Bodza: Manoma sanaphule K24 miliyoni mu Top 8

Be Forward Wanderers vs Silver Strikers

…Bullets sinangopeza K75,000 yokha

Malawi24 yapeza kuti ndi bodza la nkhunkhuniza limene a Malawi ena akulengeza lonena kuti zitagawidwa ndalama za chikho cha Airtel Top 8, timu ya Wanderers yatolera ndalama zokwana K24 miliyoni.

Malinga ndi zimene anthu ena akufalitsa, ati atagawana ndalama za mpira wa chigawo chomaliza cha chikho chimenechi, ati matimu a Silver ndi Manoma anagawana K14 miliyoni aliyense.

Be Forward Wanderers vs Silver Strikers
Masewera pakati pa Noma ndi Silver adapeza K52 Million.

Koma kafukufuku wa Malawi24 wapeza kuti utatha mpira wa loweruka, matimu awiriwa anapezapo K10 miliyoni aliyense.

Malawi24 yaona chikalata cha kagawidwe ka ndalamazi ndipo yapeza kuti palibe timu imene inalandila K14 miliyoni monga akukambila anthu.

Ndipo mosiyananso ndi zimene zikukambidwa kuti nyerere zinalandila K10 miliyoni pokhala achiwiri mu mpikisanowu, Malawi24 yapeza kuti Manoma analandila K5 miliyoni yokha.

Kuphatikiza, iwo atolela ndalama yokwana K15 miliyoni osati K24 miliyoni monga anthu akunenela.

Malawi24 yapezanso kuti nkhani yoti a Bullets analandila K75,000 yokha basi ndi yabodza.

Advertisement

3 Comments

  1. Ine masamu anga 10.5m + 5m + za game ya moyale + magame awiri a tigers = >24m. Noma ndi more.. wina alira chaka chino. Chimutu!

Comments are closed.