Ayamba kale kunjenjemela: a Chakwera athamangila ku Khoti kuti alepheletse konveshoni

65

Mkangano mu chipani cha Kongelesi wafika pamponda chimera.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Kongelesi, a Lazarus Chakwera atenga chiletso chokaniza kuti kusakhale msonkhano waukulu wa chipanichi umene ayitanitsa a Gustave Kaliwo.

Lazarus Chakwera

A Chakwera atenga chiletso cha msonkhano waukulu.

A Kaliwo ndi mlembi wamkulu wa chipanichi ndipo analengeza kuti mwezi wa mawa kukhala msonkhano waukulu wa chipanichi.

Iwo anati msonkhano umenewu uyitanitsidwa pofuna kulongosola mavuto amene ali mu chipanichi komanso kusankha adindo atsopano a chipanichi.

Kwakhala kukumveka mphekesela yoti a Kaliwo amema anthu ndipo ali ndi kuthekela kochotsa pa udindo wa mtsogoleri wa chipani a Lazarus Chakwera.

Koma a Chakwera tsopano athamangila ku Khoti kukapempha kuti a Khoti aletse Bambo Kaliwo kuitanitsa msonkhanowo.

Padakali pano, a Khoti apeleka chiletso kwa Bambo Chakwera kulepheletsa msonkhanowu.

Share.

65 Comments

 1. Ngati malamulo aMCP akunena kuti convention should b held 1 yr b4 G.election nanga a Kaliwo izi sadziwa ngati Kaliwo akuphwanya malamulo achipani nde angazakwaniritse malamulo adziko?aaaaa pali akumtuma ameneyo bwanji osafunsa nzeru kwa a veteran aTEMBO?

 2. zimayamba choncho mu MCP we need not any other sign! shame on U !…….advice to Chakwera…..open yo eyes and see things r fallen apart!

 3. That is a clear sign of weakeness. I dont know about their constitution but Mr Lazarous could have humbled himself and prove things wrong.

  • Achimwene dzizimvetsani zinthuzi sangapange zinthu chifukwa choti ena afuna kukwaniritsa zofuna zawo. Nthawi ikwana convention yovomerezeka ipangika. Iyi inali yotumidwa ndiena omwe sagona tulo ndi mighty MCP cause they really know oneday its mcp.Ndie mukamafoira kuti mcp akukangana amafuna anthu ngati inu muziona choncho momwe muoneramu ndi mitu yanu yosankhwimayo.koma ife timazimanya kuti mmm awa asewera yoduka. dere nchifukwa chake anzawoo awatembenuzira mbali ina.

 4. Excellent And Next Achotsedwe Mchipani Whoever Is Advancing For A Conuention. We Know Someone Is Behind Ith Nonsense. Agalu Ena Amasekerera Convention Kufuna Kuti Chakwera Agwe Mzayende Moyera Mwauponda. Chakwera Is Man Of The Moment Mwamva Kale Za A Afro. Munya.

 5. Kaliwo ayitanitsa bwanj I convention ngati iwo ndimtsogoleri wachipani cha Congress? He is only being used by the dpp to confuse Mcp followers

 6. A DPP musathe mau ai!Inunso kwanuko mukusunga bomba and pompano tikuonerani.Musamale posankha running mate!mwamva agalu inu!

 7. AMALAWI: ATATE NDI AMAI!! Ndithu ndikakhala chetee, kusuzumila dziko,boma ndi zipani za ndyale m’dziko lathu zikusonyezelatu kuti AMALAWI safuna chitukuko koma kunyozana! NYIMBO YATHU YA PFUKO LA MALAWI IKUMUPEMPHA MULUNGU KUTI AGONJETSE ADANI ATHU ATATU: (a) NJALA (b) NTHENDA (d) NSANJE!! Komatu ndi m’mene zilili pano m’dziko lathu n’theladi talephela kuchotsa nsanje,nkhwizi, kaduka pakati pathu, ndi chifukwa chake dziko silikutukuka! Zifukwa zili mu MCP zingathe bwino pokambilana pachiweni-weni m’nyumba yomata! Koma taonani tsono zikuchitikazi, anthu atsatila yani? Anthuni monga ndidanena kuti,” NYUMBA YA NG’ALU SIILIMBA!! Chonde chotsani mtima wa NSANJE, ndipo mukhale amodzi n’cholinga chotukula dziko lathu. Ndikati chetee kuisuzumila DPP, siinabise mau, inanenelatu kuti ku MPOTO kaya kungapezeke wa nzelu, akumwela sangamuvotele, KODI TIKATELO CHITUKUKO CHILIPO? TICHOTSE MTIMA WA NSANJE UWU, N’CHOLINGA TITUKULE DZIKO LATHU: INE NDIKUMVA CHISONI PAZONSEZI ZIKUCHITIKA M’DZIKO LATHU CHIFUKWA CHA NSANJE!!!

 8. Kkkkkk Akuopa Chani Chakwera, Wazieza Pasikelo Waziona Kuti Sakukwanila, Akaliwo Musabwelele Mmbuyo Msonkhano Uchitike Akachosedwe Pampando Mtsogoleli Wopeleka Mimbayu Kkkkkk

 9. Chipanichi chimalakalaka chitawina koma mmm anthu ake akutsogolo amangodziwa kulongolola ndale sazidziwa. aliese wotsutsana nawo amat achoke mchipani. ndale za zotelez zidapta nd kamuzu muja ankachotsa ma founders a mcp. chakwera too much ma temper, chot adziwe izi nd ndale zimafuna anthu kut chipan chiwine. mtsogoleri wa andale amakhala pa chiopsezo nd achipan chomwecho komaso zpani zina but learn to be accommodative and follow open door policy.

 10. Inu adpp mwakhaula mumaona ngati zofuna zanu zikwaniritsidwa. ngati muvutika ndi ana aprimary mungathane ndi MCP, mwachepa ana inu. Mukhalira kupha anthu chonhi.

%d bloggers like this: