akutembenuzika,,,,,nthawi ya ngozi ndi nthawi yangozi,,,,ngati boma zithu xikuwakanika avomereze basi,,,,satana ndi amene wakula dziko lathuli,,,,tiyeni tiliyike mapemphero osati kulimbana ndi kukangana zopanda mphindu,,,,,kuti mufufuze ngozi zomwe zachitika miyezi imeneyi mupeza kuti ndi mabus ndi matruck,,,,,

    1. Kkkk sorry mukamwe mankhwala mukafika man ma distance a town amaoneka ngat ndi afupi ukakwera minbus koma eeh ndi atali ine mnayendapo kuchoka ku cholomoni kufika ku limbe mwadala ndimaonana ngat mpafupi nditabwera kozacheza kwa brother wanga ndiye lunzu to limbe its not a joke kkk

    1. EMANUEL INE SINZAKO KAYA UMADYA CHAMBA APOLICE SAPANGA MALAMULO ADZIKO KOMA KU PARIAMENT. UNGANDIUZE CHIYANI IWE MBUZI YA MUNTHU. NGOZI NGAKHALE APOLICE AMAPANGA WENA SIWAJA WAGWETSA GALIMO KAYA NDI WEEK YATHAYI.

    2. Afufuze cheni cheni chikuyambitsa ngozi monga akadaulo pakufufuza nanga tichite kuwauza zifukwa zina zodziwikilatuzi

Comments are closed.