Kongelesi ipambana chisankho cha 2019 – atelo a kafukufuku

Advertisement
Lazarous Chakwera

Utsogoleri wa a Mutharika ndi chipani chawo cholamula cha DPP utha osadutsa 2019.

Lazarous Chakwera
Kongelesi ipambana chisankho cha 2019

Malingana ndi bungwe lina la kafukufuku limene m’mbuyomu linanena molondola kuti a Peter Mutharika apambana zisankho za 2014, la Afrobarometer, zisankho zitati zichitike lero, a Kongelesi akubwelela m’boma.

Kafukufuku wa bungweli anapeza kuti a Malawi ochuluka akhumudwa ndi utsogoleri wa a Peter Mutharika ndipo mmalo mwake akufuna Kongelesi basi.

Pa a Malawi handilede alionse amene anafunsidwa, a Malawi okwana 32 ananena kuti iwo atha kuvotela Kongelesi atati tivote lero.

A Malawi 27 pa handilede anakakamila chipani cha DPP kuti ndicho angasankhe atapemphedwa kuvota lero.

Chipani cha UDF chinanenedwa ndi anthu 11 pa handilede alionse kuti angakachivotele.

Anatsogolela kafukufuku uyu ndi aphunzitsi a sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ku Zomba.

Advertisement