Neba sizikuyenda: 1 pa 6 kwa Bullets, 6 pa 6 kwa Noma


Be Forward Wanderers

Timu ya mpira wa miyendo Nyasa Big Bullets ikupitilirabe kusachita bwino mu TNM super league pomwe yakwanitsa kutenga point imodzi yokha mchigawo chapakati mumasewelo awiri.

Bullets idalephera kugonjetsa timu ya Blue Eagles pa Bwalo la Nankhaka loweruka lapitali mu mzinda wa Lilongwe ndi chigoli chimodzi kwa chilowele.

Be Forward Wanderers
Be Forward Wanderers zawo zikuyenda.

Timu yafukoyi ikuoneka ngati sidapezebe njira yokhazikika yowinila italepherana ndi timu ya Master Security imene yangolowa kumene mu ligiyi posagonjetsana chigoli chilichonse pa bwalo la masewelo lalikulu mu mzinda wa Dedza.

Pa masewelo awo asanu ndi awili amene anyamata a Nswazurimo Ramadhan asewela akwanitsa kupeza ma points khumi ndi imodzi zomwe zikuwaika panambala yachitatu pa ndandanda wama team mmene akuchitila mu league yaikulu mdziko munoyi.

Bullets ikutsatanatsatana ndi timu ya Wizards yomweso ili ndi maponits khumi ndi imodzi ngakhaleso yasewela ma game asanu ndi imodzi.

Neba wa Bullets, Be forward Wanderers yamwetsa ochemelera ake wankaka mathelo omwe Bullets yawona zowawayi itakwanitsa kutenga ma points onse asanu ndi imodzi chigawo chapakati zomwe zapangitsa team imeneyi kukhala pa nambala yachiwili pa mndandanda wa ma team a mu ligi wa.

Manoma ali pa chikondwelero chifukwa yakwanitsa kupambana masewelo anayi omwe ansewela. Manoma ikufanana mapoints ndi mikango yaku Zomba, Red Lions yomwe ili pamwamba pa TNM koma yasewela masewelo asanu ndi imodzi.

Padakali pano ma team atatu okha ndi amene asewela masewelo asanu ndi awili ndipo Big Bullets ili mguluri.

Umu ndimmene mateam achitila mathelo asabata yapitayi: Loweluka Silver strikers yagonjetsa timu ya Chitipa united ndi zigoli kwa chilowele, Azam Tigers ndi Blantyre United agawana point atalephelana zigoli zitatu aliyense, Bullets idaluza kwa Blue Eagles ndi chigoli chimodzi kwa palibe, Manoma idapambadza Dwangwa United ndi chigoli chimodzi kwa palibe ndipo team ya Kamuzu Barracks idagawana point ndi team ya Civo Sporting Club atagoetsana chigoli chimodzi chimodzi.

Lamulungu timu ya Manoma idapitiliza kudzodza mateam zigoli pomwe idagonjetsa asilikali aku Zomba ndi zigoli zitatu kwa chilowele, Bullets idalepherana ndi Masters Security posagoletsana chigoli chilichonse.

Masewelo a Silver Strikers ndi Moyale Barracks adaliso opanda zigoli.

Latest vacancies

126 thoughts on “Neba sizikuyenda: 1 pa 6 kwa Bullets, 6 pa 6 kwa Noma”

  1. Ine ndinaziwa kuti anawapatsa mateam angono * 2aja kuopetsa kumenyedwa kwa akulu akulu komanso coach. Ndiye musadabwe akamachinyidwa chifukwa kwasala ziphona zokha aziona Neba.

  2. NEBA ANGODYA UDZU UDZUWAKENSO OUMA KKKKKKKKKLKK KUMPOTO WANI NANGA PAKATI WANI POINT KKKKKKKKKKKKK TEAM YA WANTHU YATHA NGATI MAKATANI PANO ATI YAKAMPANI KUTHA KKKKKKKKKKKKKLKKKKKKKKKKKKKJKK

  3. likakhala kale kwa amene tinkautsata mpirafe mkumakaona chatoma kustadium konko_tinkati bullets nkumadzulo.Charles Kafatia ndinzake uja akadziwa kt apa zada ankangopeleka penate^3kick^red card^mpaka zitheke pakavuta ikhale draw.moti kunena kwa zoona ma ligi onse 11 enieni ndi 8 atatuwa..uyu wakherere anatengako gawo powinitsa magame ena.carlsberg kt akhumudwe sponsor analinso yemweyu wakherere …lina mwa gwelo la ziwawa karelo linali limenelo

Comments are closed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading