Chenjelani anthu a danzi: ku Mazambiki ayamba kupha anthu a danzi

bal

Zoopsa kwambiri. Kaya atsale ndi ndani pa dziko pano?

Kutavuta nkhani yonyansa yopha anthu a chi alubino, zamveka kuti ku Mazambiki zigawenga tsopano zayamba kuchita chiwembu anthu okhala ndi danzi.

balMalinga ndi malipoti a atolankhani, Apolisi mu dziko la Mazambiki achenjeza anthu a danzi kuti aziyenda mosamala ati kamba zigawenga zopanda uzimu ndi umunthu zikuchita chiwembu anthu okhala ndi danzi.

Ati mwezi watha omwewu, abambo awiri a danzi anapezeka ataphedwa ndipo mmodzi anadulidwa mutu. Onse anadulidwa ziwalo.

Apolisi ati anagwila anthu awiri amene anaulula kuti anthu amene ali ndi danzi akusakidwa kuti ziwalo zawo agulitse kwa a malonda ena ku Mazambiki komweko ndinso ku Malawi ndi ku Tanzania.

Apolisi ku Mazambiki anena kuti pali zikhulupililo zoti anthu a danzi ali ndi chuma ndipo ena ati amayesa mu mutu wa danzi muli golide.

Advertisement

2 Comments

  1. Zoipa izi. Kwa munthu amene akufuna kuti dadzi lake limere tsitsi tiimbireni pa nambala izi : 0884390356/0997360260. Tili ku Matawale, Zomba~MALAWI. Pa milungu iwiri (2weeks) tsitsi kumera. “HAREHERBS Consultancy,”. Mphwayi nditsoka, fulmizani.

  2. Kkkkkkkkkkkk ndasiya kumeta buda…….koma kwa khwithima …kenako onse a mimba zazikulu…….kenako one a mbina ngati a dendekera msuko wa mowa

Comments are closed.