Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) a Richard Msowoya ati iwo alibe mantha aliwose kuti a Sidick Mia abwera poyera ndikutsimikiza kuti akapikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri pa komveshoni yomwe ikubwera posachedwapa.

A Msowoya omweso ndi mtsogoleri woyang’anira zoyankhula mnyumba ya malamulo mdziko muno ati palibe chifukwa ndichimodzi chomwe kuti iwo achitile mantha ndikubwera poyera kwa a Mia.
Iwo omwe amalankhula pa msonkhano wa ndale lamulungu lapitali pa 18 June Ku Chintheche m’boma la Nkhatabay anena kuti komveshoni yokha ndiyomwe ikasiyanitse pakati pa mzibambo ndi mnyamata ndipo ati palibe chochititsa manjenje.
Sipikalayu wati anthu akuyenera kudzasankha mwanzeru kwambiri koopa kudzakhumudwitsidwa patsogolo atapanga chisankho cholakwika posankha mtsogoleri wopamba maso mphenya abwino.
“Komveshoni yokha ndiyomwe ingadzagamule koma kusamalitsa kuyenela kukhalapo kuopa kudzakhumudwa. Amzanga okonda MCP akuenera kudziwa kuti ndalama yachitsulo monga K5 imapanga pkhokoso kwambri ikaponyedwa m’mbale ya chitsulo kusiyana ndi ndalama monga K2000 yapepala yomwe siimapanga phokoso.
Nde mutakhala mwapatsidwa mwayi osakha, inu mungasankhe iti pandalama ziwirizi? Munthu atha kukhala wankulu ndiposo atha kumalota zabwino koma palibe yemwe angadzisankhe ndikudziika yekha paudindo malingana ndi malamulo oyendetsera chipani” anatelo a Msowoya
A Msowoya anapitiliza kuti iwo atumikila bwino mumchipanichi modzipereka komaso mosakondera choncho sakuona chifukwa choti iwo azidera nkhawa kamba koti a Mia akufuna kukapikisana nawo pa komveshoni.
Komveshoni ya MCP idzachitika my July chaka chino ngati sipangakhale kusintha potengera kuti mchipanichi mikangano siikumakata.
Latest vacancies
60 thoughts on “Sindikutekeseka ndi a Mia – Msowoya”
Comments are closed.









Southern region tatenga basi mpando wa vice presedent mcp inafa kumwela mia more fire pano chikwawa south ndi mkombedzi mps 2019 mwatenga kale mcp
Iyo Nde Ndaliyo
Zayambika
talodzedwan a congress vp wanu akhale mia muzakhale panamba 3 muwone
pa 2 paja mumakhalapo chfukwa cha combination ya central and north nde mtayen msowoyayo u will c fireee!!!
Anthu wonse omwe amasatila MCP adziwe kuti mwazi wa anthu omwe anaphedwa ku mwanza aja mwazi ulipamutu pawo nduna ndi aphungu aja Arron Gadama, Dick matenje, Twayimbo sangala
Akumbutseni Malaume mwina anaiwala
ife tinali tisanabadwe koma za pa 20 july zija tidazionera tokha zahistoryzo ndizanu ife tidzavoterabe Dr laz
km agogo angawa anal alipo nde tkakhuta amandlongosoler mwaphephe
two cards to apregnat wowan.
#MCP sichipani choti changakupitiseni kutsogolo kuzawina ayi #MCP inapita ndimwini waka Kamuzu mufunse Jz Tembo, ndi Kamphulusa akuzani
watekeseka kale!!
Indeed convention will deside let’s welcome mia
NDIZOONA KUTI SIUNGATEKESEKE KOMA CHIMATEKESEKA NDICHIPANI MUMULOWA LIBOLONJE KENAKA ALIYENSE AMATEKESEKA CHENJELANI
kkkkkk kukangana ndikukangana konseko coz ov our vote muzanya nayo siku lina
He iz sheet man
kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkk inetu si vote yanu ohoooo musadalire
nde mumati anafe nditsogolo lamawa, mawa lake lidzafika liti? Zausilu
Zongonena pakamwa ndicholinga chofuna ma vote athu basiii!!!!
eeeeh anthuwa ndichimodzimodzi thats y Malawi sakutukuka
Ineso sindikutekeseka wamva Malawi 24.
A Msowoya ndi munthu wodekha timawakonda
Mia lake ndidyela
Mmmmm iwe mia sukumudzia
Sakumudziwa Ndimwana
I wud luv zitadzakhala chonchi, Presidenr = Dr Laz, Vice = Mia, Speaker = Msowoya
thats the way to go
ku mcp kumeneko et ok ndmayesa ngt ku malawi2
Enock if u dont wish/dream then its ur prob
Kungolankhula Kokhako Yamutekesa Moyo Kkkkk Akudziwa Kuti Yalakwa
Sidik Mia is a selfish politian who just want to bring confusion in mcp … looking at how he said during interview that he wants to help in politics but not as an MP but higher position
Kukokomeza nkhani nanu olemba nkhani inu.