Nyerere zaona mbwadza zitalephera kukodzela golo

1

Sadyeka wadyeka ndi mafupa omwe ndipo aja amati chikho chilichonse chikamayamba ndi chawo tsopano akuyenda ali zyolizyoli.

Timu ya mpira wa miyendo ya Be Forward Wanderers dzulo yalila mokweza itakong’onthedwa ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Airtel Top 8.

Masewelowa anachitikila mu mzinda wa Lilongwe pa bwalo la Bingu International.

Nyerere zinapita ku masewelo amenewa zikudzimva kukoma ati chifukwa mbili inali mbali yawo.

Manoma akhala akutenga zikho zonse zongoyamba kumene ndipo amayesa adutsa moyela ndi Silver.

Koma dzulo Silver inalumitsa Mano pansi ndi kusalola kuti nyerere zikokele makobili kuuna.

Anyamata a nyerere amene akhala akudalilidwa monga Yamikani Chester ndi Khumbo N’gambi dzulo asewela osaona ukonde.

Nawo anyamata a Silver anavutikanso kuti abooleze.

Atasewela kwa mphindi zonse zokwanila popanda kumwetsa, mpira unafika ku ma penate kumene anyamata a Silver amwetsa tiyi wa ndulu yang’ona kwa nyerere.

Pamene anyamata a Silver anamwetsa ma penate awo khumi, nyerere zinaphonya penate yawo yomaliza imene anamenya Harry Nyirenda.

Basi, olire olire sanamvekenso pakati pa nyerere. Ka mbiri kotenga zikho zoyamba kumene kaja kanaimila pompo.

Kugonja kwa nyerere kwapangitsa ena a chipongwe kuti anene kuti nyerere zimapambana zikakodzela pagolo. Poti dzulo kunalibe mkodzo, nyerere zathela mu ma una a ku bank zikufuna Kuba ndalama.

Share.

One Comment

  1. Kkkkkkkk azimwetsa acid! Zimafunika choncho tisamachite poloweza kuti ichi itenge ndi iyo. Nawo a Silver ali ndi vuyo ndi lochinya muligi akunthidwa