Abanduka dzulo kulisiya dziko liri pamoto.
Pamene aphunzitsi a ku Primary komanso ena a ku Secondary anyanyala ntchito, mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika lino wathawanso kumapita kunja.
A Mutharika anyamuka ku Malawi dzulo masana ati kupita ku Brussels, mu dziko la Belgium.
Akuti akachoka kumeneko, a Mutharika apita ku London mu dziko la England kumene akayankhule kwa ophunzila a pa sukulu ya ukachenjede ya Oxford.
Ati ku sukulu ya Oxford a Mutharika akayankhula pa nkhani yokhudza maphunziro. Izi zili chonchi ngakhale iwo boma lawo likukanika kupeleka maphunziro.
Ulendo wa a Mutharika wakwiyitsa a Malawi angapo amene aona kuti iwo angoononga ndalama.
“Nthawi zonse mkulu ameneyi akamachoka, amatinamiza kuti akapindulila dziko koma phindu lake sitiliona mpaka pano,” anatelo a Ntata.