Aphungu aonjezeledwa malipiro

Lazarus Chakwera

Pamene sukulu ya ukachenjede ya Chancellor idakali chitsekele ndipo aphunzitsi a ku Primary anyanyala ntchito pa nkhani yokhudza ndalama, zaululika kuti a phungu a ku nyumba ya malamulo akhala akumwemwetela mwezi ukamatha.

Malawi Parliament chakwera
Afuna kuonjezeredwa malipiro

Malinga ndi malipoti, ndalama za pa mwezi za aphungu zikuyenela kukwela kuchoka pa ndalama yoposa K1 miliyoni ya pano.

Malipoti ati dongosolo loti aphungu achite mphumi ndi chuma cha boma alongosoledwa kale ndipo angodikila a President kuti achitepo kanthu.

“Tikudikila a President basi, akangovomela ndiye kuti zathu zayela,” anatelo olemekezeka Mayi Lilian Patel.

Iwo anaopsezanso kuti nkhani imeneyi ikuyenela kuyenda changu chifukwa akachedwa, aphungu atha kuzasokoneza dongosolo la budget.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.