Mayi Joyce Banda atsimikiza zobwelera kumudzi

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino Mayi Joyce Banda atsimizikiIra mtundu wa a Malawi kuti abwelera kuno kumudzi chaka chino.

Mayi Banda amalankhula izi pa wailesi ya Zodiak Broadcasting Station mu nthawi ya pulogalamu ya “Tiuzeni Zoona.”

Joyce Banda
Banda akhala akubwerela kumudzi kuno chaka chino.

Malingana ndi a Banda, iwo akhala ali m’dziko muno chaka chino chisanathe koma alephera kunena tsiku leni leni lomwe adzaponde nthaka ya dziko lino.

“Ndibwelera kumudziko ndikamaliza ntchito zanga kunja kuno. Sindinganene tsiku limene ndidzabwelere koma izi amene adzalengeze ndi achipani changa cha People’s Party (PP),” mayi Banda atero.

Mtsogoleri wa dziko lino wakaleyu adachoka m’dziko muno mu chaka cha 2014 atalephera kutengaso udindo wa pulezidenti pa masankho apatatu pomwe adaimila chipani cha People’s.

Mu Febuwale chaka chino mphekesela zidali posepose pa makina a intaneti kufalitsa kuti Mayi Banda abwelera kuno kumudzi mwezi umenewo koma mneneri wawo a Andekuche Chanthunya adatsutsa izi.

Advertisement

5 Comments

  1. mudzatani??????????????????????????????????????????????????????????????????????????????????

Comments are closed.