Mwana wa zaka 4 amwalira atagwililidwa

2

Zina ukamva, kuchititsa nthumanzi ndi zina kuchititsa thupi kuuma kumene.

Pamene a boma ndi mabungwe akuyesetsa kufuna kuteteza amayi ndi ana, Bambo wina wa zaka 21 wapha ka mwana ka zaka 4 atakagwililila. Izi zachitika mu boma la Chiradzulu.

A Polisi mu bomalo atsekela Bambo Gift Eraton powaganizila kuti ndi mfiti imene inagwililila ka mwana ka zaka 4 mpaka kumupha.

Malinga ndi a Polisi, ati mwanayo adakumana ndi zoopsazo pamene amapita ku mjigo ndi mchemwali wake wazaka 7.

Apolisi ati gogo wa anayo anawatuma asungwana awiliwo kuti akatenge ndowa ku mjigo. Ati atsikanawa akubwelela, adakumana ndi Bambo Eraton amene anakokela patchire ka mwana ka zaka 4’ko.

Iwo pamenepo anamuchita chipongwe ndi kumusiya ali chikomokele.

Mchemwali wake wa mwanayu anali atapita kumudzi kukamemeza anthu pamene a Eraton anali kuchita u chigawenga wawowo.

Anthu atabwela, anapeza a Eraton athawa koma mwanayo adakali okomoka. Adathamangila naye ku chipatala kumene anawauza kuti afika naye atatsamila dzanja.

Apolisi adafufuza a Eraton ndipo anawamanga ndipo tsopano akudikila kupita ku Khoti.

Share.

2 Comments

  1. why Malawi???? that 1 he suppose to meet with a hard punishment…. wat kind of a nonsense z that??mahule osewa mmakwalalamu wat a stupid mankind z this???